< 역대상 3 >

1 다윗이 헤브론에서 낳은 아들들이 이러하니 맏아들은 압논이라 이스르엘 여인 아히노암의 소생이요 둘째는 다니엘이라 갈멜 여인 아비가일의 소생이요
Ana aamuna a Davide amene anabadwira ku Hebroni anali awa: Woyamba anali Amnoni, amayi ake anali Ahinoamu wa ku Yezireeli; wachiwiri anali Danieli, amayi ake anali Abigayeli wa ku Karimeli;
2 세째는 압살롬이라 그술 왕 달매의 딸 마아가의 아들이요 네째는 아도니야라 학깃의 아들이요
wachitatu anali Abisalomu, mwana wa Maaka mwana wa Talimai mfumu ya Gesuri; wachinayi anali Adoniya amayi ake anali Hagiti;
3 다섯째는 스바댜라 아비달의 소생이요, 여섯째는 이드르암이라 다윗의 아내 에글라의 소생이니
wachisanu anali Sefatiya, amayi ake anali Abitali; wachisanu ndi chimodzi anali Itireamu, amayi ake anali Egila.
4 이 여섯은 다윗이 헤브론에서 낳은 자라 다윗이 거기서 칠년 육개월을 치리하였고 또 예루살렘에서 삼십 삼년을 치리하였으며
Ana asanu ndi mmodzi awa a Davide anabadwira ku Hebroni kumene analamulirako zaka zisanu ndi ziwiri ndi miyezi isanu ndi umodzi. Davide analamuliranso mu Yerusalemu kwa zaka 33,
5 예루살렘에서 낳은 아들들은 이러하니 시므아와, 소밥과, 나단과, 솔로몬 네 사람은 다 암미엘의 딸 밧수아의 소생이요
ndipo ana amene anabadwira ku Yerusalemuko anali awa: Samua, Sobabu, Natani ndi Solomoni. Ana anayi awa anali a Batisuwa mwana wa Amieli.
6 또 입할과, 엘리사마와, 엘리벨렛과
Anaberekanso Ibihari, Elisua, Elipeleti,
7 노가와, 네벡과, 야비야와
Noga, Nefegi, Yafiya,
8 엘리사마와, 엘랴다와, 엘리벨렛 아홉 사람은
Elisama, Eliada ndi Elifeleti, onse analipo asanu ndi anayi.
9 다 다윗의 아들이요 저희의 누이는 다말이며 이 외에 또 첩의 아들이 있었더라
Onsewa anali ana a Davide, osawerengera ana a azikazi. Ndipo mlongo wawo anali Tamara.
10 솔로몬의 아들은 르호보암이요, 그 아들은 아비야요, 그 아들은 아사요, 그 아들은 여호사밧이요
Mwana wa Solomoni anali Rehabiamu, Rehabiamu anabereka Abiya, Abiya anabereka Asa, Asa anabereka Yehosafati,
11 그 아들은 요람이요, 그 아들은 아하시야요, 그 아들은 요아스요
Yehosafati anabereka Yehoramu, Yehoramu anabereka Ahaziya, Ahaziya anabereka Yowasi,
12 그 아들은 아마샤요, 그 아들은 아사랴요, 그 아들은 요담이요
Yowasi anabereka Amaziya, Amaziya anabereka Azariya, Azariya anabereka Yotamu,
13 그 아들은 아하스요, 그 아들은 히스기야요, 그 아들은 므낫세요
Yotamu anabereka Ahazi, Ahazi anabereka Hezekiya, Hezekiya anabereka Manase,
14 그 아들은 아몬이요, 그 아들은 요시야며
Manase anabereka Amoni, Amoni anabereka Yosiya.
15 요시야의 아들들은 맏아들 요하난과 둘째 여호야김과 세째 시드기야와 네째 살룸이요
Ana a Yosiya anali awa: Yohanani mwana wake woyamba, Yehoyakimu mwana wake wachiwiri, Zedekiya mwana wake wachitatu, Salumu mwana wake wachinayi.
16 여호야김의 아들들은 그 아들 여고냐 그 아들 시드기야요
Ana a Yehoyakimu: Yekoniya ndi Zedekiya mwana wake.
17 사로잡혀 간 여고냐의 아들들은 그 아들 스알디엘과
Zidzukulu za Yekoniya wa mʼndende zinali izi: mwana wake Silatieli,
18 말기람과, 브다야와, 세낫살과, 여가먀와, 호사마와, 느다뱌요
Malikiramu, Pedaya, Senazara, Yekamiya, Hosama ndi Nedabiya.
19 브다야의 아들들은 스룹바벨과, 시므이요 스룹바벨의 아들은 므술람과, 하나냐와, 그 매제 슬로밋과
Ana a Pedaya anali awa: Zerubabeli ndi Simei. Ana a Zerubabeli anali awa: Mesulamu ndi Hananiya. Mlongo wawo anali Selomiti.
20 또 하수바와, 오헬과, 베레갸와, 하사댜와, 유삽헤셋 다섯 사람이요
Panalinso ana ena asanu awa: Hasubu, Oheli, Berekiya, Hasabiya ndi Yusabu-Hesedi.
21 하나냐의 아들은 블라댜와, 여사야요, 또 르바야의 아들 아르난의 아들들, 오바댜의 아들들, 스가냐의 아들들이니
Zidzukulu za Hananiya zinali izi: Pelatiya ndi Yesaiya, ndiponso ana a Refaya, ana a Arinani, ana a Obadiya ndi ana a Sekaniya.
22 스가냐의 아들은 스마야요, 스마야의 아들들은 핫두스와, 이갈과, 바리야와, 느아랴와, 사밧 여섯 사람이요
Zidzukulu za Sekaniya zinali izi: Semaya ndi ana ake: Hatusi, Igala, Bariya, Neariya ndi Safati. Onse anali asanu ndi mmodzi.
23 느아랴의 아들은 엘료에내와, 히스기야와, 아스리감 세 사람이요
Ana a Neariya anali awa: Eliyoenai, Hezekiya ndi Azirikamu. Onse anali atatu.
24 엘료에내의 아들들은 호다위야와, 엘리아십과, 블라야와, 악굽과, 요하난과, 들라야와, 아나니 일곱 사람이더라
Ana a Eliyoenai: Hodaviya, Eliyasibu, Pelaya, Akubu, Yohanani, Delaya ndi Anani, onse anali asanu ndi awiri.

< 역대상 3 >