< 역대하 6 >

1 그때에 솔로몬이 가로되 여호와께서 캄캄한데 계시겠다 말씀하셨사오나
Pamenepo Solomoni anati, “Yehova anati adzakhala mʼmitambo yakuda;
2 내가 주를 위하여 거하실 전을 건축하였사오니 주께서 영원히 거하실 처소로소이다 하고
ine ndakumangirani Nyumba yokongola kwambiri, malo woti muzikhalamo mpaka muyaya.”
3 얼굴을 돌이켜 이스라엘의 온 회중을 위하여 축복하니 때에 이스라엘의 온 회중이 서 있더라
Aisraeli onse ali chiyimire pomwepo, mfumu inatembenuka ndi kuwadalitsa.
4 왕이 가로되 이스라엘 하나님 여호와를 송축할지로다 여호와께서 그 입으로 나의 부친 다윗에게 말씀하신 것을 이제 그 손으로 이루셨도다 이르시기를
Ndipo inati, “Atamandike Yehova, Mulungu wa Israeli amene wachita ndi dzanja lake zimene analonjeza ndi pakamwa pake kwa Davide abambo anga. Pakuti Iye anati,
5 내가 내 백성을 애굽 땅에서 인도하여 낸 날부터 내 이름을 둘 만한 집을 건축하기 위하여 이스라엘 모든 지파 가운데서 아무 성읍도 택하지 아니하였으며 내 백성 이스라엘의 주권자를 삼기 위하여 아무 사람도 택하지 아니하였더니
‘Kuyambira tsiku limene ndinatulutsa anthu anga ku Igupto, sindinasankhe mzinda wina uliwonse pa fuko lina lililonse la Aisraeli kuti kumeneko andimangire Nyumba kuti ndizikhalamo kapena munthu wina aliyense kuti akhale mtsogoleri wa Aisraeli anthu anga.
6 예루살렘을 택하여 내 이름을 거기 두고 또 다윗을 택하여 내 백성 이스라엘을 다스리게 하였노라 하신지라
Koma tsopano ndasankha Yerusalemu kuti Dzina langa likhale kumeneko ndiponso ndasankha Davide kuti alamulire anthu anga Aisraeli.’
7 내 부친 다윗이 이스라엘 하나님 여호와의 이름을 위하여 전을 건축할 마음이 있었더니
“Abambo anga Davide anali ndi maganizo mu mtima mwawo oti amangire Nyumba Yehova Mulungu wa Israeli.
8 여호와께서 내 부친 다윗에게 이르시되 네가 내 이름을 위하여 전을 건축할 마음이 있으니 이 마음이 네게 있는 것이 좋도다
Koma Yehova ananena kwa abambo anga Davide kuti, ‘Popeza zinali mu mtima mwako kumangira Nyumba dzina langa, unachita bwino kukhala ndi maganizo amenewa mu mtima mwakomo.
9 그러나 너는 그 전을 건축하지 못할 것이요 네 몸에서 낳을 네 아들 그가 내 이름을 위하여 전을 건축하리라 하시더니
Komatu si iwe amene udzamanga Nyumba ya Mulungu koma mwana wako, mwana amene iwe udzabereke. Iyeyo ndiye amene adzandimangire Nyumba.’
10 이제 여호와께서 말씀하신 대로 이루시도다 내가 여호와의 허하신 대로 내 부친 다윗을 대신하여 일어나서 이스라엘 위에 앉고 이스라엘 하나님 여호와의 이름을 위하여 전을 건축하고
“Yehova wasunga zimene analonjeza. Ine ndalowa mʼmalo mwa abambo anga Davide, ndipo tsopano ndili pa mpando waufumu wa Israeli, monga momwe Yehova analonjezera, ndipo ndamangira nyumba Dzina la Yehova Mulungu wa Israeli.
11 내가 또 그 곳에 여호와께서 이스라엘 자손으로 더불어 세우신 언약 넣은 궤를 두었노라
Mʼmenemo ndayikamo Bokosi la Chipangano, mmene muli pangano la Yehova limene anapangana ndi ana a Israeli.”
12 솔로몬이 여호와의 단 앞에서 이스라엘의 회중을 마주 서서 그 손을 펴니라
Pamenepo Solomoni anayimirira patsogolo pa guwa lansembe la Yehova patsogolo pa gulu lonse la Aisraeli ndipo anakweza manja ake.
