< 역대하 29 >

1 히스기야가 위에 나아갈 때에 나이 이십오 세라 예루살렘에서 이십구 년을 치리하니라 그 모친의 이름은 아비야라 스가랴의 딸이더라
Hezekiya anali wa zaka 25 pamene anakhala mfumu ndipo analamulira mu Yerusalemu kwa zaka 29. Dzina la amayi ake linali Abiya mwana wa Zekariya.
2 히스기야가 그 조상 다윗의 모든 행위와 같이 여호와 보시기에 정직히 행하여
Iye anachita zolungama pamaso pa Yehova, monga momwe anachitira Davide abambo ake.
3 원년 정월에 여호와의 전 문들을 열고 수리하고
Pa chaka choyamba cha ulamuliro wake, iye anatsekula zitseko za Nyumba ya Yehova ndipo anazikonza.
4 제사장들과 레위 사람들을 동편 광장에 모으고
Iye analowetsamo ansembe ndi Alevi ndipo anawasonkhanitsa ku bwalo lakummawa
5 저희에게 이르되 레위 사람들아 내 말을 들으라 이제 너희는 성결케 하고 또 너희 열조의 하나님 여호와의 전을 성결케 하여 그 더러운 것을 성소에서 없이하라
ndipo anati: “Mverani, inu Alevi! Dziyeretseni tsopano ndiponso muyeretse Nyumba ya Yehova Mulungu wa makolo anu. Muchotse zodetsa zonse ku malo opatulika.
6 우리 열조가 범죄하여 우리 하나님 여호와 보시기에 악을 행하여 하나님을 버리고 얼굴을 돌이켜 여호와의 성소를 등지고
Makolo athu anali osakhulupirika ndipo anachita zoyipa pa maso pa Yehova Mulungu wathu ndi kumusiya Yehovayo. Iwo anatembenuka ndi kusiya malo okhalako Yehova ndi kumufulatira.
7 또 낭실 문을 닫으며 등불을 끄고 성소에서 분향하지 아니하며 이스라엘 하나님께 번제를 드리지 아니한고로
Iwowo anatsekanso zitseko zapakhonde ndi kuzimitsa nyale. Sanafukize lubani kapena kupereka nsembe zopsereza ku malo opatulika a Mulungu wa Israeli.
8 여호와께서 유다와 예루살렘을 진노하시고 내어버리사 두려움과 놀람과 비웃음거리가 되게 하신 것을 너희가 목도하는 바라
Kotero, Yehova anakwiyira Yuda ndi Yerusalemu. Iye anawasandutsa chinthu chochititsa mantha, choopsa ndiponso chonyozedwa monga momwe mukuonera ndi maso anuwa lero lino.
9 이로 인하여 우리의 열조가 칼에 엎드러지며 우리의 자녀와 아내가 사로잡혔느니라
Ichi nʼchifukwa chake makolo athu anaperekedwa ku lupanga ndipo nʼchifukwa chake ana athu aamuna ndi aakazi ndi akazi athu ali ku ukapolo.
10 이제 이스라엘 하나님 여호와로 더불어 언약을 세워 그 맹렬한 노로 우리에게서 떠나게 할 마음이 내게 있노니
Tsono ine ndikuganiza zochita pangano ndi Yehova Mulungu wa Israeli, kuti mkwiyo wake woopsawu utichokere.
11 내 아들들아 이제는 게으르지 말라 여호와께서 이미 너희를 택하사 그 앞에 서서 수종들어 섬기며 분향하게 하셨느니라
Ana anga, musanyalanyaze tsopano, pakuti Yehova wakusankhani kuti muziyima pamaso pake ndi kumutumikira Iye, kugwira ntchito pamaso pake ndi kufukiza lubani.”
12 이에 레위 사람들이 일어나니 곧 그핫의 자손 중 아마새의 아들 마핫과 아사랴의 아들 요엘과 므라리의 자손 중 압디의 아들 기스와 여할렐렐의 아들 아사랴와 게르손 사람 중 심마의 아들 요아와 요아의 아들 에덴과
Ndipo Alevi awa anakonzeka kugwira ntchito: Kuchokera ku banja la Kohati, Mahati mwana wa Amasai ndi Yoweli mwana wa Azariya; kuchokera ku banja la Merari, Kisi mwana wa Abidi ndi Azariya mwana wa Yehaleleli; kuchokera ku banja la Geresoni, Yowa mwana wa Zima ndi Edeni mwana wa Yowa;
13 엘리사반의 자손 중 시므리와 여우엘과 아삽의 자손 중 스가랴와 맛다냐와
kuchokera kwa zidzukulu za Elizafani, Simiri ndi Yeiyeli; kuchokera kwa zidzukulu za Asafu, Zekariya ndi Mataniya;
14 헤만의 자손 중 여후엘과 시므이와 여두둔의 자손 중 스마야와 웃시엘이라
kuchokera kwa zidzukulu za Hemani, Yehieli ndi Simei; kuchokera kwa zidzukulu za Yedutuni, Semaya ndi Uzieli.
