< 에스겔 31 >
1 제 십 일년 삼월 초 일일에 여호와의 말씀이 내게 임하여 가라사대
Pa tsiku loyamba la mwezi wachitatu, chaka cha khumi ndi chimodzi, Yehova anandiyankhula kuti:
2 인자야 너는 애굽 왕 바로와 그 무리에게 이르기를 네 큰 위엄을 뉘게 비하랴
“Iwe mwana wa munthu, unene kwa Farao mfumu ya Igupto ndi gulu lake lankhondo. Awawuze kuti, “‘Kodi mu ukulu wanu ndani angafanane ndi inu?
3 볼지어다 앗수르 사람은 가지가 아름답고 그늘은 삼림의 그늘 같으며 키가 높고 꼭대기가 구름에 닿은 레바논 백향목이었느니라
Taonani, ndidzakufanizirani ndi mtengo wa mkungudza wa ku Lebanoni, wa nthambi zokongola zochititsa mthunzi mʼnkhalango. Unali wautali, msonga zake zooneka pamwamba pa nkhalango.
4 물들이 그것을 기르며 깊은 물이 그것을 자라게 하며 강들이 그 심긴 곳을 둘러 흐르며 보의 물이 들의 모든 나무에까지 미치매
Madzi ndiwo ankawukulitsa mkungudzawo, akasupe ozama ankawutalikitsa. Mitsinje yake inkayenda mozungulira malo amene unaliwo ndipo ngalande zake zinkafika ku mitengo yonse ya mʼmunda.
5 그 나무가 물이 많으므로 키가 들의 모든 나무보다 높으며 굵은 가지가 번성하며 가는 가지가 길게 빼어났고
Choncho unatalika kwambiri kupambana mitengo yonse ya mʼmunda. Nthambi zake zinachuluka ndi kutalika kwambiri, chifukwa inkalandira madzi ambiri.
6 공중의 모든 새가 그 큰 가지에 깃들이며 들의 모든 짐승이 그 가는 가지 밑에 새끼를 낳으며 모든 큰 나라가 그 그늘 아래 거하였었느니라
Mbalame zonse zamlengalenga zinkamanga zisa zake mʼnthambi za mtengowo. Nyama zakuthengo zonse zinkaswanirana mʼmunsi mwa nthambi zake. Mitundu yotchuka ya anthu inkakhala mu mthunzi wake.
7 그 뿌리가 큰 물가에 있으므로 그 나무가 크고 가지가 길어 모양이 아름다우매
Unali wokongola kwambiri, wa nthambi zake zotambalala, chifukwa mizu yake inazama pansi kumene kunali madzi ochuluka.
8 하나님의 동산의 백향목이 능히 그를 가리우지 못하며 잣나무가 그 굵은 가지만 못하며 단풍나무가 그 가는 가지만 못하며 하나님의 동산의 아무 나무도 그 아름다운 모양과 같지 못하였도다
Mʼmunda wa Mulungu munalibe mkungudza wofanana nawo, kapena mitengo ya payini ya nthambi zofanafana ndi nthambi zake. Munalibenso mtengo wa mkuyu nthambi zofanafana ndi zake. Mʼmunda wa Mulungu munalibe mtengo wina uliwonse wofanana ndi iwo kukongola kwake.
9 내가 그 가지로 많게 하여 모양이 아름답게 하였더니 하나님의 동산 에덴에 있는 모든 나무가지가 다 투기하였느니라
Ine ndinawupanga wokongola wa nthambi zochuluka. Mitengo yonse ya mu Edeni, mʼmunda wa Mulungu inawuchitira nsanje.
10 그러므로 나 주 여호와가 말하노라 그의 키가 높고 꼭대기가 구름에 닿아서 높이 빼어났으므로 마음이 교만하였은즉
“‘Nʼchifukwa chake Ine Ambuye Yehova ndikuti: Chifukwa kuti mtengowo unatalika kwambiri, unatulutsa songa zake mpaka ku thambo, ndipo unadzikweza chifukwa cha msinkhu wake,
11 내가 열국의 능한 자의 손에 붙일지라 그가 임의로 대접할 것은 내가 그의 악을 인하여 쫓아 내었음이라
ndinawupereka mʼdzanja la mfumu ya mitundu ya anthu kuti awulange molingana ndi kuyipa kwake.
