< 디모데후서 1 >

1 하나님의 뜻으로 말미암아 그리스도 예수 안에 있는 생명의 약속대로 그리스도 예수의 사도 된 바울은
Paulo mtumwi wa Khristu Yesu mwa chifuniro cha Mulungu. Anandituma kuti ndilalike za lonjezo la moyo umene uli mwa Khristu Yesu.
2 사랑하는 아들 디모데에게 편지하노니 하나님 아버지와 그리스도 예수 우리 주께로부터 은혜와 긍휼과 평강이 네게 있을지어다
Kwa Timoteyo, mwana wanga wokondedwa: Chisomo, chifundo ndi mtendere zochokera kwa Mulungu Atate ndi Ambuye athu Yesu Khristu.
3 나의 밤낮 간구하는 가운데 쉬지 않고 너를 생각하여 청결한 양심으로 조상적부터 섬겨 오는 하나님께 감사하고
Ndikuyamika Mulungu amene ndimamutumikira ndi chikumbumtima chosatsutsika, monga momwe ankachitira makolo anga. Usiku ndi usana ndimakukumbukira mosalekeza mʼmapemphero anga.
4 네 눈물을 생각하여 너 보기를 원함은 내 기쁨이 가득하게 하려함이니
Ndikamakumbukira misozi yako, ndimalakalaka nditakuona kuti ndidzazidwe ndi chimwemwe.
5 이는 네 속에 거짓이 없는 믿음을 생각함이라 이 믿음은 먼저 네 외조모 로이스와 네 어머니 유니게 속에 있더니 네 속에도 있는 줄을 확신하노라
Ndakumbukira za chikhulupiriro chako choona chimene chinayamba mwa agogo ako a Loisi ndi mwa amayi ako Yunike ndipo ndikutsimikiza mtima kuti chilinso mwa iwe.
6 그러므로 내가 나의 안수함으로 네 속에 있는 하나님의 은사를 다시 불일듯 하게 하기 위하여 너로 생각하게 하노니
Nʼchifukwa chake ndikukukumbutsa kuti upemerere monga amachitira moto, mphatso imene Mulungu anakupatsa nditakusanjika manja.
7 하나님이 우리에게 주신 것은 두려워하는 마음이 아니요 오직 능력과 사랑과 근신하는 마음이니
Pakuti Mzimu amene Mulungu anatipatsa, si Mzimu wotipatsa manyazi, koma Mzimu wotipatsa mphamvu, chikondi ndi kudzisunga.
8 그러므로 네가 우리 주의 증거와 또는 주를 위하여 갇힌 자 된 나를 부끄러워 말고 오직 하나님의 능력을 좇아 복음과 함께 고난을 받으라!
Choncho usachite manyazi kuchitira umboni Ambuye athu, kapena kuchita manyazi chifukwa cha ine wamʼndende. Koma umve nane zowawa chifukwa cha Uthenga Wabwino, mothandizidwa ndi mphamvu za Mulungu.
9 하나님이 우리를 구원하사 거룩하신 부르심으로 부르심은 우리의 행위대로 하심이 아니요 오직 자기 뜻과 영원한 때 전부터 그리스도 예수 안에서 우리에게 주신 은혜대로 하심이라 (aiōnios g166)
Iye anatipulumutsa ndipo anatiyitanira ku moyo oyera mtima, osati chifukwa cha chilichonse chimene tinachita, koma chifukwa cha chikonzero ndi chisomo chake. Chisomo chimenechi anatipatsa ife mwa Khristu Yesu nthawi isanayambe. (aiōnios g166)
10 이제는 우리 구주 그리스도 예수의 나타나심으로 말미암아 나타났으니 저는 사망을 폐하시고 복음으로써 생명과 썩지 아니할 것을 드러내신지라
Koma tsopano Mulungu watiwululira kudzera mʼkuoneka kwa Mpulumutsi wathu, Khristu Yesu, amene anathetsa mphamvu za imfa ndipo mwa Uthenga Wabwino anaonetsa poyera moyo umene sungafe.
11 내가 이 복음을 위하여 반포자와 사도와 교사로 세우심을 입었노라
Ine ndinasankhidwa kukhala wamthenga, ndi mtumwi ndi mphunzitsi wa Uthenga Wabwinowu.
12 이를 인하여 내가 또 이 고난을 받되 부끄러워하지 아니함은 나의 의뢰한 자를 내가 알고 또한 나의 의탁한 것을 그 날까지 저가 능히 지키실 줄을 확신함이라
Nʼchifukwa chake ndikuvutika monga ndililimu. Komabe zimenezi sizikundichititsa manyazi, popeza ndikumudziwa amene ndamukhulupirira ndipo ndikutsimikiza mtima kuti akhoza kusamalira chimene ndinamusungitsa mpaka tsiku lijalo.
13 너는 그리스도 예수 안에 있는 믿음과 사랑으로써 내게 들은 바 바른 말을 본받아 지키고
Zimene unamva kwa ine, uzisunge kuti zikhale chitsanzo cha chiphunzitso choona, mwa chikhulupiriro ndi chikondi mwa Khristu Yesu.
14 우리 안에 거하시는 성령으로 말미암아 네게 부탁한 아름다운 것을 지키라
Samalira bwino zokoma zimene anakusungitsa. Uzisamalire mothandizidwa ndi Mzimu Woyera amene amakhala mwa ife.
15 아시아에 있는 모든 사람이 나를 버린 이 일을 네가 아나니 그 중에 부겔로와 허모게네가 있느니라
Iwe udziwa kuti onse a mʼchigawo cha Asiya anandithawa, kuphatikizapo Fugelo ndi Herimogene omwe.
16 원컨대 주께서 오네시보로의 집에 긍휼을 베푸시옵소서! 저가 나를 자주 유쾌케 하고 나의 사슬에 매인 것을 부끄러워 아니하여
Mulungu achitire chifundo banja lonse la Onesiforo chifukwa ankandisangalatsa kawirikawiri ndipo sankachita nane manyazi ngakhale ndinali womangidwa ndi maunyolo.
17 로마에 있을 때에 나를 부지런히 찾아 만났느니라
Mʼmalo mwake, atangofika ku Roma, anandifunafuna ndipo anandipeza.
18 (원컨대 주께서 저로 하여금 그 날에 주의 긍휼을 얻게 하여 주옵소서) 또 저가 에베소에서 얼만큼 나를 섬긴 것을 네가 잘 아느니라
Ambuye amulole kuti adzalandire chifundo kwa Ambuye pa tsiku lijalo! Ukudziwa bwino momwe iye anandithandizira mʼnjira zosiyanasiyana ku Efeso.

< 디모데후서 1 >