15 저희가 그 형제를 모아 성결케 하고 들어가서 왕이 여호와의 말씀대로 명한 것을 좇아 여호와의 전을 깨끗케 할새
Atasonkhanitsa abale awo ndi kudziyeretsa, iwo anapita kukayeretsa Nyumba ya Yehova, monga inalamulira mfumu, potsatira mawu a Yehova.
16 제사장들도 여호와의 전 안에 들어가서 깨끗케 하여 여호와의 전에 있는 모든 더러운 것을 끌어 내어 여호와의 전 뜰에 이르매 레위 사람들이 취하여 바깥 기드론 시내로 가져갔더라
Ansembe analowa ku malo opatulika a Yehova kukayeretsako. Anatulutsira ku bwalo la Nyumba ya Yehova chilichonse chodetsedwa chimene anachipeza mʼNyumba ya Yehova. Alevi anatenga zimenezo ndi kupita nazo ku chigwa cha Kidroni.
17 정월 초하루에 성결케하기를 시작하여 그 달 초팔일에 여호와의 낭실에 이르고 또 팔 일 동안 여호와의 전을 성결케 하여 정월 십육일에 이르러 마치고
Iwo anayamba mwambo woyeretsawu tsiku loyamba la mwezi woyamba ndipo pa tsiku lachisanu ndi chitatu la mweziwo anafika pa khonde la nyumba ya Yehova. Tsono anachita mwambo woyeretsa Nyumba ya Yehova ija masiku asanu ndi atatu, ndipo anamaliza pa tsiku la 16 mwezi woyamba.
18 안으로 들어가서 히스기야 왕을 보고 가로되 우리가 여호와의 온 전과 번제단과 그 모든 기구와 떡을 진설하는 상과 그 모든 기구를 깨끗케 하였고
Ndipo anapita kwa mfumu Hezekiya ndi kukafotokoza kuti, “Ife tayeretsa Nyumba ya Mulungu yonse, guwa lansembe zopsereza ndi ziwiya zake zonse, ndiponso tebulo limene timayikapo buledi wopatulika pamodzi ndi zinthu zake zonse.
19 또 아하스 왕이 위에 있어 범죄할 때에 버린 모든 기구도 우리가 정돈하고 성결케 하여 여호와의 단 앞에 두었나이다 하니라
Takonza ndi kuyeretsa zinthu zonse zimene mfumu Ahazi anazichotsa mwa kusakhulupirika kwake pamene anali mfumu. Taziyika kutsogolo kwa guwa la Yehova.”
20 히스기야 왕이 일찍이 일어나 성읍의 귀인들을 모아 여호와의 전에 올라가서
Mmamawa tsiku linalo, mfumu Hezekiya inasonkhanitsa pamodzi akuluakulu a mu mzindawo ndipo inapita ku Nyumba ya Yehova.
21 수송아지 일곱과 수양 일곱과 어린 양 일곱과 수염소 일곱을 끌어다가 나라와 성소와 유다를 위하여 속죄 제물을 삼고 아론의 자손 제사장들을 명하여 여호와의 단에 드리게 하니
Iwo anabweretsa ngʼombe zazimuna zisanu ndi ziwiri ndi nkhosa zazimuna zisanu ndi ziwiri, ana ankhosa aamuna asanu ndi awiri, mbuzi zazimuna zisanu ndi ziwiri monga nsembe zoperekedwa chifukwa cha tchimo la ufumu, la malo opatulika ndi Yuda. Tsono mfumu inalamula ansembe, zidzukulu za Aaroni, kuti apereke zimenezi pa guwa lansembe la Yehova.
22 이에 수소를 잡으매 제사장이 그 피를 받아 단에 뿌리고 또 수양을 잡으매 그 피를 단에 뿌리고 또 어린 양을 잡으매 그 피를 단에 뿌리고
Choncho anthuwo anapha ngʼombe zazimunazo ndipo ansembe anatenga magazi ake ndi kuwawaza pa guwa lansembe, kenaka anapha nkhosa zazimuna zija ndipo anawaza magazi ake pa guwa lansembe; anaphanso ana ankhosa aja ndipo anawaza magazi ake pa guwa lansembe.
23 이에 속죄 제물로 드릴 수염소를 왕과 회중의 앞으로 끌어 오매 저희가 그 위에 안수하고
Mbuzi zoperekedwa chifukwa cha tchimo zija zinabweretsedwa pamaso pa mfumu ndi anthu onse, ndipo anasanjika manja awo pa izo.
24 제사장이 잡아 그 피로 속죄제를 삼아 단에 드려 온 이스라엘을 위하여 속죄하니 이는 왕이 명하여 온 이스라엘을 위하여 번제와 속죄제를 드리게 하였음이더라
Kenaka ansembe anapha mbuzizo ndipo anapereka magazi ake pa guwa, kuti ukhale mwambo wofafanizira machimo a Aisraeli onse, pakuti mfumu inalamula kuti nsembe yopsereza ndi yopepesera machimo zichitike chifukwa cha Aisraeli onse.
