< 사무엘하 12 >
1 여호와께서 나단을 다윗에게 보내시니 와서 저에게 이르되 한 성에 두 사람이 있는데 하나는 부하고 하나는 가난하니
Tsono Yehova anatumiza Natani kwa Davide. Atafika kwa Davide anati, “Panali anthu awiri mʼmizinda ina, wina wolemera ndi wina wosauka.
Munthu wolemerayo anali ndi nkhosa ndi ngʼombe zambiri,
3 가난한 자는 아무 것도 없고 자기가 사서 기르는 작은 암양 새끼 하나뿐이라 그 암양 새끼는 저와 저의 자식과 함께 있어 자라며 저의 먹는 것을 먹으며 저의 잔에서 마시며 저의 품에 누우므로 저에게는 딸처럼 되었거늘
koma wosaukayo analibe chilichonse kupatula kankhosa kamodzi kakakazi kamene anakagula. Iye anakasunga ndipo kanakula naye pamodzi ndi ana ake. Kamadya chakudya chake, kamamwera chikho chake ndipo kamagona mʼmanja mwake. Kanali ngati mwana wamkazi kwa iyeyo.
4 어떤 행인이 그 부자에게 오매 부자가 자기의 양과 소를 아껴 자기에게 온 행인을 위하여 잡지 아니하고 가난한 사람의 양 새끼를 빼앗아다가 자기에게 온 사람을 위하여 잡았나이다
“Ndipo mlendo anafika kwa munthu wolemera uja, koma munthu wolemerayo sanafune kutenga imodzi mwa nkhosa kapena ngʼombe zake kuti akonzere chakudya mlendo amene anafika kwa iye. Mʼmalo mwake anatenga mwana wankhosa wamkazi wa munthu wosauka uja nakonzera chakudya mlendo uja amene anabwera kwa iye.”
5 다윗이 그 사람을 크게 노하여 나단에게 이르되 여호와의 사심을 가리켜 맹세하노니 이 일을 행한 사람은 마땅히 죽을 자라
Davide anapsa mtima kwambiri chifukwa cha munthuyo ndipo anati kwa Natani, “Pali Yehova, munthu amene anachita zimenezi ayenera kufa basi!
6 저가 불쌍히 여기지 않고 이 일을 행하였으니 그 양 새끼를 사 배나 갚아 주어야 하리라
Iye ayenera kulipira mwana wankhosa wamkaziyo kanayi, chifukwa anachita chinthu chimenechi ndipo analibe chifundo.”
7 나단이 다윗에게 이르되 당신이 그 사람이라 이스라엘의 하나님 여호와께서 이처럼 이르시기를 내가 너로 이스라엘 왕을 삼기 위하여 네게 기름을 붓고 너를 사울의 손에서 구원하고
Kenaka Natani anati kwa Davide, “Munthuyo ndinu! Yehova, Mulungu wa Israeli akuti, ‘Ine ndinakudzoza kukhala mfumu ya Israeli, ndipo ndinakupulumutsa mʼdzanja la Sauli.
8 네 주인의 집을 네게 주고 네 주인의 처들을 네 품에 두고 이스라엘과 유다 족속을 네게 맡겼느니라 만일 그것이 부족하였을 것 같으면 내가 네게 이것 저것을 더 주었으리라
Ndinakupatsanso banja la mbuye wako ndiponso akazi a mbuye wako mʼmanja mwako. Ine ndinakupatsanso banja la Israeli ndi Yuda. Ndipo ngati zinthu zonse izi zinali zochepa, Ine ndikanakupatsa zambiri.
9 그러한데 어찌하여 네가 여호와의 말씀을 업신여기고 나 보기에 악을 행하였느뇨 네가 칼로 헷 사람 우리아를 죽이되 암몬 자손의 칼로 죽이고 그 처를 빼앗아 네 처를 삼았도다
Nʼchifukwa chiyani unanyoza mawu a Yehova pochita chimene chili choyipa pamaso pake? Iwe unakantha Uriya Mhiti ndi lupanga ndipo unatenga mkazi wake kukhala wako. Uriyayo unamupha ndi lupanga la Aamoni.
10 이제 네가 나를 업신여기고 헷 사람 우리아의 처를 빼앗아 네 처를 삼았은즉 칼이 네 집에 영영히 떠나지 아니하리라 하셨고
Ndipo tsopano lupanga silidzachoka pa nyumba yako, chifukwa unandinyoza ine ndi kutenga mkazi wa Uriya Mhiti kukhala wako.’
