< 에스겔 23 >

1 여호와의 말씀이 또 내게 임하여 가라사대
Yehova anandiyankhula nati:
2 인자야 두 여인이 있었으니 한 어미의 딸이라
“Iwe mwana wa munthu, panali atsikana awiri ana a mayi mmodzi.
3 그들이 애굽에서 행음하되 어렸을 때에 행음하여 그들의 유방이 눌리며 그 처녀의 가슴이 어루만진 바 되었었나니
Iwo ankachita za chiwerewere ku Igupto. Za chiwerewerezo anayamba ali achichepere. Kumeneko anthu ankangowasisita pa chifuwa ndi kuwagwiragwira mawere awo aja.
4 그 이름이 형은 오홀라요 아우는 오홀리바라 그들이 내게 속하여 자녀를 낳았나니 그 이름으로 말하면 오홀라는 사마리아요 오홀리바는 예루살렘이니라
Wamkulu dzina lake anali Ohola, ndipo mngʼono wakeyo anali Oholiba. Ine ndinawakwatira ndipo anabereka ana aamuna ndi ana aakazi. Ohola ndiye Samariya, ndipo Yerusalemu ndiye Oholiba.
5 오홀라가 내게 속하였을 때에 행음하여 그 연애하는 자 곧 그 이웃 앗수르 사람을 사모하였나니
“Ohola anachita zachiwerewere ngakhale anali mkazi wanga; ndipo iye anakangamira abwenzi ake a ku Asiriya.
6 그들은 다 자색 옷을 입은 방백과 감독이요 준수한 소년, 말 타는 자들이라
Amenewo anali asilikali ovala zibakuwa zamlangali, abwanamkubwa ndiponso atsogoleri a nkhondo. Onsewo anali anyamata osiririka ndipo ankakwera pa akavalo.
7 그가 앗수르 중에 잘 생긴 그 모든 자들과 행음하고 누구를 연애하든지 그들의 모든 우상으로 스스로 더럽혔으며
Ohola anachita zachiwerewere ndi onsewa, anthu otchuka a ku Asiriya. Iye anadziyipitsa ndi mafano a munthu aliyense amene anagona naye.
8 그가 젊었을 때에 애굽사람과 동침하매 그 처녀의 가슴이 어루만진바 되며 그 몸에 음란을 쏟음을 당한바 되었더니 그가 그 때부터 행음함을 마지 아니하였느니라
Iye sanaleke za chiwerewere zimene anaziphunzira ku Igupto. Paja akanali mtsikana anyamata ankagona naye. Iwo ankamusisita mawere akanali anthete nachita naye zachiwerewere.
9 그러므로 내가 그를 그 정든 자 곧 그 연애하는 앗수르 사람의 손에 붙였더니
“Nʼchifukwa chake Ine ndinamupereka kwa achikondi ake, Asiriya, amene iye ankawalakalaka.
10 그들이 그 하체를 드러내고 그 자녀를 빼앗으며 칼로 그를 죽여 그 누명을 여자에게 드러내었나니 이는 그들이 그에게 심문을 행함이니라
Iwowa anamuvula, namulanda ana ake aamuna ndi aakazi ndipo anamupha ndi lupanga. Ndipo atalangidwa choncho, iye anasanduka chinthu chonyozeka pakati pa akazi.
11 그 아우 오홀리바가 이것을 보고도 그 형보다 음욕을 더하며 그 형의 간음함보다 그 간음이 더 심하므로 그 형보다 더 부패하여 졌느니라
“Mphwake Oholiba anaona zimenezi natengerako. Koma iye anachita zachiwerewere kuposa mkulu wake.
12 그가 그 이웃 앗수르 사람을 연애하였나니 그들은 화려한 의복을 입은 방백과 감독이요 말타는 자들과 준수한 소년이었느니라
Iyenso anakangamira Asiriya, abwanamkubwa, olamulira asilikali, ankhondo ovala zovala zonse za nkhondo ndi okwera pa akavalo. Onsewa anali anyamata osiririka.
13 그 두 여인이 한 길로 행하므로 그도 더러워졌음을 내가 보았노라
Ndinaona kuti iyenso anadziyipitsa; ndipo onse awiriwo anatsata njira imodzi.
