< 시편 127 >
1 (솔로몬의 시. 곧 성전에 올라가는 노래) 여호와께서 집을 세우지 아니하시면 세우는 자의 수고가 헛되며 여호와께서 성을 지키지 아니하시면 파숫군의 경성함이 허사로다
Nyimbo yoyimba pokwera ku Yerusalemu. Salimo la Solomoni. Yehova akapanda kumanga nyumba, omanga nyumbayo agwira ntchito pachabe. Yehova akapanda kulondera mzinda, mlonda akanangolondera pachabe.
2 너희가 일찌기 일어나고 늦게 누우며 수고의 떡을 먹음이 헛되도다 그러므로 여호와께서 그 사랑하시는 자에게는 잠을 주시는도다
Mumangodzivuta nʼkulawirira mmamawa ndi kusagona msanga madzulo, kuvutikira chakudya choti mudye, pakuti Iye amapereka tulo kwa amene amawakonda.
3 자식은 여호와의 주신 기업이요 태의 열매는 그의 상급이로다
Ana ndiye cholowa chochokera kwa Yehova, ana ndi mphotho yochokera kwa Iye.
4 젊은 자의 자식은 장사의 수중의 화살 같으니
Ana a pa unyamata ali ngati mivi mʼmanja mwa munthu wankhondo.
5 이것이 그 전통에 가득한 자는 복되도다 저희가 성문에서 그 원수와 말할 때에 수치를 당치 아니하리로다
Wodala munthu amene motengera mivi mwake mwadzaza. Iwo sadzachititsidwa manyazi pamene alimbana ndi adani awo pa zipata.