< 箴言 知恵の泉 17 >

1 平穏であって、ひとかたまりのかわいたパンのあるのは、争いがあって、食物の豊かな家にまさる。
Nʼkwabwino kudya mkute koma pali mtendere, kuposa kuchita madyerero mʼnyumba mʼmene muli mikangano.
2 賢いしもべは身持の悪いむすこを治め、かつ、その兄弟たちの中にあって、資産の分け前を獲る。
Kapolo wanzeru adzalamulira mwana wochititsa manyazi, ndipo kapoloyo adzagawana nawo cholowa ngati mmodzi mwa abale.
3 銀を試みるものはるつぼ、金を試みるものは炉、人の心を試みるものは主である。
Siliva amamuyesa mʼngʼanjo ndipo golide amamuyesa mʼngʼanjo, koma Yehova amayesa mitima.
4 悪を行う者は偽りのくちびるに聞き、偽りをいう者は悪しき舌に耳を傾ける。
Munthu woyipa amamvera malangizo oyipa; munthu wabodza amatchera khutu mawu osakaza.
5 貧しい者をあざける者はその造り主を侮る、人の災を喜ぶ者は罰を免れない。
Iye amene amalalatira mʼmphawi amanyoza mlengi wake; amene amakondwerera tsoka la mnzake sadzakhala osalangidwa.
6 孫は老人の冠である、父は子の栄えである。
Zidzukulu ndiye ulemu wa anthu okalamba, ndipo makolo ndiye ulemerero wa ana.
7 すぐれた言葉は愚かな者には似合わない、まして偽りを言うくちびるは君たる者には似合わない。
Kuyankhula bwino sikuyenerana ndi chitsiru, nanji kuyankhula bodza kungayenerane kodi ndi mfumu?
8 まいないはこれを贈る人の目には幸運の玉のようだ、その向かう所、どこでも彼は栄える。
Chiphuphu chili ngati mankhwala amwayi kwa wochiperekayo; kulikonse kumene amapita zinthu zimamuyendera.
9 愛を追い求める人は人のあやまちをゆるす、人のことを言いふらす者は友を離れさせる。
Iye amene amakhululukira zolakwa za wina, amafunitsitsa chikondi; wobwerezabwereza nkhani amapha chibwenzi.
10 一度の戒めがさとき人に徹するのは、百度の懲しめが愚かな人に徹するよりも深い。
Munthu wanzeru amamva kamodzi kokha, munthu wopanda nzeru ndi samvamkunkhu.
11 悪しき者はただ、そむく事のみを求める、それゆえ、彼に向かっては残忍な使者がつかわされる。
Munthu woyipa maganizo ake ali pa kuwukira basi; ndipo bwana adzamutumizira wamthenga wankhanza.
12 愚かな者が愚かな事をするのに会うよりは、子をとられた雌ぐまに会うほうがよい。
Nʼkwabwino kukumana ndi chimbalangondo cholandidwa ana ake kusiyana ndi kukumana ndi chitsiru mu uchitsiru wake.
13 悪をもて善に報いる者は、悪がその家を離れることがない。
Ngati munthu abwezera choyipa kusinthana ndi zabwino, ndiye choyipa sichidzachoka mʼnyumba mwake.
14 争いの初めは水がもれるのに似ている、それゆえ、けんかの起らないうちにそれをやめよ。
Chiyambi cha mikangano chili ngati kukhamulira madzi, choncho uzichokapo mkangano usanayambe.
15 悪しき者を正しいとする者、正しい者を悪いとする者、この二つの者はともに主に憎まれる。
Kumasula munthu wolakwa kapena kumanga munthu wosalakwa, zonse ziwirizi Yehova zimamunyansa.
16 愚かな者はすでに心がないのに、どうして知恵を買おうとして手にその代金を持っているのか。
Ndalama zogulira nzeru zili ndi phindu lanji mʼmanja mwa chitsiru poti iyeyo mutu wake sumayenda bwino?
17 友はいずれの時にも愛する、兄弟はなやみの時のために生れる。
Bwenzi lako limakukonda nthawi zonse, ndipo mʼbale wako anabadwa kuti azikuthandiza pamavuto.
18 知恵のない人は手をうって、その隣り人の前で保証をする。
Munthu wopanda nzeru amavomereza zopereka chikole ndipo iyeyo amasanduka chikole cha mnansi wake.
19 争いを好む者は罪を好む、その門を高くする者は滅びを求める。
Wokonda zolakwa amakonda mkangano, ndipo wokonda kuyankhula zonyada amadziyitanira chiwonongeko.
20 曲った心の者はさいわいを得ない、みだりに舌をもって語る者は災に陥る。
Munthu wamtima woyipa zinthu sizimuyendera bwino; ndipo woyankhula zachinyengo amagwa mʼmavuto.
21 愚かな子を生む者は嘆きを得る、愚か者の父は喜びを得ない。
Mwana wopusa amamvetsa chisoni abambo ake, abambo a chitsiru sakhala ndi chimwemwe.
22 心の楽しみは良い薬である、たましいの憂いは骨を枯らす。
Mtima wosangalala uli ngati mankhwala abwino, koma mtima wokhumudwa umafowoketsa mafupa.
23 悪しき者は人のふところからまいないを受けて、さばきの道をまげる。
Munthu woyipa amalandira chiphuphu chamseri kuti apotoze chiweruzo cholungama.
24 さとき者はその顔を知恵にむける、しかし、愚かな者は目を地の果にそそぐ。
Munthu wozindikira zinthu, maso ake amakhala pa nzeru, koma chitsiru chimwazamwaza maso ake pa dziko lonse lapansi.
25 愚かな子はその父の憂いである、またこれを産んだ母の痛みである。
Mwana wopusa amamvetsa chisoni abambo ake ndipo amapweteketsa mtima amayi ake.
26 正しい人を罰するのはよくない、尊い人を打つのは悪い。
Sibwino kulipitsa munthu wosalakwa, kapena kulanga anthu osalakwa.
27 言葉を少なくする者は知識のある者、心の冷静な人はさとき人である。
Munthu wosunga pakamwa ndiye wodziwa zinthu, ndipo wodekha mtima ndiye womvetsa bwino zinthu.
28 愚かな者も黙っているときは、知恵ある者と思われ、そのくちびるを閉じている時は、さとき者と思われる。
Ngakhale chitsiru chimakhala ngati chanzeru chikakhala chete; ndipo chikatseka pakamwa chimakhala ngati munthu wochenjera.

< 箴言 知恵の泉 17 >