< 민수기 29 >
1 칠월에 이르러는 그 달 초일일에 성회로 모이고 아무 노동도 하지 말라 이는 너희가 나팔을 불 날이니라
“‘Pa tsiku loyamba la mwezi wachisanu ndi chiwiri muzichita msonkhano wopatulika ndipo musamagwire ntchito iliyonse. Ili ndi tsiku limene muziliza malipenga.
2 너희는 수송아지 하나와 수양 하나와 일년 되고 흠 없는 수양 일곱을 여호와께 향기로운 번제로 드릴 것이며
Muzipereka mwana wangʼombe wamwamuna mmodzi, nkhosa yayimuna imodzi ndi ana ankhosa asanu ndi awiri a chaka chimodzi wopanda chilema monga nsembe zopsereza, fungo lokoma kwa Yehova.
3 그 소제로는 고운 가루에 기름을 섞어서 쓰되 수송아지에는 에바 십분지 삼이요, 수양에는 에바 십분지 이요
Pa ngʼombe yayimuna iliyonse, muzipereka chopereka cha chakudya cha makilogalamu atatu a ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta. Pa nkhosa yayimuna iliyonse muzipereka makilogalamu awiri.
4 어린 양 일곱에는 매 어린 양에 에바 십분지 일을 드릴 것이며
Pa mwana wankhosa aliyense mwa asanu ndi awiri aja muzipereka kilogalamu imodzi.
5 또 너희를 속하기 위하여 수염소 하나를 속죄제로 드리되
Muziperekanso mbuzi yayimuna kuti izikhala nsembe yopepesera machimo anu.
6 월삭의 번제와 그 소제와 상번제와 그 소제와 그 전제 외에 그 규례를 따라 향기로운 화제로 여호와께 드릴 것이니라
Izi ndi zowonjezera pa nsembe zopsereza za mwezi ndi mwezi komanso za tsiku ndi tsiku pamodzi ndi zopereka za chakudya ndi zopereka za chakumwa potsata malamulo ake. Izi ndi zopereka zotentha pa moto, zoperekedwa kwa Yehova, fungo lokoma.
7 칠월 십일에는 너희가 성회로 모일 것이요 마음을 괴롭게 하고 아무 노동도 하지 말 것이며
“‘Pa tsiku lakhumi la mwezi wachisanu ndi chiwiriwu, muzichita msonkhano wopatulika. Muzisala zakudya ndipo musamagwire ntchito.
8 너희는 수송아지 하나와 수양 하나와 일년 된 수양 일곱을 다 흠없는 것으로 여호와께 향기로운 번제를 드릴 것이며
Muzipereka kwa Yehova nsembe yopsereza, yotulutsa fungo lokoma lokondweretsa Yehovayo; ngʼombe yayimuna imodzi, nkhosa yayimuna imodzi ndi ana ankhosa asanu ndi awiri a chaka chimodzi. Zimenezi zizikhala zopanda chilema.
9 그 소제로는 고운 가루에 기름을 섞어서 쓰되 수송아지 하나에는 에바 십분지 삼이요, 수양 하나에는 에바 십분지 이요
Pa ngʼombe yayimuna iliyonse, muzikonza chopereka cha chakudya cha makilogalamu atatu a ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta; pa nkhosa yayimuna iliyonse makilogalamu awiri;
10 어린 양 일곱에는 매 어린 양에 에바 십분지 일을 드릴 것이며
kilogalamu imodzi pa mwana wankhosa aliyense mwa asanu ndi awiriwo.
11 또 수염소 하나를 속죄제로 드릴 것이니 이는 속죄제와 상번제와 그 소제와 그 전제 외에니라
Muziperekanso mbuzi imodzi yayimuna kuti izikhala nsembe yopepesera machimo, kuwonjezera pa nsembe yopepesera machimo ya pa tsiku la mwambo ija, kuwonjezanso pa nsembe zopsereza za tsiku ndi tsiku zija, pamodzi ndi chopereka chake cha chakudya ndi cha chakumwa.
12 칠월 십오일에는 너희가 너희 성회로 모일 것이요 아무 노동도 하지 말 것이며 칠일 동안 여호와 앞에 절기를 지킬 것이라
“‘Pa tsiku la mwezi wachisanu ndi chiwiri, muzichita msonkhano wopatulika ndipo musamagwire ntchito iliyonse. Muzichita madyerero a Yehova masiku asanu ndi awiri.
13 너희 번제로 여호와께 향기로운 화제를 드리되 수 송아지 열셋과 수양 둘과 일년된 수양 열 넷을 다 흠 없는 것으로 드릴 것이며
Muzipereka nsembe yotentha pa moto, kuti izikhala fungo lokoma kwa Yehova, nsembe yopsereza ya ana angʼombe aamuna khumi ndi atatu, nkhosa zazimuna ziwiri, ndi ana ankhosa aamuna khumi ndi anayi a chaka chimodzi, zonse zopanda chilema.
