< 시편 8 >

1 (다윗의 시. 영장으로 깃딧에 맞춘 노래) 여호와 우리 주여, 주의 이름이 온 땅에 어찌 그리 아름다운지요 주의 영광을 하늘 위에 두셨나이다
Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Pa gititi. Salimo la Davide. Inu Yehova Ambuye athu, dzina lanu ndi la lamphamvudi pa dziko lonse lapansi! Inu mwakhazikitsa ulemerero wanu mʼmayiko onse akumwamba.
2 주의 대적을 인하여 어린 아이와 젖먹이의 입으로 말미암아 권능을 세우심이여 이는 원수와 보수자로 잠잠케 하려 하심이니이다
Kuchokera mʼkamwa mwa ana ndi makanda, Inu mwakhazikitsa mphamvu chifukwa cha adani anu, kukhazikitsa bata adani ndi anthu obwezera zoyipa.
3 주의 손가락으로 만드신 주의 하늘과 주의 베풀어 두신 달과 별들을 내가 보오니
Pamene ndilingalira za mayiko anu akumwamba, ntchito ya zala zanu, mwezi ndi nyenyezi, zimene mwaziyika pa malo ake,
4 사람이 무엇이관대 주께서 저를 권고하시나이까
munthu ndani kuti Inu mumamukumbukira, ndi mwana wa munthu kuti inu mumacheza naye?
5 저를 천사보다 조금 못하게 하시고 영화와 존귀로 관을 씌우셨나이다
Inu munamupanga kukhala wocheperapo kusiyana ndi zolengedwa zakumwamba ndipo mwamuveka ulemerero ndi ulemu.
6 주의 손으로 만드신 것을 다스리게 하시고 만물을 그 발 아래 두셨으니
Inu munamuyika wolamulira ntchito ya manja anu; munayika zinthu zonse pansi pa mapazi ake;
7 곧 모든 우양과 들짐승이며
nkhosa, mbuzi ndi ngʼombe pamodzi ndi nyama zakuthengo,
8 여호와 우리 주여, 주의 이름이 온 땅에 어찌 그리 아름다운지요
mbalame zamlengalenga ndi nsomba zamʼnyanja zonse zimene zimayenda pansi pa nyanja.
9
Inu Yehova, Ambuye athu, dzina lanu ndi lamphamvudi pa dziko lonse lapansi!

< 시편 8 >