< レビ記 7 >

1 愆祭のおきては次のとおりである。それはいと聖なる物である。
“‘Malamulo a nsembe yopepesera kupalamula imene ndi nsembe yopatulika kwambiri ndi awa:
2 愆祭は燔祭をほふる場所でほふらなければならない。そして祭司はその血を祭壇の周囲に注ぎかけ、
Nsembe yopepesera machimo iziphedwa pamalo pomwe amaphera nsembe yopsereza ndipo awaze magazi ake mbali zonse za guwa.
3 そのすべての脂肪をささげなければならない。すなわち脂尾、内臓をおおう脂肪、
Tsono apereke mafuta ake onse: mchira wamafuta ndi mafuta amene amakuta matumbo.
4 二つの腎臓とその上の腰のあたりにある脂肪、腎臓と共に取られる肝臓の上の小葉である。
Aperekenso impsyo ziwiri, mafuta ake pamodzi ndi mafuta onse amene ali chamʼchiwuno, ndiponso mafuta onse amene aphimba chiwindi.
5 祭司はこれを祭壇の上で焼いて、主に火祭としなければならない。これは愆祭である。
Wansembe azitenthe pa guwa kuti zikhale nsembe yotentha pa moto, yoperekedwa kwa Yehova. Imeneyi ndi nsembe yopepesera tchimo lopalamula.
6 祭司たちのうちのすべての男子は、これを食べることができる。これは聖なる所で食べなければならない。これはいと聖なる物である。
Munthu wamwamuna aliyense wa mʼbanja la wansembe angathe kudyako nsembeyo koma adyere ku malo opatulika. Imeneyi ndi nsembe yopatulika kwambiri.
7 罪祭も愆祭も、そのおきては一つであって、異なるところはない。これは、あがないをなす祭司に帰する。
“‘Nsembe yopepesera tchimo lopalamula ndi yofanana ndi nsembe yoperekedwa chifukwa cha tchimo. Ndipo nsembe ziwiri zonsezi zili ndi lamulo limodzi lokha. Wansembe amene wachita mwambo wa nsembe yopepesera machimo a kupalamula atenge nyamayo ngati yake.
8 人が携えてくる燔祭をささげる祭司、その祭司に、そのささげる燔祭のものの皮は帰する。
Wansembe wopereka nsembe yopsereza ya munthu wina aliyense, atenge chikopa cha nsembe yopserezayo kuti chikhale chake.
9 すべて天火で焼いた素祭、またすべて深鍋または平鍋で作ったものは、これをささげる祭司に帰する。
Chopereka chilichonse cha chakudya chophika mu uvuni kapena chokazinga mu mʼphika kapena mu chiwaya ndi cha wansembe amene wapereka nsembezo.
10 すべて素祭は、油を混ぜたものも、かわいたものも、アロンのすべての子たちにひとしく帰する。
Ndipo chopereka china chilichonse cha chakudya chosakaniza ndi mafuta kapena chowuma, chikhale cha ana onse a Aaroni ndipo anawo achigawane mofanana.
11 主にささぐべき酬恩祭の犠牲のおきては次のとおりである。
“‘Malamulo a nsembe ya chiyanjano imene munthu angathe kupereka kwa Yehova ndi awa:
12 もしこれを感謝のためにささげるのであれば、油を混ぜた種入れぬ菓子と、油を塗った種入れぬ煎餅と、よく混ぜた麦粉に油を混ぜて作った菓子とを、感謝の犠牲に合わせてささげなければならない。
“‘Ngati munthuyo apereka chifukwa cha kuthokoza, apereke nsembeyo pamodzi ndi makeke wopanda yisiti, osakaniza ndi mafuta; timitanda ta buledi wopanda yisiti, topyapyala, topaka mafuta, ndiponso makeke a ufa wosalala wophikidwa bwino, wosakaniza ndi mafuta.
13 また種を入れたパンの菓子をその感謝のための酬恩祭の犠牲に合わせ、供え物としてささげなければならない。
Pamodzi ndi nsembe yachiyanjano yothokozerayo abwerenso ndi makeke opangidwa ndi yisiti ngati chopereka chake.
14 すなわちこのすべての供え物のうちから、菓子一つずつを取って主にささげなければならない。これは酬恩祭の血を注ぎかける祭司に帰する。
Munthuyo atenge mtanda umodzi pa mtanda wa buledi wa mtundu uliwonse kuti ukhale nsembe yopereka kwa Yehova. Tsono mtanda umenewo ndi wake wa wansembe amene awaze magazi a nsembe yachiyanjano.