14 그 소제로는 고운 가루에 기름을 섞어서 수송아지 열셋에는 각기 에바 십분지 삼이요, 수양 둘에는 각기 에바 십분지 이요
Pa mwana wangʼombe aliyense mwa ana angʼombe aamuna khumi ndi atatu aja, muzikonza chopereka cha chakudya cha makilogalamu atatu a ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta. Pa nkhosa iliyonse mwa nkhosa ziwiri zija, mukonza chopereka cha chakudya cha makilogalamu awiri.
15 어린 양 열넷에는 각기 에바 십분지 일을 드릴 것이며
Pa mwana wankhosa aliyense mwa ana ankhosa aamuna khumi ndi anayiwo, muzipereka chakudya cha kilogalamu imodzi.
16 또 수염소 하나를 속죄제로 드릴지니 상번제와 그 소제와 그 전제 외에니라
Muziperekanso mbuzi yayimuna imodzi kuti izikhale nsembe yopepesera machimo, kuwonjezera pa nsembe zopsereza za tsiku ndi tsiku zija pamodzi ndi chopereka chake cha chakudya ndi chakumwa.
17 둘째 날에는 수송아지 열둘과 수양 둘과 일년 되고 흠 없는 수양 열넷을 드릴 것이며
“‘Pa tsiku lachiwiri muzipereka ana angʼombe aamuna khumi ndi awiri aja, nkhosa zazimuna ziwiri ndi ana ankhosa aamuna khumi ndi anayi a chaka chimodzi aja, zonse zopanda chilema.
18 그 소제와 전제는 수송아지와 수양과 어린 양의 수효를 따라서 규례대로 할 것이며
Pamodzi ndi ngʼombe zazimuna, nkhosa zazimuna ndi ana ankhosa, muzipereka zopereka za chakudya ndi za chakumwa molingana ndi chiwerengero cha nyamazo.
19 또 수염소 하나를 속죄제로 드릴지니 상번제와 그 소제와 그 전 제 외에니라
Muziperekanso mbuzi imodzi yayimuna ya nsembe yopepesera machimo powonjezera pa nsembe yopsereza ya tsiku ndi tsiku pamodzi ndi chopereka chake cha chakudya ndi chakumwa.
20 세째 날에는 수송아지 열 하나와 수양 둘과 일년 되고 흠없는 수양 열넷을 드릴 것이며
“‘Pa tsiku lachitatu muzipereka ngʼombe zazimuna khumi ndi imodzi, nkhosa zazimuna ziwiri ndi ana ankhosa aamuna khumi ndi anayi a chaka chimodzi, zonse zopanda chilema.
21 그 소제와 전제는 수송아지와 수양과 어린 양의 수효를 따라서 규례대로 할 것이며
Pamodzi ndi ngʼombe zazimuna, nkhosa zazimuna ndi ana ankhosa, muzipereka zopereka za chakudya ndi za chakumwa molingana ndi chiwerengero cha nyamazo.
22 또 수염소 하나를 속죄제로 드릴지니 상번제와 그 소제와 그 전제 외에니라
Muziperekanso mbuzi imodzi yayimuna ya nsembe yopepesera machimo, powonjezera pa nsembe yopsereza ya tsiku ndi tsiku pamodzi ndi chopereka chake cha chakudya ndi chakumwa.
23 네째 날에는 수송아지 열과 수양 둘과 일년 되고 흠 없는 수양 열넷을 드릴 것이며
“‘Pa tsiku lachinayi muzipereka ngʼombe zazimuna khumi, nkhosa zazimuna ziwiri ndi ana ankhosa aamuna khumi ndi anayi a chaka chimodzi, zonse zopanda chilema.
24 그 소제와 전제는 수송아지와 수양과 어린 양의 수효를 따라서 규례대로 할 것이며
Pamodzi ndi ngʼombe zazimuna, nkhosa zazimuna ndi ana ankhosa, muzipereka chopereka cha chakudya ndi chakumwa molingana ndi chiwerengero cha nyamazo.
25 또 수염소 하나를 속죄제로 드릴지니 상번제와 그 소제와 그 전제 외에니라
Muziperekanso mbuzi imodzi yayimuna ya nsembe yopepesera machimo, powonjezera pa nsembe yopsereza ya tsiku ndi tsiku pamodzi ndi chopereka chake cha chakudya ndi chakumwa.
26 다섯째 날에는 수송아지 아홉과 수양 둘과 일년 되고 흠없는 수양 열넷을 드릴 것이며
“‘Pa tsiku lachisanu muzipereka ngʼombe zazimuna zisanu ndi zinayi, nkhosa zazimuna ziwiri ndi ana ankhosa aamuna khumi ndi anayi a chaka chimodzi, zonse zopanda chilema.