13 솔로몬이 이왕에 놋으로 대를 만들었으니 장이 다섯 규빗이요 광이 다섯 규빗이요 고가 세 규빗이라 뜰 가운데 두었더니 저가 그위에 서서 이스라엘의 회중앞에서 무릎을 꿇고 하늘을 향하여 손을 펴고
Iyeyo anali atapanga nsanja yamkuwa, kutalika kwake kunali mamita awiri, mulifupi mwake munali mamita awiri, msinkhu wake unali mita imodzi ndi theka ndipo nsanjayo anayimika pakati pa bwalo lakunja. Iye anayimirira pa nsanjapo nagwada pamaso pa gulu lonse la Aisraeli ndipo anakweza manja ake kumwamba.
14 가로되 이스라엘 하나님 여호와여, 천지에 주와 같은 신이 없나이다 주께서는 온 마음으로 주의 앞에서 행하는 주의 종들에게 언약을 지키시고 은혜를 베푸시나이다
Iye anati, “Inu Yehova, Mulungu wa Israeli, palibe Mulungu wofanana nanu kumwamba kapena pa dziko. Inu amene mumasunga pangano ndi kuonetsa chikondi chosasinthika kwa atumiki anu amene amayenda pamaso panu ndi mtima wawo wonse.
15 주께서 주의 종 내 아비 다윗에게 허하신 말씀을 지키시되 주의 입으로 말씀하신 것을 손으로 이루심이 오늘날과 같으니이다
Inu mwasunga lonjezo lanu kwa abambo anga Davide, mtumiki wanu. Inde zimene munalonjeza ndi pakamwa panu, mwazikwaniritsa ndi manja anu monga mmene tikuonera lero lino.
16 이스라엘 하나님 여호와여, 주께서 주의 종 내 아비 다윗에게 말씀하시기를 네 자손이 자기 길을 삼가서 네가 내 앞에서 행한 것같이 내 율법대로 행하기만 하면 네게로 좇아 나서 이스라엘 위에 앉을 사람이 내 앞에서 끊어지지 아니하리라 하셨사오니 이제 다윗을 위하여 그 허하신 말씀을 지키시옵소서
“Ndipo tsopano, Inu Yehova Mulungu wa Israeli, sungani zimene munalonjeza kwa abambo anga Davide, mtumiki wanu pamene munati, ‘Sudzasowa munthu wokhala pamaso panga pa mpando waufumu wa Israeli, ngati ana ako adzasamalira mayendedwe awo ndi kusunga malamulo anga monga iwe wachitira.’
17 그런즉 이스라엘 하나님 여호와여, 원컨대 주는 주의 종 다윗에게 하신 말씀이 확실하게 하옵소서
Ndipo tsopano Inu Yehova, Mulungu wa Israeli, lolani kuti mawu anu akwaniritsidwe amene munalonjeza mtumiki wanu Davide.
18 하나님이 참으로 사람과 함께 땅에 거하시리이까 하늘과 하늘들의 하늘이라도 주를 용납지 못하겠거든 하물며 내가 건축한 이 전이오리이까
“Kodi Mulungu angakhaledi pa dziko lapansi ndi munthu? Mlengalenga ngakhale kumwamba kwenikweni sikungakukwaneni. Nanga kuli bwanji ndi Nyumba iyi imene ndamanga!
19 그러나 나의 하나님 여호와여, 종의 기도와 간구를 돌아보시며 종이 주의 앞에서 부르짖음과 비는 기도를 들으시옵소서
Koma Inu Yehova, Mulungu wanga, imvani pemphero ndi pembedzero la mtumiki wanu. Imvani kulira ndi pemphero la mtumiki wanu limene ndikupempha pamaso panu.
20 주께서 전에 말씀하시기를 내 이름을 거기 두리라 하신 곳 이 전을 향하여 주의 눈이 주야로 보옵시며 종이 이 곳을 향하여 비는 기도를 들으시옵소서
Maso anu azikhala otsekuka kuyangʼana Nyumba ino usana ndi usiku, malo ano amene Inu munati mudzayikamo Dzina lanu, imvani pemphero la mtumiki wanu limene akupemphera pa malo ano.
21 종과 주의 백성 이스라엘이 이곳을 향하여 기도할때에 주는 그 간구함을 들으시되 주의 계신 곳 하늘에서 들으시고 들으시사 사하여 주옵소서
Imvani mapembedzero a mtumiki wanu ndi a anthu anu Aisraeli pamene akupemphera akuyangʼana malo ano. Imvani kumwambako, malo anu amene mumakhala; ndipo mukamva muzitikhululukira.
