< 箴言 知恵の泉 16 >
1 心にはかることは人に属し、舌の答は主から出る。
Zolinga za mu mtima ndi za munthu, koma kwa Yehova ndiye kumachokera yankho.
2 人の道は自分の目にことごとく潔しと見える、しかし主は人の魂をはかられる。
Zochita zonse za munthu zimaoneka zabwino pamaso pake, koma Yehova ndiye amasanthula zolinga zako.
3 あなたのなすべき事を主にゆだねよ、そうすれば、あなたの計るところは必ず成る。
Pereka ntchito zako zonse mʼmanja mwa Yehova, ndipo zolinga zako zidzachitikadi.
4 主はすべての物をおのおのその用のために造り、悪しき人をも災の日のために造られた。
Yehova amachita zonse ndi cholinga chake, ngakhale anthu oyipa kuti aone tsiku latsoka.
5 すべて心に高ぶる者は主に憎まれる、確かに、彼は罰を免れない。
Munthu aliyense wodzikuza amamunyansa Yehova. Koma dziwani izi: Iwo sadzakhala osalangidwa.
6 いつくしみとまことによって、とがはあがなわれる、主を恐れることによって、人は悪を免れる。
Chifukwa cha chikondi chosasinthika ndi kukhulupirika, munthu amakhululukidwa machimo ake; chifukwa cha kuopa Yehova munthu amapewa zoyipa.
7 人の道が主を喜ばせる時、主はその人の敵をもその人と和らがせられる。
Pamene makhalidwe a munthu akondweretsa Yehova, ngakhale adani ake amakhala naye mwa mtendere.
8 正義によって得たわずかなものは、不義によって得た多くの宝にまさる。
Kuli bwino kukhala ndi zinthu pangʼono zozipeza mwachilungamo, kusiyana ndi kukhala ndi zinthu zambiri zozipeza popanda chilungamo.
9 人は心に自分の道を考え計る、しかし、その歩みを導く者は主である。
Mtima wa munthu umalingalira zochita, koma Yehova ndiye amakhazikitsa njira zake.
10 王のくちびるには神の決定がある、さばきをするとき、その口に誤りがない。
Mawu a mfumu ali ngati mawu ochokera kwa Mulungu; ndipo pakamwa pake sipalakwa poweruza mlandu.
11 正しいはかりと天びんとは主のものである、袋にあるふんどうもすべて彼の造られたものである。
Miyeso ndi masikelo achilungamo zimachokera kwa Yehova; miyala yonse yoyesera ya mʼthumba anayipanga ndi Yehova.
12 悪を行うことは王の憎むところである、その位が正義によって堅く立っているからである。
Kuchita zoyipa kumanyansa mafumu, pakuti chilungamo ndiye maziko a ufumu wake.
13 正しいくちびるは王に喜ばれる、彼は正しい事を言う者を愛する。
Mawu owona amakondweretsa mfumu. Iyo imakonda munthu woyankhula choonadi.
14 王の怒りは死の使者である、知恵ある人はこれをなだめる。
Ukali wa mfumu ndi mthenga wa imfa, koma munthu wanzeru amawupepesa ukaliwo.
15 王の顔の光には命がある、彼の恵みは春雨をもたらす雲のようだ。
Kuwala kwa nkhope ya mfumu kumapatsa moyo; ndipo kukoma mtima kwake kuli ngati mitambo ya mvula nthawi ya chilimwe.
16 知恵を得るのは金を得るのにまさる、悟りを得るのは銀を得るよりも望ましい。
Nʼkwabwino kwambiri kupeza nzeru kupambana golide. Kukhala womvetsa bwino zinthu nʼkwabwino kupambana ndi kukhala ndi siliva.
17 悪を離れることは正しい人の道である、自分の道を守る者はその魂を守る。
Msewu wa munthu wowongoka mtima umapewa zoyipa; wopenyetsetsa kumene akupita amasunga moyo wake.
18 高ぶりは滅びにさきだち、誇る心は倒れにさきだつ。
Kunyada kumafikitsa ku chiwonongeko, ndipo munthu wodzikuza adzagwa.
19 へりくだって貧しい人々と共におるのは、高ぶる者と共にいて、獲物を分けるにまさる。
Nʼkwabwino kukhala ndi mtima wodzichepetsa pakati pa anthu oponderezedwa, kusiyana ndi kugawana zolanda ndi anthu onyada.
20 慎んで、み言葉をおこなう者は栄える、主に寄り頼む者はさいわいである。
Munthu womvera malangizo zinthu zimamuyendera bwino, ndipo wodala ndi amene amadalira Yehova.
21 心に知恵ある者はさとき者ととなえられる、くちびるが甘ければ、その教に人を説きつける力を増す。
A mtima wanzeru amatchedwa ozindikira zinthu, ndipo mawu ake okoma amawonjezera nzeru.
22 知恵はこれを持つ者に命の泉となる、しかし、愚かさは愚かな者の受ける懲しめである。
Kumvetsa zinthu ndi kasupe wa moyo kwa iwo amene ali nako, koma uchitsiru umabweretsa chilango kwa zitsiru.
23 知恵ある者の心はその言うところを賢くし、またそのくちびるに人を説きつける力を増す。
Mtima wanzeru umathandiza munthu kuyankhula mwa nzeru, ndipo mawu ake amawonjezera nzeru.
24 ここちよい言葉は蜂蜜のように、魂に甘く、からだを健やかにする。
Mawu okometsera ali ngati chisa cha njuchi, amakoma mu mtima ndipo amalimbitsa thupi.
25 人が見て自分で正しいとする道があり、その終りはついに死にいたる道となるものがある。
Pali njira ina yooneka ngati yowongoka kwa munthu koma kumatsiriziro kwake ndi imfa.
26 ほねおる者は飲食のためにほねおる、その口が自分に迫るからである。
Njala ya munthu wantchito imamuthandiza kulimbikira; njalayo imamukakamiza kuchitapo kanthu.
27 よこしまな人は悪を企てる、そのくちびるには激しい火のようなものがある。
Munthu wopanda pake amakonzekera kuchita zoyipa ndipo mawu ake ali ngati moto wopsereza.
28 偽る者は争いを起し、つげ口する者は親しい友を離れさせる。
Munthu woyipa mtima amayambitsa mikangano, ndipo miseche imalekanitsa anthu okondana kwambiri.
29 しえたげる者はその隣り人をいざない、これを良くない道に導く。
Munthu wandewu amakopa mnansi wake, ndipo amamuyendetsa njira imene si yabwino.
30 めくばせする者は悪を計り、くちびるを縮める者は悪事をなし遂げる。
Amene amatsinzinira maso ake amalingalira zinthu zokhota; amene amachita msunamo amakonzeka kuchita zoyipa.
31 しらがは栄えの冠である、正しく生きることによってそれが得られる。
Imvi zili ngati chipewa chaufumu chaulemerero; munthu amazipeza akakhala moyo wolungama.
32 怒りをおそくする者は勇士にまさり、自分の心を治める者は城を攻め取る者にまさる。
Munthu wosapsa mtima msanga amaposa munthu wankhondo, munthu wowugwira mtima wake amaposa amene amalanda mzinda.
33 人はくじをひく、しかし事を定めるのは全く主のことである。
Maere amaponyedwa pa mfunga, koma ndiye Yehova amene amalongosola zonse.