< 사도행전 22 >
1 부형들아 내가 지금 너희 앞에서 변명하는 말을 들으라 하더라
Iye anati, “Inu abale anga ndi makolo anga, tamvani mawu akudziteteza kwanga.”
2 저희가 그 히브리 방언으로 말함을 듣고 더욱 종용한지라 이어 가로되
Atamva iye akuyankhula Chihebri, anakhala chete. Kenaka Paulo anati,
3 나는 유대인으로 길리기아 다소에서 났고 이 성에서 자라 가말리엘의 문하에서 우리 조상들의 율법의 엄한 교훈을 받았고 오늘 너희 모든 사람처럼 하나님께 대하여 열심하는 자라
“Ine ndine Myuda, wobadwira ku Tarisisi wa ku Kilikiya, koma ndinaleredwa mu mzinda muno, ndinaphunzitsidwa mwatsatanetsatane kusunga malamulo a makolo athu ndi Gamalieli ndipo ndinali wodzipereka pa za Mulungu monga mmene inu mulili lero.
4 내가 이 도를 핍박하여 사람을 죽이기까지 하고 남녀를 결박하여 옥에 넘겼노니
Ine ndinkazunza anthu otsatira Njirayi mpaka kuwapha. Ndinkagwira amuna ndi amayi ndi kuwayika mʼndende.
5 이에 대제사장과 모든 장로들이 내 증인이라 또 내가 저희에게서 다메섹 형제들에게 가는 공문을 받아 가지고 거기 있는 자들도 결박하여 예루살렘으로 끌어다가 형벌 받게 하려고 가더니
Mkulu wa ansembe ndiponso akuluakulu a Ayuda angathe kundichitira umboni. Iwowa anandipatsa makalata opita nawo kwa abale awo ku Damasiko. Ndipo ndinapita kumeneko kuti ndikawagwire anthu amenewa ndi kubwera nawo ku Yerusalemu kuti adzalangidwe.
6 가는데 다메섹에 가까왔을 때에 오정쯤 되어 홀연히 하늘로서 큰 빛이 나를 둘러 비취매
“Nthawi ya masana, nditayandikira ku Damasiko, mwadzidzidzi kuwala kwakukulu kochokera kumwamba kunandizungulira.
7 내가 땅에 엎드러져 들으니 소리 있어 가로되 사울아 사울아 네가 왜 나를 핍박하느냐 하시거늘
Ndinagwa pansi ndipo ndinamva mawu akuti, ‘Saulo! Saulo! Ukundizunziranji?’”
8 내가 대답하되 주여 뉘시니이까? 하니 가라사대 나는 네가 핍박하는 나사렛 예수라 하시더라
Ine ndinafunsa kuti, “Ndinu ndani Ambuye?” Iye anayankha kuti, “Ndine Yesu wa ku Nazareti, amene iwe ukumuzunza.”
9 나와 함께 있는 사람들이 빛은 보면서도 나더러 말하시는 이의 소리는 듣지 못하더라
Anzanga a paulendo anaona kuwalako, koma sanamve mawuwo, a Iye amene amayankhula nane.
10 내가 가로되 주여 무엇을 하리이까? 주께서 가라사대 일어나 다메섹으로 들어가라 정한 바 너희 모든 행할 것을 거기서 누가 이르리라 하시거늘
Ine ndinafunsa kuti, “Kodi ndichite chiyani Ambuye?” Ambuye anati, “Imirira ndipo pita ku Damasiko. Kumeneko adzakuwuza zonse zimene ukuyenera kuchita.”
11 나는 그 빛의 광채를 인하여 볼 수 없게 되었으므로 나와 함께 있는 사람들의 손에 끌려 다메섹에 들어갔노라
Anzanga anandigwira dzanja kupita nane ku Damasiko, popeza kuwala kunja kunandichititsa khungu.
12 율법에 의하면 경건한 사람으로 거기 사는 모든 유대인들에게 칭찬을 듣는 아나니아라 하는 이가
“Munthu wina dzina lake Hananiya anabwera kudzandiona. Iyeyu anali munthu woopa Mulungu ndi wosunga Malamulo. Ayuda onse okhala kumeneko amamupatsa ulemu waukulu.
13 내게 와 곁에 서서 말하되 형제 사울아 다시 보라 하거늘 즉시 그를 쳐다보았노라
Iye anayimirira pafupi nane nati, ‘Mʼbale Saulo, penyanso!’ Ndipo nthawi yomweyo ndinapenya ndikumuona iyeyo.
14 그가 또 가로되 우리 조상들의 하나님이 너를 택하여 너로 하여금 자기 뜻을 알게 하시며 저 의인을 보게 하시고 그 입에서 나오는 음성을 듣게 하셨으니
“Ndipo iye anati, ‘Mulungu wa makolo athu wakusankha iwe kuti udziwe chifuniro chake ndi kuona Wolungamayo ndi kumva mawu ochokera pakamwa pake.
15 네가 그를 위하여 모든 사람 앞에서 너의 보고 들은 것에 증인이 되리라
Iwe udzakhala mboni yake kwa anthu onse pa zimene waziona ndi kuzimva.