25 왕이 레위 사람을 여호와의 전에 두어서 다윗과 왕의 선견자 갓과 선지자 나단의 명한대로 제금과 비파와 수금을 잡게 하니 이는 여호와께서 그 선지자들로 이렇게 명하셨음이라
Iye anayika Alevi mʼNyumba ya Yehova ali ndi ziwaya za malipenga, azeze ndi apangwe potsata lamulo la Davide, Gadi mlosi wa mfumu ndi mneneri Natani. Pakuti Yehova ndiye analamula zimenezi kudzera mwa aneneri.
26 레위 사람은 다윗의 악기를 잡고 제사장은 나팔을 잡고 서매
Kotero Alevi anayima okonzekera atanyamula zoyimbira za Davide ndiponso ansembe atanyamula malipenga awo.
27 히스기야가 명하여 번제를 단에 드릴새 번제 드리기를 시작하는 동시에 여호와의 시로 노래하고 나팔을 불며 이스라엘 왕 다윗의 악기를 울리고
Hezekiya analamulira kuti apereke nsembe zopsereza pa guwa. Pamene amayamba kupereka nsembezo, kuyimbira Yehova kunayambikanso, pamodzi ndi malipenga ndi zipangizo zoyimbira za Davide mfumu ya Israeli.
28 온 회중이 경배하며 노래하는 자들은 노래하고 나팔 부는 자들은 나팔을 불어 번제를 마치기까지 이르니라
Anthu onse anawerama pansi ndi kulambira, pamene oyimba amayimba ndi malipenga. Izi zonse zinapitirira mpaka pa mapeto pa nsembe zopsereza.
29 제사 드리기를 마치매 왕과 그 함께 있는 자가 다 엎드려 경배하니라
Zopereka zitatha, mfumu ndi wina aliyense amene anali naye anagwada pansi ndi kulambira.
30 히스기야 왕이 귀인들로 더불어 레위 사람을 명하여 다윗과 선견자 아삽의 시로 여호와를 찬송하게 하매 저희가 즐거움으로 찬송하고 몸을 굽혀 경배하니라
Mfumu Hezekiya ndi akuluakulu ake analamulira Alevi kuti atamande Yehova potsata mawu a Davide ndi mlosi Asafu. Kotero anayimba nyimbo zamatamando mokondwera ndipo anaweramitsa mitu yawo ndi kulambira.
31 이에 히스기야가 일러 가로되 너희가 이제 몸을 깨끗케하여 여호와께 드렸으니 마땅히 나아와 제물과 감사제물을 여호와의 전으로 가져오라 회중이 드디어 제물과 감사제물을 가져 오되 무릇 마음에 원하는 자는 또한 번제물을 가져오니
Kenaka Hezekiya anati, “Inu mwadzipereka tsopano kwa Yehova. Bwerani ndipo mufike ndi nsembe ndi zopereka zachiyamiko ku Nyumba ya Yehova.” Choncho anthu onse anabweretsa nsembe ndi zopereka zachiyamiko, ndipo anthu onse amene anali ofuna mu mtima mwawo anabweretsa nsembe zopsereza.
32 회중의 가져온 번제물의 수효는 수소가 칠십이요 수양이 일백이요 어린 양이 이백이니 이는 다 여호와께 번제물로 드리는 것이며
Chiwerengero cha nsembe zopsereza chimene anthu onse anabweretsa chinali ngʼombe zazimuna makumi asanu ndi awiri, nkhosa zazimuna 100, ana ankhosa aamuna 200 ndipo zonsezi zinali za nsembe yopsereza kwa Yehova.
33 또 구별하여 드린 소가 육백이요 양이 삼천이라
Ziweto zimene zinapatulidwa kukhala nsembe zinalipo ngʼombe zazimuna 600, nkhosa ndi mbuzi 3,000.
34 그런데 제사장이 부족하여 그 모든 번제 짐승의 가죽을 능히 벗기지 못하는고로 그 형제 레위 사람이 그 일을 마치기까지 돕고 다른 제사장의 성결케 하기까지 기다렸으니 이는 레위 사람의 성결케함이 제사장들보다 성심이 있었음이라
Koma ansembe anali ochepa kuti asende zonse zopsereza. Choncho abale awo Alevi anawathandiza mpaka ntchito yonse inatha ndipo mpaka ansembe ena atadziyeretsa, pakuti Alevi anachita changu kudziyeretsa kulekana ndi momwe anachitira ansembe.
35 번제와 화목제의 기름과 각 번제에 속한 전제가 많더라 이와 같이 여호와의 전에서 섬기는 일이 순서대로 갖추어지니라
Panali nsembe zopsereza zochuluka, pamodzi ndi mafuta a nsembe yachiyanjano ndi nsembe yachakumwa imene imachitika pamodzi ndi nsembe yopsereza. Kotero ntchito ya mʼNyumba ya Mulungu inakhazikitsidwanso.
36 이 일이 갑자기 되었을지라도 하나님이 백성을 위하여 예비하셨음을 인하여 히스기야가 백성으로 더불어 기뻐하였더라
Hezekiya ndi anthu onse anakondwera pa zimene Mulungu anachitira anthu ake, chifukwa zinachita mwamsangamsanga.

< 역대하 29 >