12 열국의 강포한 다른 민족이 그를 찍어버렸으므로 그 가는 가지가 산과 모든 골짜기에 떨어졌고 그 굵은 가지가 그 땅 모든 물가에 꺽어졌으며 세상 모든 백성이 그를 버리고 그 그늘 아래서 떠나매
Anthu ankhanza kwambiri amitundu ya anthu achilendo adzawudula ndi kuwusiya. Nthambi zake zidzagwera pa mapiri ndi mu zigwa zonse. Nthambi zake zidzathyokera mʼmitsinje ya mʼdzikomo. Motero mitundu yonse ya anthu a dziko lapansi amene ankasangalala mu mthunzi wake idzawusiya.
13 공중의 모든 새가 그 넘어진 나무에 거하며 들의 모든 짐승이 그 가지에 있으리니
Mbalame zonse zamlengalenga zidzakhala pa mtengo wakugwawo, ndipo nyama zakuthengo zonse zidzakhala pa nthambi zake.
14 이는 물 가에 있는 모든 나무로 키가 높다고 교만치 못하게 하며 그 꼭대기로 구름에 닿지 못하게 하며 또 물 대임을 받는 능한 자로 스스로 높아 서지 못하게 함이니 그들을 다 죽는데 붙여서 인생 중 구덩이로 내려가는 자와 함께 지하로 내려가게 하였음이니라
Zidzakutero kuti pasakhalenso mitengo inanso ya mʼmbali mwa madzi yotalika kwambiri, imene idzatalike kwambiri ndi songa zake kufika mpaka ku mitambo. Komanso kuti pasadzakhalenso mitengo yolandira bwino madzi, imene idzatalika motero. Paja yonseyo kutha kwake ndi kufa, kupita ku dziko lapansi kukhala ndi anthu akufa amene analowa mʼmanda kale.
15 나 주 여호와가 말하노라 그가 음부에 내려가던 날에 내가 그를 위하여 애곡하게 하며 깊은 바다를 덮으며 모든 강을 쉬게 하며 큰 물을 그치게 하고 레바논으로 그를 위하여 애곡하게 하며 들의 모든 나무로 그로 인하여 쇠잔하게 하였느니라 (Sheol )
“‘Ine Ambuye Yehova ndikuti: Pa nthawi imene mkungudzawo unatsikira ku manda, ndinawuza nyanja kuti iwulire maliro pakuwuphimba. Ndinawumitsa mitsinje ndipo madzi ambiri anaphwa. Ndinabweretsa mdima pa Lebanoni chifukwa cha mtengowo ndipo mitengo yonse ya mʼdzikomo inawuma. (Sheol )
16 내가 그로 구덩이에 내려가는 자와 함께 음부에 떨어뜨리던 때에 열국으로 그 떨어지는 소리를 인하여 진동하게 하였고 물 대임을받은 에덴의 모든 나무 곧 레바논의 뛰어나고 아름다운 나무들로 지하에서 위로를 받게 하였느니라 (Sheol )
Mitundu ya anthu inagwedezeka pakumva mkokomo wa kugwa kwake, pamene ndinawutsitsira ku manda pamodzi ndi iwo amene anafa. Pamenepo ku dziko la akufa mitengo yonse ya ku Edeni pamodzi ndi ya ku Lebanoni yosankhidwa bwino inasangalatsidwa chifukwa cha zimenezi. (Sheol )
17 그러나 그들도 그와 함께 음부에 내려 칼에 살륙을 당한 자에게 이르렀나니 그들은 옛적에 그의 팔이 된 자요 열국 중에서 그 그늘 아래 거하던 자니라 (Sheol )
Amene ankakhala mu mthunzi wake, amene ankayanjana nawo, iwonso anapita nawo pamodzi ku manda, kukakhala pamodzi ndi amene anaphedwa ndi lupanga pakati pa mitundu ya anthu. (Sheol )
18 너의 영화와 광대함이 에덴 모든 나무 중에 어떤 것과 같은고 그러나 네가 에덴 나무와 함께 지하에 내려갈 것이요 거기서 할례 받지 못하고 칼에 살륙 당한 자 중에 누우리라 이들은 바로와 그 모든 군대니라 나 주 여호와의 말이니라 하라
“‘Ndi mitengo iti ya mu Edeni imene ingafanane ndi kukongola kwako ndi ulemerero wako? Komabe iwenso, udzatsikira ku dziko la anthu akufa pamodzi ndi mitengo ya mu Edeni. Udzagona pamodzi ndi anthu osachita mdulidwe, anthu amene anaphedwa pa nkhondo. “‘Mtengowo ndi Farao ndi gulu lake lankhondo, akutero Ambuye Yehova.’”