< 箴言 知恵の泉 3 >
1 わが子よ、わたしの教を忘れず、わたしの戒めを心にとめよ。
Mwana wanga, usayiwale malangizo anga, mtima wako usunge malamulo anga.
2 そうすれば、これはあなたの日を長くし、命の年を延べ、あなたに平安を増し加える。
Ukatero zaka za moyo wako zidzachuluka ndipo udzakhala pa mtendere.
3 いつくしみと、まこととを捨ててはならない、それをあなたの首に結び、心の碑にしるせ。
Makhalidwe ochitira ena chifundo ndi owonetsa kukhulupirika asakuchokere. Uwamangirire mʼkhosi mwako ngati mkanda ndi kuwalemba pa mtima pako.
4 そうすれば、あなたは神と人との前に恵みと、誉とを得る。
Ukatero udzapeza kuyanja ndi mbiri yabwino pamaso pa Mulungu ndi anthu.
5 心をつくして主に信頼せよ、自分の知識にたよってはならない。
Uzikhulupirira Yehova ndi mtima wako wonse ndipo usadalire nzeru zako za kumvetsa zinthu.
6 すべての道で主を認めよ、そうすれば、主はあなたの道をまっすぐにされる。
Pa zochita zako zonse uvomereze kuti Mulungu alipo, ndipo Iye adzawongola njira zako.
7 自分を見て賢いと思ってはならない、主を恐れて、悪を離れよ。
Usamadzione ngati wa nzeru. Uziopa Yehova ndi kupewa zoyipa.
8 そうすれば、あなたの身を健やかにし、あなたの骨に元気を与える。
Ukatero thupi lako lidzakhala la moyo wabwino ndi mafupa ako adzakhala olimba.
9 あなたの財産と、すべての産物の初なりをもって主をあがめよ。
Uzilemekeza Yehova ndi chuma chako chonse; zokolola zonse zoyamba kucha uzilemekeza nazonso Yehova.
10 そうすれば、あなたの倉は満ちて余り、あなたの酒ぶねは新しい酒であふれる。
Ukatero nkhokwe zako zidzadzaza ndi zinthu zambiri, ndiponso mitsuko yako idzadzaza ndi vinyo.
11 わが子よ、主の懲しめを軽んじてはならない、その戒めをきらってはならない。
Mwana wanga usanyoze malangizo a Yehova, ndipo usayipidwe ndi chidzudzulo chake.
12 主は、愛する者を、戒められるからである、あたかも父がその愛する子を戒めるように。
Paja Yehova amadzudzula amene amamukonda, monga abambo achitira mwana amene amakondwera naye.
13 知恵を求めて得る人、悟りを得る人はさいわいである。
Wodala munthu amene wapeza nzeru, munthu amene walandira nzeru zomvetsa zinthu,
14 知恵によって得るものは、銀によって得るものにまさり、その利益は精金よりも良いからである。
pakuti phindu la nzeru ndi labwino kuposa la siliva, phindu lakelo ndi labwino kuposanso golide.
15 知恵は宝石よりも尊く、あなたの望む何物も、これと比べるに足りない。
Nzeru ndi yoposa miyala yamtengowapatali; ndipo zonse zimene umazikhumba sizingafanane ndi nzeru.
16 その右の手には長寿があり、左の手には富と、誉がある。
Mʼdzanja lake lamanja muli moyo wautali; mʼdzanja lake lamanzere muli chuma ndi ulemu.
17 その道は楽しい道であり、その道筋はみな平安である。
Njira zake ndi njira zosangalatsa, ndipo mu njira zake zonse muli mtendere.
18 知恵は、これを捕える者には命の木である、これをしっかり捕える人はさいわいである。
Nzeru ili ngati mtengo wopatsa moyo kwa oyigwiritsitsa; wodala munthu amene amayigwiritsa kwambiri.
19 主は知恵をもって地の基をすえ、悟りをもって天を定められた。
Yehova anakhazikitsa dziko lapansi pogwiritsa ntchito nzeru. Anagwiritsanso ntchito nzeru zakudziwa bwino zinthu pamene ankakhazikitsa zakumwamba.
20 その知識によって海はわきいで、雲は露をそそぐ。
Mwa nzeru zake Yehova anatumphutsa madzi kuchokera mʼnthaka ndiponso mitambo inagwetsa mvula.
21 わが子よ、確かな知恵と、慎みとを守って、それをあなたの目から離してはならない。
Mwana wanga usunge nzeru yeniyeni ndi khalidwe lomalingarira zinthu bwino. Zimenezi zisakuchokere.
22 それはあなたの魂の命となりあなたの首の飾りとなる。
Zimenezi zidzakupatsa moyo, moyo wake wosangalatsa ndi wabwino ngati mkanda wa mʼkhosi.
23 こうして、あなたは安らかに自分の道を行き、あなたの足はつまずくことがない。
Choncho udzayenda pa njira yako mosaopa kanthu, ndipo phazi lako silidzapunthwa;
24 あなたは座しているとき、恐れることはなく、伏すとき、あなたの眠りはここちよい。
pamene ugona pansi, sudzachita mantha; ukadzagona pansi tulo tako tidzakhala tokoma.
25 あなたはにわかに起る恐怖を恐れることなく、悪しき者の滅びが来ても、それを恐れることはない。
Usaope tsoka lobwera mwadzidzidzi kapena chiwonongeko chimene chidzagwera anthu oyipa,
26 これは、主があなたの信頼する者であり、あなたの足を守って、わなに捕われさせられないからである。
pakuti Yehova adzakulimbitsa mtima ndipo adzasunga phazi lako kuti lisakodwe mu msampha.
27 あなたの手に善をなす力があるならば、これをなすべき人になすことをさし控えてはならない。
Usaleke kuchitira zabwino amene ayenera kulandira zabwino, pamene uli nazo mphamvu zochitira zimenezi.
28 あなたが物を持っている時、その隣り人に向かい、「去って、また来なさい。あす、それをあげよう」と言ってはならない。
Usanene kwa mnansi wako kuti, “Pita, uchite kubweranso. Ndidzakupatsa mawa” pamene uli nazo tsopano.
29 あなたの隣り人がかたわらに安らかに住んでいる時、これに向かって、悪を計ってはならない。
Usamukonzere chiwembu mnansi wako, amene anakhala nawe pafupi mokudalira.
30 もし人があなたに悪を行ったのでなければ、ゆえなく、これと争ってはならない。
Usakangane ndi munthu wopanda chifukwa pamene iye sanakuchitire zoyipa.
31 暴虐な人を、うらやんではならない、そのすべての道を選んではならない。
Usachite naye nsanje munthu wachiwawa kapena kutsanzira khalidwe lake lililonse.
32 よこしまな者は主に憎まれるからである、しかし、正しい者は主に信任される。
Pakuti Yehova amanyansidwa ndi munthu woyipa koma amayanjana nawo anthu olungama.
33 主の、のろいは悪しき者の家にある、しかし、正しい人のすまいは主に恵まれる。
Yehova amatemberera nyumba ya munthu woyipa, koma amadalitsa nyumba ya anthu olungama.
34 彼はあざける者をあざけり、へりくだる者に恵みを与えられる。
Anthu onyoza, Iye amawanyoza, koma amakomera mtima anthu odzichepetsa.
35 知恵ある者は、誉を得る、しかし、愚かな者ははずかしめを得る。
Anthu anzeru adzalandira ulemu, koma zitsiru adzazichititsa manyazi.