< 에스겔 14 >

1 이스라엘 장로 두어 사람이 나아와 내 앞에 앉으니
Tsiku lina ena mwa akuluakulu a Israeli anabwera kwa ine ndipo anakhala pansi pamaso panga.
2 여호와의 말씀이 내게 임하여 가라사대
Ndipo Yehova anandipatsa uthenga uwu nati,
3 인자야! 이 사람들이 자기 우상을 마음에 들이며 죄악의 거치는 것을 자기 앞에 두었으니 그들이 내게 묻기를 내가 조금인들 용납하랴
“Iwe mwana wa munthu, anthu awa ayika mtima pa mafano awo. Ayikanso maso awo pa zinthu zina zoyipa zopunthwitsa. Kodi ayembekezera kuti ndiwayankhe chimene atandifunse?
4 그런즉 너는 그들에게 말하여 이르라 나 주 여호와가 말하노라 이스라엘 족속 중에 무릇 그 우상을 마음에 들이며 죄악의 거치는 것을 자기 앞에 두고 선지자에게 나아오는 자에게는 나 여호와가 그 우상의 많은대로 응답하리니
Tsono yankhula nawo ndi kuwawuza kuti zimene akunena Ambuye Yehova: ‘Ngati Mwisraeli aliyense ayika mtima wake pa mafano ndi kuyika maso ake pa zinthu zoyipa zopunthwitsa, kenaka nʼkupita kwa mneneri, Ineyo Yehova mwini wakene ndidzamuyankha molingana ndi kuchuluka kwa mafano ake.
5 이는 이스라엘 족속이 다 그 우상으로 인하여 나를 배반하였으므로 내가 그들의 마음에 먹은대로 그들을 잡으려 함이니라
Ine ndidzachita zimenezi kuti mwina nʼkukopa mitima ya anthu a Israeli, amene andisiya chifukwa cha mafano awo.’
6 그런즉 너는 이스라엘 족속에게 이르기를 주 여호와의 말씀에 너희는 마음을 돌이켜 우상을 떠나고 얼굴을 돌이켜 모든 가증한 것을 떠나라
“Nʼchifukwa chake uwawuze Aisraeli kuti Ine Ambuye Yehova ndikuti: Lapani! Siyani mafano anu ndi ntchito zanu zonse zonyansa!
7 이스라엘 족속과 이스라엘 가운데 우거하는 외인 중에 무릇 나를 떠나고 자기 우상을 마음에 들이며 죄악의 거치는 것을 자기 앞에 두고 자기를 위하여 내게 묻고자 하여 선지자에게 나아오는 자에게는 나 여호와가 친히 응답하여
“‘Ngati Mwisraeli wina aliyense kapena mlendo wina aliyense wokhala pakati pa Israeli adzichotsa yekha kwa Ine ndi kuyika mtima pa mafano ake ndi kuyikanso maso ake pa zinthu zopunthwitsa ndipo kenaka nʼkupita kwa mneneri kukafunsa nzeru, Ineyo Yehova mwini wakene ndidzamuyankha.
8 그 사람을 대적하여 그들로 놀라움과 감계와 속담거리가 되게 하여 내 백성 가운데서 끊으리니 너희가 나를 여호와인 줄 알리라
Ine ndidzalimbana naye munthu ameneyo ndipo ndidzamusandutsa chitsanzo ndi chisudzo. Ndidzamuchotsa pakati pa anthu anga. Pamenepo inu mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova.
9 만일 선지자가 유혹을 받고 말을 하면 나 여호와가 그 선지자로 유혹을 받게 하였음이어니와 내가 손을 펴서 내 백성 이스라엘 가운데서 그를 멸할 것이라
“‘Ndipo ngati mneneri anyengedwa nanenera, Ine Yehova ndiye ndamunyenga mneneri ameneyo, ndipo ndidzatambasula dzanja langa kumukantha ndi kumuwononga pakati pa anthu anga Aisraeli.
10 선지자의 죄악과 그에게 묻는 자의 죄악이 같은즉 각각 자기의 죄악을 담당하리니
Iwo adzalangidwa chifukwa cha kulakwa kwawo. Chilango cha wodzafunsira nzeru kwa mneneri chidzafanana ndi chilango cha mneneriyo.
11 이는 이스라엘 족속으로 다시는 미혹하여 나를 떠나지 않게 하며 다시는 모든 범죄함으로 스스로 더럽히지 않게 하여 그들로 내 백성을 삼고 나는 그들의 하나님이 되려 함이니라 나 주 여호와의 말이니라 하셨다 하라
Ndidzachita zimenezi kuti Aisraeli asasocherenso kundisiya Ine ndi kuti asadziyipitsenso ndi machimo awo. Adzakhala anthu anga, ndipo Ine ndidzakhala Mulungu wawo, akutero Ambuye Yehova.’”