22 만일 어떤 사람이 그 이웃에게 범죄하므로 맹세시킴을 받고 저가 와서 이 전에 있는 주의 단 앞에서 맹세하거든
“Munthu akalakwira mnzake, nawuzidwa kuti alumbire, akabwera kudzalumbira patsogolo pa guwa lansembe la Nyumba ino,
23 주는 하늘에서 들으시고 행하시되 주의 종들을 국문하사 악한 자의 죄를 정하여 그 행위대로 그 머리에 돌리시고 의로운 자를 의롭다 하사 그 의로운 대로 갚으시옵소서
imvani kumwambako ndi kuchitapo kanthu. Weruzani atumiki anuwo, wochimwa mugamule kuti ndi wolakwa ndipo alangidwe chifukwa cha zimene wachita. Wosachimwa mugamule kuti wosalakwa, ndipo muonetse kusalakwa kwakeko.
24 만일 주의 백성 이스라엘이 주께 범죄하여 적국 앞에 패하게 되므로 주께로 돌아와서 주의 이름을 인정하고 이 전에서 주께 빌며 간구하거든
“Anthu anu Aisraeli akagonja kwa adani awo chifukwa akuchimwirani ndipo akatembenukira kwa Inu ndi kuvomereza Dzina lanu, kupemphera ndi kupembedzera pamaso panu mʼNyumba ino,
25 주는 하늘에서 들으시고 주의 백성 이스라엘의 죄를 사하시고 그와 그 열조에게 주신 땅으로 돌아오게 하옵소서
pamenepo imvani kumwambako ndi kukhululukira tchimo la anthu anu Aisraeli ndi kuwabweretsa ku dziko limene munawapatsa iwo ndi makolo awo.
26 만일 저희가 주께 범죄함을 인하여 하늘이 닫히고 비가 없어서 주의 벌을 받을 때에 이 곳을 향하여 빌며 주의 이름을 인정하고 그 죄에서 떠나거든
“Pamene kumwamba kwatsekeka ndipo mvula sikugwa chifukwa anthu anu akuchimwirani, ndipo pamene apemphera akuyangʼana malo ano ndi kuvomereza Dzina lanu ndi kutembenuka kuchoka ku machimo awo chifukwa inu mwawalanga,
27 주는 하늘에서 들으사 주의 종들과 주의 백성 이스라엘의 죄를 사하시고 그 마땅히 행할 선한 길을 가르쳐 주옵시며 주의 백성에게 기업으로 주신 주의 땅에 비를 내리시옵소서
pamenepo imvani kumwambako ndipo muwakhululukire atumiki anu, anthu anu Aisraeli. Aphunzitseni makhalidwe oyenera, ndipo gwetsani mvula mʼdziko limene munapereka kwa anthu anu monga cholowa chawo.
28 만일 이 땅에 기근이나 온역이 있거나 곡식이 시들거나 깜부기가 나거나 메뚜기나 황충이 나거나 적국이 와서 성읍을 에워 싸거나 무슨 재앙이나 무슨 질병이 있든지 무론하고
“Pamene mʼdziko mwagwa njala kapena mliri, chinoni kapena chiwawu, dzombe kapena kapuchi, kapena pamene adani azungulira mzinda wawo wina uliwonse, kaya mavuto kapena matenda abwera,
29 한 사람이나 혹 주의 온 백성 이스라엘이 다 각각 자기의 마음에 재앙과 고통을 깨닫고 이 전을 향하여 손을 펴고 무슨 기도나 무슨 간구를 하거든
ndipo wina aliyense mwa Aisraeli akapemphera kapena kukudandaulirani, aliyense wa iwo akadziwa masautso ake ndi ululu wake, ndi kukweza manja awo kuloza Nyumba ino,
30 주는 계신 곳 하늘에서 들으시며 사유하시되 각 사람의 마음을 아시오니 그 모든 행위대로 갚으시옵소서 주만 홀로 인생의 마음을 아심이니이다
pamenepo imvani kumwambako, malo anu wokhalamo. Khululukani ndipo muchitire aliyense molingana ndi zonse zimene anachita popeza Inu mumadziwa mtima wake, (pakuti ndinu nokha amene mumadziwa mitima ya anthu),
31 그리하시면 저희가 주께서 우리 열조에게 주신 땅에서 사는 동안에 항상 주를 경외하며 주의 길로 행하리이다
motero iwo adzakuopani ndipo adzayenda mʼnjira zanu masiku onse amene adzakhale mʼdziko limene munalipereka kwa makolo athu.
