< 시편 126 >
1 (성전에 올라가는 노래) 여호와께서 시온의 포로를 돌리실 때에 우리가 꿈꾸는 것 같았도다
Nyimbo yoyimba pokwera ku Yerusalemu. Yehova atabwezera akapolo ku Ziyoni, tinali ngati amene akulota.
2 그 때에 우리 입에는 웃음이 가득하고 우리 혀에는 찬양이 찼었도다 열방 중에서 말하기를 여호와께서 저희를 위하여 대사를 행하셨다 하였도다
Pakamwa pathu panadzaza ndi kuseka; malilime athu ndi nyimbo zachimwemwe. Pamenepo kunanenedwa pakati pa anthu kuti, “Yehova wawachitira zinthu zazikulu.”
3 여호와를 위하여 대사를 행하셨으니 우리는 기쁘도다
Yehova watichitira zinthu zazikulu, ndipo tadzazidwa ndi chimwemwe.
4 여호와여, 우리의 포로를 남방 시내들 같이 돌리소서
Tibwezereni madalitso athu, Inu Yehova, monga mitsinje ya ku Negevi.
5 눈물을 흘리며 씨를 뿌리는 자는 기쁨으로 거두리로다
Iwo amene amafesa akulira, adzakolola akuyimba nyimbo zachimwemwe.
6 울며 씨를 뿌리러 나가는 자는 정녕 기쁨으로 그 단을 가지고 돌아 오리로다
Iye amene amayendayenda nalira, atanyamula mbewu yokafesa, adzabwerera akuyimba nyimbo zachimwemwe, atanyamula mitolo yake.