14 그가 음행을 더하였음은 붉은 것으로 벽에 그린 사람의 형상 곧 갈대아 사람의 형상을 보았음이니
“Koma Oholiba uja anachita chigololo kopitirira mkulu wake. Iye anaona zithunzi za amuna pa khoma, zithunzi za Ababuloni zolembedwa ndi inki yofiira,
15 그 형상은 허리를 띠로 동이고 머리를 긴 수건으로 쌌으며 용모는 다 존귀한 자 곧 그 고토 갈대아 바벨론 사람 같은 것이라
atamanga malamba mʼchiwuno mwawo ndi kuvala nduwira pa mitu yawo. Onse amaoneka ngati atsogoleri a magaleta a Ababuloni, mbadwa za ku Kaldeya.
16 그가 보고 곧 연애하여 사자를 갈대아 그들에게로 보내매
Oholiba atangowaona, anawalakalaka ndipo anatuma amithenga ku Kaldeya kukawayitana.
17 바벨론 사람이 나아와 연애하는 침상에 올라 음란으로 그를 더럽히매 그가 더럽힘을 입은 후에 그들을 싫어하는 마음이 생겼느니라
Ndipo Ababuloni anabwera nʼkudzagona naye. Choncho mwa chilakolako chawo anamuyipitsa. Koma atamuyipitsa choncho, iye ananyansidwa nawo.
18 그가 이와 같이 그 음행을 나타내며 그 하체를 드러내므로 내 마음이 그 형을 싫어한 것 같이 그를 싫어하였으나
Iye atachita chiwerewere chake poyera ndi kuonetsa umaliseche wake, Ine ndinamuchokera monyansidwa monga mmene ndinachitira ndi mʼbale wake.
19 그가 그 음행을 더하여 그 젊었을 때 곧 애굽 땅에서 음행하던 때를 생각하고
Koma anachitabe zachiwerewere osalekeza. Ankakumbukira masiku a ubwana wake pamene ankachita za chiwerewere mʼdziko la Igupto.
20 그 하체는 나귀 같고 그 정수는 말 같은 음란한 간부를 연애하였도다
Kumeneko iye ankalakalaka zibwenzi zake, amene ziwalo zawo zinali ngati za abulu ndipo kutentha kwawo kunali ngati kwa akavalo.
21 네가 젊었을 때에 행음하여 애굽 사람에게 네 가슴과 유방이 어루만진바 되었던 것을 오히려 생각하도다
Motero, iwe Oholiba unafuna kuchitanso zadama monga unkachitira ku Igupto pamene unali mtsikana. Nthawi imene ija ankakusisita pa chifuwa ndi kugwiragwira mawere ako osagwa aja.
22 그러므로 오홀리바야 나 주 여호와가 말하노라 내가 너의 연애하다가 싫어하던 자들을 격동시켜서 그들로 사방에서 와서 너를 치게 하리니
“Tsono iwe Oholiba, Ine Ambuye Yehova ndikuti: Ndidzakudzutsira zibwenzi zako zimene unkanyansidwa nazo zija kuti zilimbane nawe. Ndidzaziyitana kuti zibwere kuchokera mbali zonse.
23 그들은 바벨론 사람과 갈대아 모든 무리 브곳과 소아와 고아 사람과 또 그와 함께 한 모든 앗수르 사람 곧 준수한 소년이며 다 방백과 감독이며 귀인과 유명한 자, 다 말 타는 자들이라
Ndidzayitana anthu a ku Babuloni ndi Akaldeya onse, anthu a ku Pekodi, Sowa ndi Kowa pamodzi ndi Asiriya onse. Onsewa ndi amuna osiririka, abwanamkubwa, atsogoleri a ankhondo, oyenda pa magaleta, anthu a maudindo akuluakulu. Onsewa ndi okwera akavalo.
24 그들이 병기와 병거와 수레와 크고 작은 방패를 이끌고 투구 쓴 군대를 거느리고 치러 와서 너를 에워쌀지라 내가 심문권을 그들에게 맡긴즉 그들이 그 심문권대로 너를 심문하리라
Iwo adzabwera kudzalimbana nawe ndi zida za nkhondo, magaleta ndi ngolo, pamodzi ndi anthu ambiri. Adzakuzinga mbali zonse atavala zishango zankhondo ndi zipewa zankhondo. Ndidzakupereka kwa iwo kuti akulange ndipo adzakulanga monga momwe adzafunire.
