< 여호수아 24 >

1 여호수아가 이스라엘 모든 지파를 세겜에 모으고 이스라엘 장로들과 그 두령들과 재판장들과 유사들을 부르매 그들이 하나님 앞에 보인지라
Tsono Yoswa anasonkhanitsa mafuko onse a Israeli ku Sekemu. Iye anayitanitsa akuluakulu, atsogoleri, oweruza, ndi akuluakulu a boma la Israeli, ndipo iwo anafika pamaso pa Mulungu.
2 여호수아가 모든 백성에게 이르되 `이스라엘 하나님 여호와의 말씀에 옛적에 너희 조상들 곧 아브라함의 아비, 나홀의 아비 데라가 강 저편에 거하여 다른 신들을 섬겼으나
Yoswa anati kwa anthu onse, “Yehova Mulungu wa Israeli akuti, ‘Kalekale makolo anu, kuphatikiza Tera, abambo a Abrahamu ndi Nahori ankakhala kutsidya kwa Mtsinje ndipo ankapembedza milungu ina.
3 내가 너희 조상 아브라함을 강 저편에서 이끌어내어 가나안으로 인도하여 온 땅을 두루 행하게 하고 그 씨를 번성케 하려고 그에게 이삭을 주었고
Koma ine ndinatenga kholo lanu Abrahamu kumuchotsa ku dziko la kutsidya kwa mtsinje wa Yufurate ndipo ndinamutsogolera kupita ku dziko la Kanaani. Ndinamupatsa zidzukulu zambiri. Ndinamupatsa Isake,
4 이삭에게는 야곱과 에서를 주었으며 에서에게는 세일산을 소유로 주었으나 야곱과 그 자손들은 애굽으로 내려갔으므로
ndipo Isake ndinamupatsa Yakobo ndi Esau. Ndinapereka dziko la mapiri la Seiri kwa Esau, koma Yakobo ndi ana ake anapita ku Igupto.
5 내가 모세와 아론을 보내었고 또 애굽에 재앙을 내렸나니 곧 내가 그 가운데 행한 것과 같고 그 후에 너희를 인도하여 내었었노라
“‘Kenaka ndinatuma Mose ndi Aaroni, ndipo ine ndinazunza Aigupto. Pambuyo pake ndinakutulutsani.
6 내가 너희 열조를 애굽에서 인도하여 내어 바다에 이르게 한즉 애굽 사람이 병거와 마병을 거느리고 너희 열조를 홍해까지 따르므로
Nditatulutsa makolo anu ku Igupto ndinafika nawo ku Nyanja Yofiira. Aigupto anawathamangira ndi magaleta ndi okwera pa akavalo mpaka ku Nyanja Yofiira.
7 너희 열조가 나 여호와께 부르짖기로 내가 너희와 애굽 사람 사이에 흑암을 두고 바다를 이끌어 그들을 덮었었나니 내가 애굽에서 행한 일을 너희가 목도하였으며 또 너희가 여러 날을 광야에 거하였었느니라
Tsono makolo anuwo anapemphera kwa Ine kuti ndiwathandize, ndipo ndinayika mtambo wakuda pakati pawo ndi Aiguptowo, ndipo Nyanja inamiza Aigupto aja. Inu munaona ndi maso anu zimene ndinachita kwa Aiguptowo ndipo inu munakhala mʼchipululu nthawi yayitali.
8 내가 또 너희를 인도하여 요단 저편에 거하는 아모리 사람의 땅으로 들어가게 하매 그들이 너희와 싸우기로 내가 그들을 너희 손에 붙이매 너희가 그 땅을 점령하였고 나는 그들을 너희 앞에서 멸절시켰으며
“‘Pambuyo pake Ine ndinabwera nanu ku dziko la Aamori amene amakhala kummawa kwa Yorodani. Iwo anamenyana nanu koma ndinawapereka mʼdzanja lanu. Ndinawawononga pamaso panu, ndipo inu munalanda dziko lawo.
9 때에 모압 왕 십볼의 아들 발락이 일어나 이스라엘을 대적하여 사람을 보내어 브올의 아들 발람을 불러다가 너희를 저주케 하려 하였으나
Balaki mwana wa Zipori, mfumu ya Mowabu, analimbana ndi Israeli. Iye anayitanitsa Balaamu mwana wa Beori kuti akutemberereni.
10 내가 발람을 듣기를 원치 아니한 고로 그가 오히려 너희에게 축복하였고 나는 너희를 그 손에서 건져 내었으며
Koma ine sindinamvere Balaamu, kotero iye anakudalitsani mowirikiza ndipo ndinakulanditsani mʼdzanja lake.
