< 詩篇 133 >
1 ダビデがよめる京まうでの歌 観よはらから相睦てともにをるはいかに善いかに樂きかな
Salimo la Davide. Nyimbo yoyimba pokwera ku Yerusalemu. Onani, nʼkokoma ndi kokondweretsa ndithu pamene abale akhala pamodzi mwachiyanjano!
2 首にそそがれたる貴きあぶら鬚にながれ アロンの鬚にながれ その衣のすそにまで流れしたたるるがごとく
Zili ngati mafuta amtengowapatali othiridwa pa mutu, otsikira ku ndevu, ku ndevu za Aaroni, oyenderera mpaka mʼkhosi mwa mkanjo wake.
3 またヘルモンの露くだりてシオンの山にながるるがごとし そはヱホバかしこに福祉をくだし窮なき生命をさへあたへたまへり
Zili ngati mame a ku Heremoni otsikira pa Phiri la Ziyoni. Pakuti pamenepo Yehova amaperekapo dalitso, ndiwo moyo wamuyaya.