27 그 소제와 전제는 수송아지와 수양과 어린 양의 수효를 따라서 규례대로 할 것이며
Pamodzi ndi ngʼombe zazimuna, nkhosa zazimuna ndi ana ankhosa, muzipereka chopereka cha chakudya ndi chakumwa molingana ndi chiwerengero cha nyamazo.
28 또 수염소 하나를 속죄제로 드릴지니 상번제와 그 소제와 그 전제 외에니라
Muziperekanso mbuzi imodzi yayimuna ya nsembe yopepesera machimo, powonjezera pa nsembe yopsereza ya tsiku ndi tsiku ndi chopereka chake cha chakudya ndi chakumwa.
29 여섯째 날에는 수송아지 여덟과 수양 둘과 일년 되고 흠없는 수양 열넷을 드릴 것이며
“‘Pa tsiku lachisanu ndi chimodzi muzipereka ngʼombe zazimuna zisanu ndi zitatu, nkhosa zazimuna ziwiri ndi ana ankhosa aamuna khumi ndi anayi a chaka chimodzi, zonse zopanda chilema.
30 그 소제와 전제는 수송아지와 수양과 어린 양의 수효를 따라서 규례대로 할 것이며
Pamodzi ndi ngʼombe zazimuna, nkhosa zazimuna ndi ana ankhosa, muzipereka chopereka cha chakudya ndi cha chakumwa molingana ndi chiwerengero cha nyamazo.
31 또 수염소 하나를 속죄제로 드릴지니 상번제와 그 소제와 그 전제 외에니라
Muziperekenso mbuzi imodzi yayimuna ya nsembe yopepesera machimo, powonjezera pa nsembe yopsereza ya tsiku ndi tsiku pamodzi ndi chopereka chake cha chakudya ndi chakumwa.
32 일곱째 날에는 수송아지 일곱과 수양 둘과 일년 되고 흠 없는 수양 열넷을 드릴 것이며
“‘Pa tsiku lachisanu ndi chiwiri muzipereka ngʼombe zazimuna zisanu ndi ziwiri, nkhosa zazimuna ziwiri ndi ana ankhosa amuna khumi ndi anayi a chaka chimodzi, zonse zopanda chilema.
33 그 소제와 전제는 수송아지와 수양과 어린 양의 수효를 따라서 규례대로 할 것이며
Pamodzi ndi ngʼombe zazimuna, nkhosa zazimuna ndi ana ankhosa, muzipereka chopereka cha chakudya ndi chakumwa molingana ndi chiwerengero cha nyamazo.
34 또 수염소 하나를 속죄제로 드릴지니 상번제와 그 소제와 그 전제 외에니라
Muziperekanso mbuzi imodzi yayimuna ya nsembe yopepesera machimo, powonjezera pa nsembe yopsereza ya tsiku ndi tsiku pamodzi ndi chopereka chake cha chakudya ndi chakumwa.
35 여덟째 날에는 거룩한 대회로 모일 것이요 아무 노동도 하지 말것이며
“‘Pa tsiku lachisanu ndi chitatu muzichita msonkhano ndipo musamagwire ntchito iliyonse.
36 번제로 여호와께 향기로운 화제를 드리되 수송아지 하나와 수양 하나와 일년 되고 흠 없는 수양 일곱을 드릴 것이며
Muzipereka chopereka chotentha pa moto monga fungo lokoma kwa Yehova, nsembe yopsereza ya ngʼombe imodzi yayimuna, nkhosa yayimuna imodzi ndi ana ankhosa amuna asanu ndi awiri a chaka chimodzi, zonse zopanda chilema.
37 그 소제와 전제는 수송아지와 수양과 어린 양의 수효를 따라서 규례대로 할 것이며
Pamodzi ndi ngʼombe yayimunayo, nkhosa yayimunayo ndi ana ankhosawo, muzipereka chopereka cha chakudya ndi chakumwa molingana ndi chiwerengero cha nyamazo.
38 또 수염소 하나를 속죄제로 드릴지니 상번제와 그 소제와 그 전제 외에니라
Muziperekanso mbuzi imodzi yayimuna ya nsembe yopepesera machimo, powonjezera pa nsembe yopsereza ya tsiku ndi tsiku pamodzi ndi chopereka chake cha chakudya ndi chakumwa.
39 너희가 이 절기를 당하거든 여호와께 이같이 드릴지니 이는 너희 서원제나 낙헌제외에 번제, 소제, 전제, 화목제를 드릴 것이니라
“‘Kuwonjezera pa zopereka zimene munalumbirira ndi pa zopereka zanu zaufulu, muzipereka zimenezi kwa Yehova pa masiku osankhika a chikondwerero chanu. Nsembe zanu zachakumwa ndi nsembe zanu zachiyanjano.’”
40 모세가 여호와께서 자기로 명하신 모든 일을 이스라엘 자손에게 고하니라
Mose anawuza Aisraeli zonse zimene Yehova anamulamulira.