< 열왕기하 12 >

1 예후의 칠년에 요아스가 위에 올라 예루살렘에서 사십년을 치리하니라 그 모친의 이름은 시비아라 브엘세바 사람이더라
Mʼchaka chachisanu ndi chiwiri cha Yehu, Yowasi anakhala mfumu, ndipo analamulira mu Yerusalemu zaka makumi anayi. Amayi ake anali Zibiya wa ku Beeriseba.
2 요아스가 제사장 여호야다의 교훈을 받을 동안에 여호와 보시기에 정직히 행하였으되
Yowasi anachita zolungama pamaso pa Yehova masiku onse amene wansembe Yehoyada ankamulangiza.
3 오직 산당을 제하지 아니하였으므로 백성이 오히려 산당에서 제사하며 분향하였더라
Komabe sanachotse malo opembedzerapo mafano ndipo anthu anapitiriza kupereka nsembe ndi kufukiza lubani ku malo opembedzerako mafanowo.
4 요아스가 제사장들에게 이르되 무릇 여호와의 전에 거룩하게 하여 드리는 은 곧 사람의 통용하는 은이나 각 사람의 몸값으로 드리는 은이나 자원하여 여호와의 전에 드리는 모든 은을
Yowasi anati kwa ansembe, “Tolerani ndalama zonse zimene zimaperekedwa monga chopereka chopatulika ku Nyumba ya Yehova, ndalama zonse zamsonkho wa munthu aliyense, ndalama zomwe munthu amapereka akalonjeza ndiponso ndalama zimene munthu amapereka mwaufulu ku Nyumba ya Yehova.
5 제사장들이 각각 아는 자에게서 받아 들여서 전의 어느 곳이든지 퇴락한 것을 보거든 그것으로 수리하라 하였더니
Wansembe aliyense alandire ndalamazo kuchokera kwa abwenzi ake, ndipo zigwiritsidwe ntchito yokonzera chilichonse chimene chipezeke kuti ndi chowonongeka mʼnyumbayo.”
6 요아스왕 이십 삼년에 이르도록 제사장들이 오히려 전의 퇴락한데를 수리하지 아니하였는지라
Koma pofika chaka cha 23 cha ufumu wa Yowasi, ansembewo anali asanakonze nyumbayo.
7 요아스왕이 대제사장 여호야다와 제사장들을 불러서 이르되 너희가 어찌하여 전의 퇴락한 데를 수리하지 아니하였느냐 이제부터는 너희 아는 사람에게서 은을 받지 말고 저희로 전 퇴락한 데를 위하여 드리게 하라
Choncho Mfumu Yowasi inayitanitsa wansembe Yehoyada ndi ansembe ena ndipo inafunsa kuti, “Chifukwa chiyani simukukonza malo owonongeka a mʼnyumbayi? Musasungenso ndalama zina zochokera kwa abwenzi anu, koma muzipereke kuti akonzere nyumbayi.”
8 제사장들이 다시는 백성에게 은을 받지도 아니하고 전 퇴락한 것을 수리하지도 아니하기로 응락하니라
Ansembe anavomera kuti salandiranso ndalama kuchokera kwa anthu ndipo kuti sindiwo amene ati akonzenso nyumbayo.
9 제사장 여호야다가 한 궤를 취하여 그 뚜껑에 구멍을 뚫어 여호와의 전문 어귀 우편 곧 단 옆에 두매 무릇 여호와의 전에 가져 오는 은을 다 문을 지키는 제사장들이 그 궤에 넣더라
Koma wansembe Yehoyada anatenga bokosi ndipo anabowola chivundikiro chake. Anayika bokosilo pambali pa guwa lansembe, kudzanja lamanja la aliyense amene akulowa mʼNyumba ya Yehovayo. Ansembe amene ankalondera pa khomopo ankaponya mʼbokosi ndalama zonse zimene ankabwera nazo ku nyumba ya Yehova.
10 이에 그 궤 가운데 은이 많은 것을 보면 왕의 서기와 대제사장 이 올라와서 여호와의 전에 있는대로 그 은을 계수하여 봉하고
Nthawi zonse akaona kuti mʼbokosimo muli ndalama zambiri, mlembi wa mfumu ndi mkulu wa ansembe ankabwera ndipo ankawerenga ndalama zomwe anthu ankabwera nazo ku Nyumba ya Yehova ndi kuziyika mʼmatumba.