11 여호와께서 또 이처럼 이르시기를 내가 네 집에 재화를 일으키고 내가 네 처들을 가져 네 눈 앞에서 다른 사람에게 주리니 그 사람이 네 처들로 더불어 백주에 동침하리라
“Yehova akuti, ‘Ine ndidzabweretsa tsoka pa iwe lochokera mʼbanja lako. Ndidzatenga akazi ako iwe ukuona ndi kuwapereka kwa wina amene ali pafupi nawe, ndipo iye adzagona ndi akazi ako masanasana Aisraeli onse akuona.
12 너는 은밀히 행하였으나 나는 이스라엘 무리 앞 백주에 이 일을 행하리라 하셨나이다
Iwe unachita zimenezi mwamseri koma Ine ndidzachita izi masanasana Aisraeli onse akuona.’”
13 다윗이 나단에게 이르되 내가 여호와께 죄를 범하였노라 하매 나단이 다윗에게 대답하되 여호와께서도 당신의 죄를 사하셨나니 당신이 죽지 아니하려니와
Kenaka Davide anati kwa Natani, “Ine ndachimwira Yehova.” Natani anayankha kuti, “Yehova wachotsa tchimo lanu. Simufa ayi.
14 이 일로 인하여 여호와의 원수로 크게 훼방할 거리를 얻게 하였으니 당신의 낳은 아이가 정녕 죽으리이다 하고
Komabe, popeza pochita zimenezi mwachititsa kuti adani a Yehova amunyoze, mwana amene akubalireniyo adzafa.”
15 나단이 자기 집으로 돌아가니라 우리아의 처가 다윗에게 낳은 아이를 여호와께서 치시매 심히 앓는지라
Natani atapita kwawo, Yehova anakantha mwana amene mkazi wa Uriya anabereka ndipo anayamba kudwala.
16 다윗이 그 아이를 위하여 하나님께 간구하되 금식하고 안에 들어가서 밤새도록 땅에 엎드렸으니
Davide anapempherera mwanayo kwa Mulungu. Iye anasala chakudya ndipo analowa mʼnyumba mwake nagona pansi usiku wonse.
17 그 집의 늙은 자들이 곁에 이르러 다윗을 일으키려 하되 왕이 듣지 아니하고 저희로 더불어 먹지도 아니하더라
Akuluakulu a banja lake anayima pambali pake kuti amudzutse, koma iye anakana, ndipo sanadye chakudya chilichonse pamodzi ndi iwo.
18 이레만에 그 아이가 죽으니라 그러나 다윗의 신복들이 아이의 죽은 것을 왕에게 고하기를 두려워하니 이는 저희가 말하기를 아이가 살았을 때에 우리가 말하여도 왕이 그 말을 듣지 아니하셨나니 어떻게 그 아이의 죽은 것을 고할 수 있으랴 왕이 훼상하시리로다
Mwana anamwalira pa tsiku lachisanu ndi chiwiri. Antchito a Davide anaopa kumuwuza kuti mwanayo wamwalira, popeza ankaganiza kuti, “Pamene mwanayu anali ndi moyo, ife tinayankhula Davide koma sanatimvere. Nanga tingamuwuze bwanji kuti mwana wamwalira? Mwina atha kudzipweteka.”
19 다윗이 그 신복들의 서로 수군거리는 것을 보고 그 아이가 죽은 줄을 깨닫고 그 신복들에게 묻되 아이가 죽었느냐 대답하되 죽었나이다
Davide anaona kuti antchito ake amanongʼonezana pakati pawo ndipo anazindikira kuti mwanayo wamwalira. Iye anafunsa kuti, “Kodi mwanayo wamwalira?” Iwo anayankha kuti, “Inde wamwalira.”
20 다윗이 땅에서 일어나 몸을 씻고 기름을 바르고 의복을 갈아 입고 여호와의 전에 들어가서 경배하고 궁으로 돌아와서 명하여 음식을 그 앞에 베풀게 하고 먹은지라
Ndipo Davide anayimirira. Anakasamba nadzola mafuta ndi kusintha zovala zake. Pambuyo pake anapita ku nyumba ya Yehova kukapembedza. Kenaka anapita ku nyumba kwake ndipo atapempha chakudya anamupatsa nadya.