16 이제는 왜 주저하느뇨 일어나 주의 이름을 불러 세례를 받고 너의 죄를 씻으라 하더라
Ndipo tsopano ukudikira chiyani? Dzuka ndi kutama dzina la Ambuye mopemba, ubatizidwe ndi kuchotsa machimo ako.’
17 후에 내가 예루살렘으로 돌아와서 성전에서 기도할 때에 비몽사몽간에
“Nditabwerera ku Yerusalemu, ndikupemphera mʼNyumba ya Mulungu, ndinachita ngati ndakomoka.
18 보매 주께서 내게 말씀하시되 속히 예루살렘에서 나가라 저희는 네가 내게 대하여 증거하는 말을 듣지 아니하리라 하시거늘
Ndinaona Ambuye akundiwuza kuti, ‘Fulumira! Tuluka mu Yerusalemu msangamsanga, chifukwa anthuwa sadzavomereza umboni wako wonena za Ine.’”
19 내가 말하기를 주여 내가 주 믿는 사람들을 가두고 또 각 회당에서 때리고
Ine ndinayankha Ambuye kuti, “Anthu awa akudziwa kuti ine ndinkapita ku sunagoge iliyonse ndipo ndinkawaponya mʼndende ndi kuwakwapula amene ankakhulupirira inu.
20 또 주의 증인 스데반의 피를 흘릴 적에 내가 곁에 서서 찬성하고 그 죽이는 사람들의 옷을 지킨 줄 저희도 아나이다
Ndipo pamene ankapha Stefano, ine ndinali pomwepo kuvomereza ndi kusunga zovala za amene amamupha.”
21 나더러 또 이르시되 떠나가라 내가 너를 멀리 이방인에게로 보내리라 하셨느니라
Pamenepo Ambuye anandiwuza kuti, “Nyamuka; Ine ndidzakutuma kutali kwa anthu a mitundu ina.”
22 이 말 하는 것까지 저희가 듣다가 소리질러 가로되 이러한 놈은 세상에서 없이 하자 살려 둘 자가 아니라 하여
Gulu la anthu linamvetsera mawu a Paulo mpaka pamene ananena izi, kenaka anakweza mawu awo nafuwula kuti, “Ameneyo aphedwe basi! Ngosayenera kukhala moyo!”
23 떠들며 옷을 벗어 던지고 티끌을 공중에 날리니
Akufuwula ndi kuponya zovala zawo ndi kuwaza fumbi kumwamba,
24 천부장이 바울을 영문 안으로 데려가라 명하고 저희가 무슨 일로 그를 대하여 떠드나 알고자 하여 채찍질하며 신문하라 한대
mkulu wa asilikali analamulira kuti amutenge Paulo kupita naye ku malo a asilikali. Iye analamula kuti Paulo akwapulidwe kwambiri ndi kumufunsa kuti apeze chimene anthu ankafuwulira chotere.
25 가죽줄로 바울을 매니 바울이 곁에 섰는 백부장더러 이르되 `너희가 로마 사람 된 자를 죄도 정치 아니하고 채찍질할 수 있느냐? 하니
Atamumanga kuti amukwapule, Paulo anati kwa msilikali wolamulira asilikali 100 amene anayima pamenepo, “Kodi malamulo amalola kukwapula nzika ya Chiroma imene sinapezedwe yolakwa?”
26 백부장이 듣고 가서 천부장에게 전하여 가로되 `어찌하려 하느뇨 이는 로마 사람이라' 하니
Wolamulira asilikali 100 uja atamva zimenezi, anapita kwa mkulu wa asilikali ndi kumufotokozera. Iye anafunsa kuti, “Kodi mukuchita chiyani ndi munthuyu amene ndi nzika ya Chiroma?”
27 천부장이 와서 바울에게 말하되 `네가 로마 사람이냐? 내게 말하라' 가로되 `그러하다'
Mkulu wa asilikali uja anapita kwa Paulo ndipo anamufunsa kuti, “Tandiwuze, kodi ndiwe nzika ya Chiroma?” Paulo anayankha kuti, “Inde.”
28 천부장이 대답하되 `나는 돈을 많이 들여 이 시민권을 얻었노라' 바울이 가로되 `나는 나면서부터로라' 하니
Kenaka mkulu wa asilikaliyo anati, “Ine ndinapereka ndalama zambiri kuti ndikhale nzika.” Paulo anayankha kuti, “Koma ine ndinabadwa nzika.”
29 신문하려던 사람들이 곧 그에게서 물러가고 천부장도 그가 로마 사람인줄 알고 또는 그 결박한 것을 인하여 두려워하니라
Iwo amene anati amufunse analeka nthawi yomweyo. Mkulu wa asilikali uja anachita mantha atazindikira kuti wamanga Paulo amene ndi nzika ya Chiroma.
30 이튿날 천부장이 무슨 일로 유대인들이 그를 송사하는지 실상을 알고자 하여 그 결박을 풀고 명하여 제사장들과 온 공회를 모으고 바울을 데리고 내려가서 저희 앞에 세우니라
Mmawa mwake, mkulu wa asilikali pofuna kupeza chifukwa chenicheni chimene Ayuda amamunenera Paulo, anamumasula ndipo analamula kuti akulu a ansembe ndi onse akuluakulu a Bwalo Lalikulu asonkhane. Ndipo iye anabweretsa Paulo namuyimiritsa patsogolo pawo.