< 욥기 40 >
2 변박하는 자가 전능자와 다투겠느냐? 하나님과 변론하는 자는 대답할지니라
“Kodi iwe ufuna kukangana ndi Wamphamvuzonse? Iwe amene unatsutsana ndi Mulungu umuyankhe Iyeyo!”
Pamenepo Yobu anayankha Yehova:
4 나는 미천하오니 무엇이라 주께 대답하리이까 손으로 내 입을 가릴 뿐이로소이다
“Ine sindili kanthu konse, kodi ndingathe kukuyankhani chiyani? Ndagwira pakamwa panga.
5 내가 한두번 말하였사온즉 다시는 더하지도 아니하겠고 대답지도 아니하겠나이다
Ndinayankhula kamodzi, koma pano ndilibe yankho, ndinayankha kawiri, koma sindiwonjezeranso mawu ena.”
6 여호와께서 폭풍 가운데서 욥에게 말씀하여 가라사대
Ndipo Yehova anayankha Yobu mʼkamvuluvulu kuti,
7 너는 대장부처럼 허리를 묶고 내가 네게 묻는 것을 대답할지니라
“Tsopano vala dzilimbe ngati mwamuna; ndikufunsa mafunso ndipo iwe undiyankhe.
8 네가 내 심판을 폐하려느냐? 스스로 의롭다 하려 하여 나를 불의하다 하느냐?
“Kodi iwe unganyoze chiweruzo changa cholungama? Kodi ungandidzudzule kuti iweyo ukhale wolungama?
9 네가 하나님처럼 팔이 있느냐? 하나님처럼 우렁차게 울리는 소리를 내겠느냐?
Kodi uli ndi dzanja monga la Mulungu, ndipo mawu ako angagunde ngati mphenzi monga a Mulungu?
10 너는 위엄과 존귀로 스스로 꾸미며 영광과 화미를 스스로 입을지니라
Ngati zili choncho udzikometsere ndi ulemerero ndi kukongola, ndipo udziveke ulemu ndi ulemerero waufumu.
11 너의 넘치는 노를 쏟아서 교만한 자를 발견하여 낱낱이 낮추되
Tsanula ukali wako wosefukirawo, uyangʼane aliyense wodzikuza ndipo umuchepetse,
12 곧 모든 교만한 자를 발견하여 낮추며 악인을 그 처소에서 밟아서
Uyangʼane aliyense wodzikweza ndipo umutsitse, uwapondereze oyipa onse pamalo pomwe alilipo.
13 그들을 함께 진토에 묻고 그 얼굴을 싸서 어둑한 곳에 둘지니라
Onsewo uwakwirire pamodzi mfumbi; ukulunge nkhope zawo mʼmanda.
14 그리하면 네 오른손이 너를 구원할 수 있다고 내가 인정하리라
Ukatero Ine ndidzakuvomereza kuti dzanja lako lamanja lakupulumutsadi.
15 이제 소 같이 풀을 먹는 하마를 볼지어다 내가 너를 지은 것 같이 그것도 지었느니라
“Taganiza za mvuwu, imene ndinayipanga monga momwe ndinapangira iwe, ndipo imadya udzu ngati ngʼombe.
16 그 힘은 허리에 있고 그 세력은 배의 힘줄에 있고
Mphamvu zake ndi zazikulu kwambiri, thupi lake ndi lanyonga kwambiri!
17 그 꼬리 치는 것은 백향목이 흔들리는 것 같고 그 넓적다리 힘줄은 서로 연락되었으며
Mchira wake umayima tolotolo ngati mtengo wamkungudza; mitsempha ya ntchafu zake ndi yogwirana bwino.
18 그 뼈는 놋관 같고 그 가릿대는 철장 같으니
Mafupa ake ali ngati mapayipi amkuwa, nthiti zake zili ngati mipiringidzo yachitsulo.
19 그것은 하나님의 창조물 중에 으뜸이라 그것을 지은 자가 칼을 주었고
Mvuwuyo ndi yayikulu mwa zolengedwa za Mulungu, komatu mlengi wake amatha kuyiopseza ndi lupanga lake.
20 모든 들 짐승의 노는 산은 그것을 위하여 식물을 내느니라
Imapeza chakudya chake ku mtunda ndipo nyama zakuthengo zonse zimasewera pambali pake.
21 그것이 연 줄기 아래나 갈 밭 가운데나 못속에 엎드리니
Imagona pa tsinde pa zitsamba za mipeta, imabisala mʼbango ndiponso pa thawale.
Imaphimbika ndi mthunzi wazitsamba za mipeta; imazunguliridwa ndi misondozi ya mu mtsinje.
23 하수가 창일한다 할지라도 그것이 놀라지 않고 요단강이 불어 그 입에 미칠지라도 자약하니
Madzi a mu mtsinje akakokoma, sichita mantha, iyo sitekeseka, ngakhale madzi a mu Yorodani afike mʼkhosi mwake.
24 그것이 정신 차리고 있을 때에 누가 능히 잡을 수 있겠으며 갈고리로 그 코를 꿸 수 있겠느냐?
Kodi alipo amene angathe kukola mvuwu ndi mbedza kapena kuyikola mu msampha?