12 여호와의 말씀이 또 내게 임하여 가라사대
Yehova anayankhula nane kuti,
13 인자야 가령 어느 나라가 불법하여 내게 범죄하므로 내가 손을 그 위에 펴서 그 의뢰하는 양식을 끊어 기근을 내려서 사람과 짐승을 그 나라에서 끊는다 하자
“Iwe mwana wa munthu, ngati dziko lindichimwira posandikhulupirira, Ine ndidzatambasula dzanja langa kulikantha pochepetsa chakudya chake. Ndidzatumiza njala pa dzikolo ndi kuwononga anthu ake ndi nyama zomwe.
14 비록 노아, 다니엘, 욥, 이 세사람이 거기 있을지라도 그들은 자기의 의로 자기의 생명만 건지리라 나 주 여호와의 말이니라
Ngakhale anthu atatu awa, Nowa, Danieli ndi Yobu akanakhala mʼmenemo, akanangopulumutsa moyo wawo chifukwa cha chilungamo chawo. Ndikutero Ine Ambuye Yehova.
15 가령 내가 사나운 짐승으로 그 땅에 통행하여 적막케 하며 황무케 하여 사람으로 그 짐승을 인하여 능히 통행하지 못하게 한다 하자
“Kapena ndikanatumiza zirombo mʼdziko monse ndi kulisiya lopanda anthu, ndipo dzikolo nʼkukhala chipululu chakuti munthu sangadutse chifukwa cha zirombo.
16 비록 이 세 사람이 거기 있을지라도 나의 삶을 두고 맹세하노니 그들은 자녀도 건지지 못하고 자기만 건지겠고 그 땅은 황무하리라 나 주 여호와의 말이니라
Apanso, ndikunenetsa Ine Ambuye Yehova kuti, ‘Ngakhale anthu atatu awa akanakhalamo, sakanatha kupulumutsa ana awo aamuna ndi aakazi. Iwo okha akanapulumuka, koma dziko likanasanduka chipululu.’
17 가령 내가 칼로 그 땅에 임하게 하고 명하기를 칼아 이 땅에 통행하라 하여 사람과 짐승을 거기서 끊는다 하자
“Kapena ndikanatumiza lupanga mʼdzikolo ndi kunena kuti, ‘Lupanga lipite mʼdziko monse,’ ndi kuwononga anthu ake ndi nyama zomwe.
18 비록 이 세 사람이 거기 있을지라도 나의 삶을 두고 맹세하노니 그들은 자녀도 건지지 못하고 자기만 건지리라 나 주 여호와의 말이니라
Apanso ndikunenetsa Ine Ambuye Yehova kuti, ‘Ngakhale anthu atatu awa akanakhalamo, sakanatha kupulumutsa ana awo aamuna kapena ana aakazi. Iwo okha akanapulumuka.’
19 가령 내가 그 땅에 온역을 내려 죽임으로 내 분을 그 위에 쏟아 사람과 짐승을 거기서 끊는다 하자
“Kapena ndikanatumiza mliri mʼdzikomo ndi kuonetsa ukali wanga pokhetsa magazi, kuwononga anthu ake ndi nyama zomwe.
20 비록 노아, 다니엘, 욥이 거기 있을지라도 나의 삶을 두고 맹세하오니 그들은 자녀도 건지지 못하고 자기의 의로 자기의 생명만 건지리라 나 주 여호와의 말이니라 하시니라
Apanso ndikunenetsa Ine Ambuye Yehova kuti ngakhale Nowa, Danieli ndi Yobu akanakhala mʼmenemo, sakanatha ngakhale kupulumutsa mwana wamwamuna kapena wamkazi. Akanangodzipulumutsa okha chifukwa cha chilungamo chawo.
21 주 여호와께서 가라사대 내가 나의 네 가지 중한 벌 곧 칼과 기근과 사나운 짐승과 온역을 예루살렘에 함께 내려 사람과 짐승을 그 중에서 끊으리니 그 해가 더욱 심하지 않겠느냐
“Pakuti Ambuye Yehova akuti: Kudzakhala zoopsa kwambiri pamene ndidzatumiza pa Yerusalemu zilango zanga zinayi izi: lupanga, njala, zirombo ndi mliri kuti ziwononge anthu ake ndi nyama zomwe!
22 그러나 그 가운데 면하는 자가 남아 있어 끌려 나오리니 곧 자녀들이라 그들이 너희에게로 나아 오리니 너희가 그 행동과 소위를 보면 내가 예루살렘에 내린 재앙 곧 그 내린 모든 일에 대하여 너희가 위로를 받을 것이라
Komabe padzakhala ena opulumuka, ana aamuna ndi ana aakazi amene adzatulutsidwa mʼdzikomo. Iwo adzabwera kwa inu, ndipo mukadzaona makhalidwe awo ndi zochita zawo, mitima yanu idzakhala pansi mukadzakumbukira chilango chimene ndinachita pa Yerusalemu.
23 너희가 그 행동과 소위를 볼 때에 그들로 인하여 위로를 받고 내가 예루살렘에서 행한 모든 일이 무고히 한 것이 아닌 줄을 알리라 나 주 여호와의 말이니라
Mitima yanu idzakhala pansi mukadzaona makhalidwe awo ndi zochita zawo. Tsono mudzadziwa kuti Yerusalemu sindinamuchite zimenezi popanda chifukwa, akutero Ambuye Yehova.”

< 에스겔 14 >