25 내가 너를 향하여 투기를 발하리니 그들이 분노로 네게 행하여 네 코와 귀를 깎아버리고 남은 자를 칼로 엎드러뜨리며 네 자녀를 빼앗고 그 남은 자를 불에 사르며
Ndidzaonetsa mkwiyo wanga pa iwe ndipo iwo adzakulanga iwe mwankhanza. Adzadula mphuno zanu ndi makutu anu, ndipo amene adzatsalira mwa iwe adzaphedwa ndi lupanga. Iwo adzakulanda ana ako aamuna ndi aakazi ndipo amene adzatsalira adzaphedwa ndi moto.
26 또 네 옷을 벗기며 네 장식품을 빼앗을지라
Adzakuvulaninso zovala zanu ndikukulandani zodzikongoletsera zanu zamtengowapatali.
27 이와 같이 내가 네 음란과 애굽 땅에서부터 음행하던 것을 그치게 하여 너로 그들을 향하여 눈을 들지도 못하게 하며 다시는 애굽을 기억하지도 못하게 하리라
Motero ndidzathetsa zonyansa zako ndi zachigololo zomwe unaziyamba ku Igupto. Choncho sudzalakalaka za ku Igupto kapena kuzikumbukiranso.
28 나 주 여호와가 말하노라 내가 너의 미워하는 자와 네 마음에 싫어하는 자의 손에 너를 붙이리니
“Ine Ambuye Yehova ndikuti: Ndikukupereka mʼmanja mwa amene amadana nawe, kwa iwo amene unawafulatira moyipidwa nawo.
29 그들이 미워하는 마음으로 네게 행하여 네 모든 수고한 것을 빼앗고 너를 벌거벗겨 적신으로 두어서 네 음행의 벗은 몸 곧 네 음란하며 음행하던 것을 드러낼 것이라
Adzachita nawe mwachidani. Adzakulanda zonse zimene unagwirira ntchito. Adzakusiya wamaliseche ndiponso wausiwa. Kuyipa kwa makhalidwe ako achiwerewere kudzakhala pammbalambanda. Zonyansa zako ndi chiwerewere chako,
30 네가 이같이 당할 것은 네가 음란히 이방을 좇고 그 우상들로 더럽혔음이로다
zabweretsa izi pa iwe chifukwa unachita zonyansa ndi anthu a mitundu ndi kudziyipitsa ndi mafano awo.
31 네가 네 형의 길로 행하였은즉 내가 그의 잔을 네 손에 주리라
Unatsata zochita za mkulu wako; choncho Ine ndidzayika chikho cha chilango chake mʼdzanja lako.
32 나 주 여호와가 말하노라 깊고 크고 가득히 담긴 네 형의 잔을 네가 마시고 비소와 조롱을 당하리라
“Ine Ambuye Yehova ndikuti: “Udzamwera chikho cha mkulu wako, chikho chachikulu ndi chakuya; anthu adzakuseka ndi kukunyoza, pakuti chikhocho ndi chodzaza kwambiri.
33 네가 네 형 사마리아의 잔 곧 놀람과 패망의 잔에 넘치게 취하고 근심할지라
Udzaledzera ndipo mtima wako udzadzaza ndi chisoni. Chimenechi ndi chikho chachiwonongeko ndi chipasupasu, chikho cha mkulu wako Samariya.
34 네가 그 잔을 다 기울여 마시고 그 깨어진 조각을 씹으며 네 유방을 꼬집을 것은 내가 이렇게 말하였음이니라 나 주 여호와의 말이니라
Udzamwa chikhocho mpaka kugugudiza. Tsono udzaphwanyaphwanya chikhocho ndipo udzangʼamba mawere ako ndi zigoba zake. Ine ndayankhula, akutero Ambuye Yehova.
35 그러므로 나 주 여호와가 말하노라 네가 나를 잊었고 또 나를 네 등 뒤에 버렸은즉 너는 네 음란과 네 음행의 죄를 담당할지니라 하시니라
“Chifukwa chake, Ine Ambuye Yehova ndikuti: Popeza wandiyiwala Ine ndi kundifulatira, chomwecho uyenera kulangidwa chifukwa cha zonyansa zako ndi chiwerewere chako.”
36 여호와께서 또 내게 이르시되 인자야 네가 오홀라와 오홀리바를 국문하려느냐 그러면 그 가증한 일을 그들에게 고하라
Yehova anandifunsa kuti, “Iwe mwana wa munthu, kodi udzaweruza Ohola ndi Oholiba? Tsono uwayimbe mlandu chifukwa cha machitidwe awo onyansa.