32 주의 백성 이스라엘에 속하지 않은 이방인에게 대하여도 저희가 주의 큰 이름과 능한 손과 펴신 팔을 위하여 먼 지방에서 와서 이 전을 향하여 기도하거든
“Ndipo kunena za mlendo amene si mmodzi wa anthu anu Aisraeli, koma wabwera kuchokera ku dziko lakutali chifukwa cha dzina lanu lotchukali, ndiponso za dzanja lanu lamphamvu ndi lochita zazikulu, kudzapemphera akuyangʼana Nyumba ino,
33 주는 계신 곳 하늘에서 들으시고 무릇 이방인이 주께 부르짖는 대로 이루사 땅의 만민으로 주의 이름을 알고 주의 백성 이스라엘처럼 경외하게 하옵시며 또 내가 건축한 이 전을 주의 이름으로 일컫는 줄을 알게 하옵소서
pamenepo imvani kumwambako, malo anu okhalamo, ndipo muchite zonse zimene mlendoyo akukupemphani, kotero kuti anthu onse a dziko lapansi adziwe dzina lanu ndi kukuopani monga amachitira anthu anu Aisraeli, ndipo adziwe kuti nyumba ino imene ndakumangirani imadziwika ndi dzina lanu.
34 주의 백성이 그 적국으로 더불어 싸우고자 하여 주의 보내신 길로 나갈때에 저희가 주의 빼신 이 성과 내가 주의 이름을 위하여 건축한 전있는 편을 향하여 여호와께 기도하거든
“Anthu akapita ku nkhondo kukamenyana ndi adani awo, kulikonse kumene mungawatume, ndipo akapemphera moyangʼana mzinda uno umene mwausankha ndi Nyumba yanu imene ndakumangirani,
35 주는 하늘에서 저희의 기도와 간구를 들으시고 그 일을 돌아보옵소서
pamenepo imvani kumwamba pemphero lawo ndi kupempha kwawo ndipo muwapulumutse.
36 범죄치 아니하는 사람이 없사오니 저희가 주께 범죄하므로 주께서 저희에게 진노하사 저희를 적국에게 붙이시매 적국이 저희를 사로잡아 땅의 원근을 물론하고 끌어간 후에
“Pamene achimwira inu, pakuti palibe amene sachimwa, ndipo inu mwawakwiyira ndi kuwapereka kwa adani awo, amene awatenga ukapolo ku dziko lawo lakutali kapena pafupi.
37 저희가 사로잡혀 간 땅에서 스스로 깨닫고 그 사로잡은 자의 땅에서 돌이켜 주께 간구하기를 우리가 범죄하여 패역을 행하며 악을 지었나이다 하며
Ngati asintha mitima yawo ku dziko limene ali akapolo ndi kulapa ndi kukudandaulirani inu mʼdziko la ukapolo wawo ndi kunena kuti, ‘Ife tachimwa, tachita zolakwa ndipo tachita moyipa kwambiri.’
38 자기를 사로잡아 간 적국의 땅에서 온 마음과 온 뜻으로 주께 돌아와서 주께서 그 열조에게 주신 땅과 주의 빼신 성과 내가 주의 이름을 위하여 건축한 전 있는 편을 향하여 기도하거든
Ndipo ngati atembenukira kwa inu ndi mtima ndi moyo wawo wonse mʼdziko lawo la ukapolo kumene anatengedwako ndi kupemphera moyangʼana dziko limene inu munalipereka kwa makolo awo, moyangʼana Nyumba yanu imene ndakumangirani;
39 주는 계신 곳 하늘에서 저희의 기도와 간구를 들으시고 저희의 일을 돌아보옵시며 주께 득죄한 주의 백성을 용서하옵소서
pamenepo imvani kumwamba, malo anu okhala, pemphero lawo ndi kudandaula kwawo, ndipo muwapulumutse. Ndipo mukhululukire anthu anu, amene akuchimwirani.
40 나의 하나님이여, 이제 이곳에서 하는 기도에 눈을 드시고 귀를 기울이소서
“Tsono Inu Mulungu wanga, tsekulani maso anu ndi makutu anu kuti mumve mapemphero ochitikira pa malo ano.
41 여호와 하나님이여, 일어나 들어가사 주의 능력의 궤와 함께 주의 평안한 처소에 계시옵소서 여호와 하나님이여 원컨대 주의 제사장으로 구원을 입게 하시고 또 주의 성도로 은혜를 기뻐하게 하옵소서
“Tsopano dzukani Inu Yehova Mulungu, ndipo bwerani ku malo anu ampumulo,
42 여호와 하나님이여, 주의 기름부음 받은 자에게서 얼굴을 돌이키지 마옵시고 주의 종 다윗에게 베푸신 은총을 기억하옵소서
Inu Yehova Mulungu musamukane wodzozedwa wanu.

< 역대하 6 >