11 그 달아본 은을 일하는 자 곧 여호와의 전을 맡은 자의 손에 붙이면 저희는 또 여호와의 전을 수리하는 목수와 건축하는 자들에게 주고
Ankati akadziwa kuti ndalamazo zilipo zingati, ankazipereka kwa anthu amene ankayangʼanira ntchito yokonza nyumbayo. Ndalamazo ankalipira anthu amene ankagwira ntchito yokonza Nyumba ya Yehova, amisiri a matabwa ndi amisiri omanga nyumba,
12 또 미장이와 석수에게 주고 또 여호와의 전 퇴락한 데를 수리할 재목과 다듬은 돌을 사게 하며 그 전을 수리할 모든 물건을 위하여 쓰게 하였으되
amisiri a miyala ndiponso anthu ophwanya miyala. Iwo ankagula matabwa ndi miyala yosema yokonzera Nyumba ya Yehova ndipo ankalipira zinthu zonse zofunika pokonzanso nyumbayo.
13 여호와의 전에 드린 그 은으로 그 전의 은대접이나 불집게나 주발이나 나팔이나 아무 금그릇이나 은그릇을 만들지 아니하고
Koma ndalama zomwe anthu ankabwera nazo ku nyumbayo sanagulire siliva wopangira mabeseni, zozimitsira nyale, mbale zowazira magazi, malipenga kapena ziwiya zina zilizonse zagolide kapena zasiliva za ku Nyumba ya Yehova.
14 오직 그 은을 일하는 자에게 주어 그것으로 여호와의 전을 수리하게 하였으며
Ndalamazi anazipereka kwa anthu antchito amene anazigwiritsa ntchito yokonzera nyumbayo.
15 또 그 은을 받아 일군에게 주는 사람들과 회계하지 아니하였으니 이는 성실히 일을 하였음이라
Koma sanawafunse kuti afotokoze kagwiritsidwe ntchito ka ndalama zolipira amene ankagwira ntchito, chifukwa anthuwo ankagwira ntchitoyo mokhulupirika kwambiri.
16 속건제의 은과 속죄제의 은은 여호와의 전에 드리지 아니하고 제사장에게 돌렸더라
Ndalama zomwe zinkaperekedwa pa nsembe yopepesera machimo ndi nsembe yoperekedwa chifukwa cha tchimo sanabwere nazo ku Nyumba ya Yehova pakuti zinali za ansembe.
17 때에 아람 왕 하사엘이 올라와서 가드를 쳐서 취하고 예루살렘을 향하여 올라오고자 한고로
Pa nthawi imeneyo, Hazaeli, mfumu ya Aramu anapita kukathira nkhondo mzinda wa Gati nawulanda. Kenaka Hazaeli anatembenuka kupita kukathira nkhondo mzinda wa Yerusalemu.
18 유다 왕 요아스가 그 열조 유다 왕 여호사밧과 여호람과 아하시야가 구별하여 드린 모든 성물과 자기가 구별하여 드린 성물과 여호와의 전 곳간과 왕궁에 있는 금을 다 취하여 아람 왕 하사엘에게 보내었더니 하사엘이 예루살렘에서 떠나갔더라
Koma Yowasi mfumu ya Yuda anatenga zinthu zonse zopatulika zomwe anazipatula Yehosafati, Yehoramu, ndi Ahaziya abambo ake, mafumu a Yuda ndi mphatso zonse zomwe iye mwini anazipereka: golide yense amene anapezeka mʼnyumba yosungiramo chuma cha mʼnyumba ya Yehova ndi zomwe zinali mʼnyumba ya mfumu, nazipereka kwa Hazaeli mfumu ya Aramu. Pamenepo iye anachoka ku Yerusalemuko.
19 요아스의 남은 사적과 그 모든 행한 것은 유다 왕 역대지략에 기록되지 아니하였느냐
Ndipo ntchito zina za Yowasi ndi zonse zimene anachita, kodi sizinalembedwe mʼbuku la mbiri ya mafumu a Yuda?
20 요아스의 신복들이 일어나서 모반하여 실라로 내려가는 길 가의 밀로궁에서 저를 죽였고
Akuluakulu ake anamuchitira chiwembu ndi kumupha ku Beti Milo, pa njira yotsikira ku Silo.
21 저를 쳐서 죽인 신복은 시므앗의 아들 요사갈과 소멜의 아들 여호사바드이었더라 저는 다윗 성에 그 열조와 함께 장사되고 그 아들 아마샤가 대신하여 왕이 되니라
Yozakara mwana wa Simeati ndi Yehozabadi mwana wa Someri atumiki ake anamukantha nafa. Ndipo anamuyika mʼmanda pamodzi ndi makolo ake mu Mzinda wa Davide. Ndipo Amaziya mwana wake analowa ufumu mʼmalo mwake.

< 열왕기하 12 >