37 그들이 행음하였으며 피를 손에 묻혔으며 또 그 우상과 행음하며 내게 낳아준 자식들을 우상을 위하여 화제로 살랐으며
Iwo achita chigololo ndipo anapha anthu. Anachita chigololo popembedza mafano awo. Ngakhale ana amene anandiberekera Ine anawapereka kwa mafanowo ngati chakudya chawo.
38 이외에도 그들이 내게 행한 것이 있나니 당일에 내 성소를 더럽히며 내 안식일을 범하였도다
Anachitanso izi: Iwo anayipitsa malo anga opatulika ndi kudetsa masabata anga.
39 그들이 자녀를 죽여 그 우상에게 드린 당일에 내 성소에 들어와서 더럽혔으되 그들이 내 성전 가운데서 그렇게 행하였으며
Atapereka ana awo kwa mafano, tsiku lomwelo anakalowanso mʼNyumba yanga yopatulika ndi kuyipitsamo. Izi ndi zimene anachita mʼNyumba mwanga.
40 또 사자를 원방에 보내어 사람을 불러오게 하고 그들이 오매 그들을 위하여 목욕하며 눈썹을 그리며 스스로 단장하고
“Iwo anatuma amithenga kukayitana amuna a ku mayiko akutali. Anthuwo atabwera, abale awiri aja anasambasamba, kudzola utoto wodzikometsera kumaso, kenaka ndi kuvala zovala zamakaka.
41 화려한 자리에 앉아 앞에 상을 베풀고 내 향과 기름을 그 위에 놓고
Anakhala pa bedi lokongola ndipo patsogolo pawo panali tebulo pamene munayikapo lubani ndi mafuta. Zonse zowapatsa Ine.
42 그 무리와 편히 지껄이고 즐겼으며 또 광야에서 잡류와 술취한 사람을 청하여 오매 그들이 팔쇠를 그 손목에 끼우고 아름다운 면류관을 그 머리에 씌웠도다
“Mfuwu wa chigulu cha anthu unamveka. Anthu oledzera ochokera ku chipululu anabwera pamodzi ndi anthu wamba ndipo anaveka akaziwo zibangiri kumanja ndi zipewa zaufumu zokongola ku mutu.
43 내가 음행으로 쇠한 여인을 가리켜 말하노라 그가 그래도 그들과 피차 행음하는도다
Ndipo ine ndinati za mkazi wotheratu ndi chigololoyo, ‘Tsono asiyeni kuti achite naye monga wachiwerewere, pakuti ichi ndi chimene iye ali basi.’
44 그들이 그에게 나아오기를 기생에게 나아옴 같이 음란한 여인 오홀라와 오홀리바에게 나아왔은즉
Tsono anapita kwa iwo monga mmene anthu amapitira kwa mkazi wadama. Momwemo anapita kwa Ohola ndi kwa Oholiba kukachita nawo zadama.
45 의인이 음부를 심문함 같이 심문하며 피를 흘린 여인을 심문함 같이 심문하리니 그들은 음부요 또 피가 그 손에 묻었음이니라
Koma anthu olungama adzawazenga anthuwa mlandu wa chigololo ndi wa kupha anthu. Ndi iwodi anthu achigololo ndiponso mʼmanja mwawo muli magazi.
46 나 주 여호와가 말하노라 내가 군대를 거느리고 와서 치게 하여 그들로 학대와 약탈을 당하게 하리니
“Ambuye Yehova akuti: Itanitsani chigulu cha anthu kuti chidzawalange ndi kulanda chuma chawo.
47 그 군대가 그들을 돌로 치며 칼로 죽이고 그 자녀도 죽이며 그 집들을 불사르리라
Anthuwo adzawaponye miyala akazi awiriwo ndi kuwatema ndi malupanga awo. Ana awo aamuna ndi aakazi adzawaphe ndi kutentha nyumba zawo.
48 이와 같이 내가 이 땅에서 음란을 그치게 한즉 모든 여인이 경성하여 너희 음행을 본받지 아니하리라
“Motero Ine ndidzathetsa zachigololo mʼdzikomo, ndipo akazi onse adzatengapo phunziro kuti asadzachite zachigololo monga za iwowo.
49 그들이 너희 음란으로 너희에게 보응한즉 너희가 모든 우상을 위하던 죄를 담당할지라 너희가 나를 주 여호와인 줄 알리라 하시니라
Ndidzawalanga chifukwa cha ntchito zawo za dama ndipo adzazunzika chifukwa cha tchimo lawo lopembedza mafano. Choncho adzadziwa kuti Ine ndine Ambuye Yehova.”

< 에스겔 23 >