< 전도서 11 >
1 너는 네 식물을 물 위에 던지라 여러날 후에 도로 찾으리라
Ponya chakudya chako pa madzi, udzachipezanso patapita masiku ambiri.
2 일곱에게나 여덟에게 나눠줄지어다 무슨 재앙이 땅에 임할는지 네가 알지 못함이니라
Ndalama zako uzisungitse kwa anthu asanu ndi awiri, inde kwa anthu asanu ndi atatu, pakuti sudziwa ndi tsoka lanji limene likubwera pa dziko.
3 구름에 비가 가득하면 땅에 쏟아지며 나무가 남으로나 북으로나 쓰러지면 그 쓰러진 곳에 그냥 있으리라
Ngati mitambo yadzaza ndi madzi, imagwetsa mvula pa dziko lapansi. Mtengo ukagwera cha kummwera kapena cha kumpoto, ndiye kuti udzagonera kumene wagwerako.
4 풍세를 살펴보는 자는 파종하지 아니할 것이요 구름을 바라보는 자는 거두지 아니하리라
Amene amayangʼana mphepo sadzadzala; amene amayangʼana mitambo sadzakolola.
5 바람의 길이 어떠함과 아이 밴 자의 태에서 뼈가 어떻게 자라는 것을 네가 알지 못함같이 만사를 성취하시는 하나님의 일을 네가 알지 못하느니라
Momwe sudziwira mayendedwe a mphepo, kapena momwe mzimu umalowera mʼthupi la mwana mʼmimba mwa amayi, momwemonso sungathe kudziwa ntchito za Mulungu, Mlengi wa zinthu zonse.
6 너는 아침에 씨를 뿌리고 저녁에도 손을 거두지 말라 이것이 잘 될는지, 저것이 잘 될는지, 혹 둘이 다 잘 될는지 알지 못함이니라
Dzala mbewu zako mmawa ndipo madzulo usamangoti manja lobodo, pakuti sudziwa chimene chidzapindula, mwina ichi kapena icho, kapena mwina zonse ziwiri zidzachita bwino.
7 빛은 실로 아름다운 것이라 눈으로 해를 보는 것이 즐거운 일이로다
Kuwala nʼkwabwino, ndipo maso amasangalala kuona dzuwa.
8 사람이 여러 해를 살면 항상 즐거워할지로다 그러나 캄캄한 날이 많으리니 그 날을 생각할지로다 장래 일은 다 헛되도다
Munthu akakhala wa zaka zambiri, mulekeni akondwerere zaka zonsezo, koma iye azikumbukira masiku a mdima, pakuti adzakhala ochuluka. Chilichonse chimene chikubwera ndi chopanda phindu.
9 청년이여 네 어린 때를 즐거워 하며 네 청년의 날을 마음에 기뻐하여 마음에 원하는 길과 네 눈이 보는대로 좇아 행하라 그러나 하나님이 이 모든 일로 인하여 너를 심판하실 줄 알라
Kondwera mnyamata iwe, pamene ukanali wamngʼono, ndipo mtima wako usangalale pa nthawi ya unyamata wako. Tsatira zimene mtima wako ukufuna, ndiponso zimene maso ako akuona, koma dziwa kuti pa zinthu zonsezo Mulungu adzakuweruza.
10 그런즉 근심으로 네 마음에서 떠나게 하며 악으로 네 몸에서 물러가게 하라 어릴 때와 청년의 때가 다 헛되니라
Choncho uchotse zokusautsa mu mtima mwako, upewe zokupweteka mʼthupi mwako, pakuti unyamata ndi ubwana ndi zopandapake.