21 신복들이 왕께 묻되 아이가 살았을 때에는 위하여 금식하고 우시더니 죽은 후에는 일어나서 잡수시니 어찜이니이까
Antchito ake anamufunsa kuti, “Chifukwa chiyani mukuchita zinthu motere? Pamene mwana anali ndi moyo, munkasala chakudya ndi kulira, koma tsopano pamene mwana wamwalira inu mukudzuka ndi kudya!”
22 가로되 아이가 살았을 때에 내가 금식하고 운 것은 혹시 여호와께서 나를 불쌍히 여기사 아이를 살려주실는지 누가 알까 생각함이어니와
Iye anayankha kuti, “Pamene mwana anali ndi moyo ine ndinkasala zakudya ndi kulira. Ine ndinkaganiza kuti, ‘Akudziwa ndani? Yehova atha kundikomera mtima kuti mwanayo akhale ndi moyo.’
23 시방은 죽었으니 어찌 금식하랴 내가 다시 돌아오게 할 수 있느냐 나는 저에게로 가려니와 저는 내게로 돌아오지 아니하리라
Koma tsopano wamwalira ndisaliranji chakudya? Kodi ndingathe kumubwezanso? Ine ndidzapita kumene kuli iyeko, koma iye sadzabwerera kwa ine.”
24 다윗이 그 처 밧세바를 위로하고 저에게 들어가 동침하였더니 저가 아들을 낳으매 그 이름을 솔로몬이라 하니라 여호와께서 그를 사랑하사
Ndipo Davide anatonthoza mkazi wake Batiseba, napita kwa iye ndi kugona naye. Iye anabereka mwana wamwamuna, ndipo anamutcha dzina lake Solomoni. Yehova ankamukonda iye.
25 선지자 나단을 보내사 그 이름을 여디디야라 하시니 이는 여호와께서 사랑하심을 인함이더라
Ndipo chifukwa chakuti Yehova ankamukonda iyeyo, Yehovayo anatumiza mawu kwa mneneri Natani kuti akamutchule Yedidiya.
26 요압이 암몬 자손의 왕성 랍바를 쳐서 취하게 되매
Pa nthawi imeneyi Yowabu anamenyana ndi Raba ku Amoni ndipo analanda nsanja yaufumu.
27 사자를 다윗에게 보내어 가로되 내가 랍바 곧 물들의 성을 쳐서 취하게 되었으니
Ndipo Yowabu anatumiza amithenga kwa Davide kukanena kuti, “Ine ndamenyana ndi Raba ndipo ndatenga zitsime zake za madzi.
28 이제 왕은 남은 군사를 모아 진치고 이 성을 쳐서 취하소서 내가 이 성을 취하면 이 성이 내 이름으로 일컬음을 받을까 두려워하나이다
Ndipo tsopano sonkhanitsani asilikali onse ndipo muzungulire mzindawo ndi kuwulanda.”
29 다윗이 모든 군사를 모아 랍바로 가서 쳐서 취하고
Kotero Davide anasonkhanitsa ankhondo onse ndipo anapita ku Raba kukawuthira nkhondo ndi kuwulanda.
30 그 왕의 머리에서 보석 있는 면류관을 취하니 그 중량이 한 금 달란트라 다윗이 머리에 쓰니라 다윗이 또 그 성에서 노략한 물건을 무수히 내어오고
Davide anachotsa chipewa chaufumu pamutu pa mfumu yawo ndipo Davide anavala chipewacho. Chipewacho chinkalemera makilogalamu asanu agolide, ndiponso chinali ndi miyala yokongola. Iye anatenga katundu wambiri kuchokera mu mzindawo,
31 그 가운데 백성들을 끌어내어 톱질과 써레질과 도끼질과 벽돌구이를 하게 하니라 암몬 자손의 모든 성을 이같이 하고 다윗과 모든 백성이 예루살렘으로 돌아오니라
ndipo anatulutsa anthu amene anali mʼmenemo, nawayika kuti azigwira ntchito ya macheka, yosula makasu ndi nkhwangwa, ndiponso yowomba njerwa. Davide anachita izi ndi mizinda yonse ya Aamoni. Kenaka iye pamodzi ndi gulu lake lonse lankhondo anabwerera ku Yerusalemu.