11 너희가 요단을 건너 여리고에 이른즉 여리고 사람과, 아모리 사람과, 브리스 사람과, 가나안 사람과, 헷 사람과, 기르가스 사람과, 히위 사람과, 여부스 사람들이 너희와 싸우기로 내가 그들을 너희의 손에 붙였으며
“‘Ndipo inu munawoloka Yorodani ndi kufika ku Yeriko. Anthu a ku Yeriko analimbana nanu pamodzi ndi Aamori, Aperezi, Akanaani, Ahiti, Agirigasi, Ahivi ndi Ayebusi. Koma Ine ndinawapereka mʼdzanja lanu.
12 내가 왕벌을 너희 앞에 보내어 그 아모리 사람의 두 왕을 너희 앞에서 쫓아내게 하였나니 너희 칼로나 너희 활로나 이같이 한 것이 아니며
Ine ndinatumiza mavu amene anapirikitsa mafumu awiri Aamori aja pamaso panu. Inu simunachite izi ndi lupanga ndi uta wanu.
13 내가 또 너희의 수고하지 아니한 땅과 너희가 건축지 아니한 성읍을 너희에게 주었더니 너희가 그 가운데 거하며 너희가 또 자기의 심지 아니한 포도원과 감람원의 과실을 먹는다 하셨느니라
Motero ndinakupatsani dziko limene simunalivutikire ndiponso mizinda imene simunamange. Inu mukukhala mʼmenemo ndi kumadya zipatso za mʼmunda wamphesa ndi kuthyola zipatso mʼmitengo ya olivi zimene simunadzale.’
14 그러므로 이제는 여호와를 경외하며 성실과 진정으로 그를 섬길 것이라 너희의 열조가 강 저편과 애굽에서 섬기던 신들을 제하여 버리고 여호와만 섬기라!
“Ndipo tsopano wopani Yehova ndi kumutumikira Iye mokhulupirika ndi moona. Chotsani milungu imene makolo anu ankapembedza kutsidya kwa mtsinje wa Yufurate ndi ku Igupto ndipo tumikirani Yehova.
15 만일 여호와를 섬기는 것이 너희에게 좋지 않게 보이거든 너희 열조가 강 저편에서 섬기던 신이든지 혹 너희의 거하는 땅 아모리 사람의 신이든지 너희 섬길 자를 오늘날 택하라! 오직 나와 내 집은 여호와를 섬기겠노라!'
Koma ngati kutumikira Yehova kukuyipirani, sankhani lero amene mudzamutumikire, kapena milungu imene makolo anu ankayitumikira kutsidya kwa mtsinje wa Yufurate, kapena milungu ya Aamori, amene mukukhala mʼdziko lawo. Koma ine ndi banja langa, tidzatumikira Yehova.”
16 백성이 대답하여 가로되 `여호와를 버리고 다른 신들 섬기는 일을 우리가 결단코 하지 아니하오리니
Ndipo anthu anayankha, “Sizingatheke kuti timusiye Yehova ndi kutumikira milungu ina!
17 이는 우리 하나님 여호와 그가 우리와 우리 열조를 인도하여 애굽 땅 종 되었던 집에서 나오게 하시고 우리 목전에서 그 큰 이적들을 행하시고 우리가 행한 모든 길에서, 우리의 지난 모든 백성 중에서 우리를 보호하셨음이며
Yehova Mulungu wathu ndiye amene anatitulutsa ife ndi makolo athu mu ukapolo, mʼdziko la Igupto. Tinaona ndi maso athu zizindikiro zozizwitsa zimene anachita. Iye anatiteteza pa ulendo wathu wonse ndi pakati pa mitundu yonse imene tinkakumana nayo.
18 여호와께서 또 모든 백성 곧 이 땅에 거하던 아모리 사람을 우리 앞에서 쫓아내셨음이라 그러므로 우리도 여호와를 섬기리니 그는 우리 하나님이심이니이다!'
Ife tikufika Iye anapirikitsa anthu onse pamodzi ndi Aamori amene ankakhala mʼdzikoli. Ifenso tidzatumikira Yehova chifukwa Iye ndiye Mulungu.”
19 여호수아가 백성에게 이르되 `너희가 여호와를 능히 섬기지 못할 것은 그는 거룩하신 하나님이시요! 질투하는 하나님이시니 너희 허물과 죄를 사하지 아니하실 것임이라
Koma Yoswa anati kwa anthuwo, “Inutu simungathe kutumikira Yehova. Iye ndi Mulungu woyera, salola kupikisana naye. Sadzakukhululukirani ngati mumuwukira ndi kumuchimwira.
20 만일 너희가 여호와를 버리고 이방 신들을 섬기면 너희에게 복을 내리신 후에라도 돌이켜 너희에게 화를 내리시고 너희를 멸하시리라'
Ngati inu musiya Yehova ndi kutumikira milungu yachilendo, adzakufulatirani. Iye adzakulangani ndi kukuwonongani ngakhale kuti poyamba anakuchitirani zabwino.”
21 백성이 여호수아에게 말하되 `아니니이다! 우리가 정녕 여호와를 섬기겠나이다!'
