< 창세기 33 >
1 야곱이 눈을 들어 보니 에서가 사백인을 거느리고 오는지라 그 자식들을 나누어 레아와 라헬과 두 여종에게 맡기고
Yakobo atakweza maso ake anaona Esau akubwera ndi anthu ake 400. Choncho ana ake anawagawira Leya, Rakele ndi antchito awiri aja.
2 여종과 그 자식들은 앞에 두고 레아와 그 자식들은 다음에 두고 라헬과 요셉은 뒤에 두고
Anayika antchito ndi ana awo patsogolo, kenaka nʼkubwera Leya ndi ana ake, ndipo pambuyo pawo Rakele ndi Yosefe.
3 자기는 그들 앞에서 나아가되 몸을 일곱번 땅에 굽히며 그 형 에서에게 가까이 하니
Iye mwini anakhala patsogolo nawerama mpaka kukhudza pansi kasanu ndi kawiri pamene amayandikira mʼbale wake.
4 에서가 달려와서 그를 맞아서 안고 목을 어긋맞기고 그와 입맞추고 피차 우니라
Koma Esau anathamanga kukakumana ndi Yakobo ndipo anamukupatira namupsompsona. Onse awiri ankangolira.
5 에서가 눈을 들어 여인과 자식들을 보고 묻되 너와 함께한 이들은 누구냐 야곱이 가로되 하나님이 주의 종에게 은혜로 주신 자식이니이다
Kenaka Esau ataona amayi ndi ana awo anamufunsa Yakobo kuti, “Kodi anthu amene uli nawowa ndi a ndani?” Yakobo anayankha kuti, “Awa ndi ana amene Mulungu, mwa kukoma mtima kwake, wapereka kwa mtumiki wanune.”
6 때에 여종들이 그 자식으로 더불어 나아와 절하고
Tsono antchito aja anayandikira naweramitsa mitu pansi.
7 레아도 그 자식으로 더불어 나아와 절하고 그 후에 요셉이 라헬로 더불어 나아와 절하니
Kenaka, Leya ndi ana ake anabwera. Nawonso anaweramitsa mitu pansi. Potsiriza pa onse anabwera Yosefe ndi Rakele naweramitsanso mitu yawo pansi.
8 에서가 또 가로되 나의 만난 바 이 모든 떼는 무슨 까닭이냐 야곱이 가로되 내 주께 은혜를 입으려 함이니이다
Esau anafunsa kuti, “Kodi gulu la ziweto ndakumana nalo lija ndi layani?” Yakobo anayankha nati, “Mbuye wanga, gulu lija ndi lanu kuti mundikomere mtima.”
9 에서가 가로되 내 동생아 내게 있는 것이 족하니 네 소유는 네게두라
Koma Esau anati, “Mʼbale wanga, ine ndili nazo kale zambiri. Zinthu zakozi sunga.”
10 야곱이 가로되 그렇지 아니하니이다 형님께 은혜를 얻었사오면 청컨대 내 손에서 이 예물을 받으소서 내가 형님의 얼굴을 뵈온 즉 하나님의 얼굴을 본 것 같사오며 형님도 나를 기뻐하심이니이다
Yakobo anati, “Chonde musatero. Ngati mwandikomera mtima, landirani mphatso yangayi kuchokera kwa ine. Pakuti ndi mmene mwandirandira bwinomu, ine ndikamaona nkhope yanu ndikuchita ngati ndikuona nkhope ya Mulungu.
11 하나님이 내게 은혜를 베푸셨고 나의 소유도 족하오니 청컨대 내가 형님께 드리는 예물을 받으소서 하고 그에게 강권하매 받으니라
Chonde, landirani mphatso imene ndakutengeraniyi, popeza Mulungu wandikomera mtima kwambiri moti ndili ndi zonse zimene ndizifuna.” Ndipo popeza kuti Yakobo anamuwumiriza, Esau analandira.
12 에서가 가로되 우리가 떠나가자 내가 너의 앞잡이가 되리라
Ndipo Esau anati, “Tiyeni tizipita; nditsagana nanu.”
13 야곱이 그에게 이르되 내 주도 아시거니와 자식들은 유약하고 내게 있는 양떼와 소가 새끼를 데렸은즉 하루만 과히 몰면 모든 떼가 죽으리니
Koma Yakobo anati kwa iye, “Mbuye wanga, inu mudziwa kuti anawa ndi a nthete ndiponso ndiyenera kusamalira nkhosa ndi ngʼombe zimene zikuyamwitsa ana awo. Ngati ndizimenya kuti zifulumire, tsiku limodzi lokha nyamazo zidzafa.
14 청컨대 내 주는 종보다 앞서 가소서 나는 앞에 가는 짐승과 자식의 행보대로 천천히 인도하여 세일로 가서 내 주께 나아가리이다
Choncho, mbuye wanga lolani kuti mutsogole. Ine ndiziyenda pangʼonopangʼono pambuyo pa ziwetozi ndi anawa mpaka ndikafika ku Seiri.”
15 에서가 가로되 내가 내 종자 수인을 네게 머물리라 야곱이 가로되 어찌하여 그리하리이까 나로 내 주께 은혜를 얻게 하소서 하매
Esau anati, “Ndiye bwanji ndikusiyireko ena mwa anthu anga.” Koma Yakobo anati, “Koma muchitiranji zimenezi? Chachikulu nʼkuti mwandilandira bwino, mbuye wanga.”
Choncho tsiku limenelo Esau anayamba ulendo wobwerera ku Seiri.
17 야곱은 숙곳에 이르러 자기를 위하여 집을 짓고 짐승을 위하여 우릿간을 지은 고로 그 땅 이름을 숙곳이라 부르더라
Komabe Yakobo anapita ku Sukoti. Kumeneko anamanga nyumba yake ndi makola a ziweto zake. Nʼchifukwa chake malowa amatchedwa Sukoti.
18 야곱이 밧단아람에서부터 평안히 가나안 땅 세겜 성에 이르러 성앞에 그 장막을 치고
Mmene ankabwerera kuchokera ku Padanaramu, Yakobo anafika ku Salemu, mzinda wa Sekemu ku Kanaani. Anamanga msasa pamalopo moyangʼanana ndi mzindawo.
19 그 장막 친 밭을 세겜의 아비 하몰의 아들들의 손에서 은 일백개로 사고
Malo amenewo anagula kwa zidzukulu za Hamori, abambo a Sekemu ndi ndalama 100 zasiliva.
20 거기 단을 쌓고 그 이름을 엘엘로헤이스라엘이라 하였더라
Pamalopo anamanganso guwa lansembe, nalitcha Eli Elohe Israeli.