Koma anthuwo anati kwa Yoswa, “Ayi! Ife tidzatumikira Yehova.”
22 여호수아가 백성에게 이르되 `너희가 여호와를 택하고 그를 섬기리라 하였으니 스스로 증인이 되었느니라' 그들이 가로되 `우리가 증인이 되었나이다'
Kenaka Yoswa anati, “Inu mukudzichitira nokha umboni kuti mwasankha kutumikira Yehova.” Iwo anayankha kuti, “Inde ife ndife mboni.”
23 여호수아가 가로되 `그러면 이제 너희 중에 있는 이방 신들을 제하여 버리고 너희 마음을 이스라엘의 하나님 여호와께로 향하라!'
Yoswa anati, “Tsono chotsani milungu yachilendo imene ili pakati panu ndipo perekani mitima yanu kwa Yehova Mulungu wa Israeli.”
24 백성이 여호수아에게 말하되 `우리 하나님 여호와를 우리가 섬기고 그 목소리를 우리가 청종하리이다!' 한지라
Ndipo anthuwo anati kwa Yoswa, “Ife tidzatumikira Yehova Mulungu wathu ndi kumvera Iye.”
25 그 날에 여호수아가 세겜에서 백성으로 더불어 언약을 세우고 그들을 위하여 율례와 법도를 베풀었더라
Choncho pa tsiku limenelo Yoswa anachita pangano mʼmalo mwa anthuwo, ndipo pa Sekemu pomwepo iye anapereka malamulo ndi malangizo kwa anthu aja.
26 여호수아가 이 모든 말씀을 하나님의 율법책에 기록하고 큰 돌을 취하여 거기 여호와의 성소 곁에 있는 상수리나무 아래 세우고
Ndipo Yoswa analemba zinthu izi mʼbuku la malamulo a Mulungu. Kenaka iye anatenga mwala waukulu nawuyimika pansi pa mtengo wa thundu pa malo wopatulika a Yehova.
27 모든 백성에게 이르되 `보라, 이 돌이 우리에게 증거가 되리니 이는 여호와께서 우리에게 하신 모든 말씀을 이 돌이 들었음이라 그런즉 너희로 너희 하나님을 배반치 않게 하도록 이 돌이 증거가 되리라' 하고
Yoswa anati kwa anthu onse, “Tamvani! Mwala uwu udzakhala mboni yotitsutsa. Mwalawu wamva mawu onse amene Yehova wayankhula kwa ife. Udzakhala mboni yotitsutsa ngati mukhala osakhulupirika kwa Mulungu wanu.”
28 백성을 보내어 각기 기업으로 돌아가게 하였더라
Kenaka Yoswa analola anthu kuti apite, aliyense ku dera lake.
29 이 일 후에 여호와의 종 눈의 아들 여호수아가 일백 십세에 죽으매
Zitatha zinthu izi, Yoswa mwana wa Nuni, mtumiki wa Yehova, anamwalira ali ndi zaka 110,
30 무리가 그를 그의 기업의 경내 딤낫 세라에 장사하였으니 딤낫 세라는 에브라임 산지 가아스산 북이었더라
ndipo anamuyika mʼmanda mʼdziko lake, ku Timnati-Sera dziko lamapiri la ku Efereimu, kumpoto kwa phiri la Gaasi.
31 이스라엘이 여호수아의 사는 날 동안과 여호수아 뒤에 생존한 장로들 곧 여호와께서 이스라엘을 위하여 행하신 모든 일을 아는 자의 사는 날 동안 여호와를 섬겼더라
Israeli anatumikira Yehova pa nthawi yonse imene Yoswa anali ndi moyo ndiponso pa nthawi ya akuluakulu amene anali moyo Yoswa atamwalira, anthu amene ankadziwa zonse zimene Yehova anachitira Israeli.
32 이스라엘 자손이 애굽에서 이끌어 낸 요셉의 뼈를 세겜에 장사하였으니 이 곳은 야곱이 세겜의 아비 하몰의 자손에게 금 일백개를 주고 산 땅이라 그것이 요셉 자손의 기업이 되었더라
Ndipo mafupa a Yosefe amene Aisraeli anawatulutsa ku Igupto anawayika mʼmanda a ku Sekemu pa malo amene Yakobo anagula ndi ndalama zasiliva 100 kwa ana a Hamori, abambo a Sekemu. Malo awa anakhala cholowa cha adzukulu a Yosefe.
33 아론의 아들 엘르아살도 죽으매 무리가 그를 그 아들 비느하스가 에브라임 산지에서 받은 산에 장사하였더라
Ndipo Eliezara mwana wa Aaroni anamwalira ndipo anayikidwa mʼmanda ku Gibeya, malo amene anapatsidwa kwa Finehasi mwana wake, mʼdziko lamapiri la Efereimu.

< 여호수아 24 >