15 その感謝のための酬恩祭の犠牲の肉は、その供え物をささげた日のうちに食べなければならない。少しでも明くる朝まで残して置いてはならない。
Nyama ya nsembe yachiyanjano yothokozera idyedwe pa tsiku lomwe nsembeyo yaperekedwa ndipo isatsaleko mpaka mmawa.
16 しかし、その供え物の犠牲がもし誓願の供え物、または自発の供え物であるならば、その犠牲をささげた日のうちにそれを食べ、その残りはまた明くる日に食べることができる。
“‘Koma ngati nsembe yakeyo apereka chifukwa cha lumbiro kapena mwaufulu, nsembeyo adye tsiku lomwe yaperekedwalo. Koma yotsala angathe kuyidya mmawa mwake.
17 ただし、その犠牲の肉の残りは三日目には火で焼き捨てなければならない。
Ngati nyama ina ya nsembe yatsalabe mpaka tsiku lachitatu, imeneyo itenthedwe pa moto.
18 もしその酬恩祭の犠牲の肉を三日目に少しでも食べるならば、それは受け入れられず、また供え物と見なされず、かえって忌むべき物となるであろう。そしてそれを食べる者はとがを負わなければならない。
Ngati munthu adya nyama yachiyanjano pa tsiku lachitatu, nsembeyo sidzalandiridwa. Amene wayipereka nsembeyo Mulungu sadzamulandira ndipo nsembeyo idzakhala yonyansa pamaso pa Mulungu, yosamupindulira kanthu woperekayo.
19 その肉がもし汚れた物に触れるならば、それを食べることなく、火で焼き捨てなければならない。犠牲の肉はすべて清い者がこれを食べることができる。
“‘Nyama imene yakhudza chilichonse chodetsedwa, munthu asayidye, koma itenthedwe pa moto. Aliyense amene ali woyeretsedwa angathe kudya nyama inayo.
20 もし人がその身に汚れがあるのに、主にささげた酬恩祭の犠牲の肉を食べるならば、その人は民のうちから断たれるであろう。
Koma ngati munthu wina amene ndi wosayeretsedwa adya nyama ya nsembe yachiyanjano imene ndi ya Yehova, ameneyo achotsedwe pakati pa anthu a mtundu wake.
21 また人がもしすべて汚れたもの、すなわち人の汚れ、あるいは汚れた獣、あるいは汚れた這うものに触れながら、主にささげた酬恩祭の犠牲の肉を食べるならば、その人は民のうちから断たれるであろう』」。
Ndipo ngati munthu wina akhudza chinthu chodetsedwa, kaya chonyansa cha munthu kapena cha nyama, kapenanso chonyansa china chilichonse, ndipo kenaka nʼkudya nyama ya nsembe yachiyanjano imene ndi ya Yehova, munthu ameneyo achotsedwe pakati anthu a mtundu wake.’”
22 主はまたモーセに言われた、
Yehova anayankhula ndi Mose kuti,
23 「イスラエルの人々に言いなさい、『あなたがたは、すべて牛、羊、やぎの脂肪を食べてはならない。
“Awuze Aisraeli kuti, ‘Musadye mafuta a ngʼombe, nkhosa kapenanso mbuzi.
24 自然に死んだ獣の脂肪および裂き殺された獣の脂肪は、さまざまのことに使ってもよい。しかし、それは決して食べてはならない。
Mafuta a nyama yofa yokha, kapena mafuta a nyama yophedwa ndi zirombo akhoza kuwagwiritsa ntchito iliyonse, koma inu musadye mafuta amenewo.
25 だれでも火祭として主にささげる獣の脂肪を食べるならば、これを食べる人は民のうちから断たれるであろう。
Pakuti munthu wakudya mafuta a nyama yoperekedwa kwa Yehova ngati nsembe yotentha pa moto, ayenera kuchotsedwa pakati pa anthu a mtundu wake.
26 またあなたがたはすべてその住む所で、鳥にせよ、獣にせよ、すべてその血を食べてはならない。
Ndipo kulikonse kumene mukakhale musakadye magazi a mbalame iliyonse kapena magazi a nyama iliyonse.
27 だれでもすべて血を食べるならば、その人は民のうちから断たれるであろう』」。
Ngati munthu aliyense adya magazi achotsedwe pakati pa anthu a mtundu wake.’”
28 主はまたモーセに言われた、
Yehova anayankhula ndi Mose kuti,
29 「イスラエルの人々に言いなさい、『酬恩祭の犠牲を主にささげる者は、その酬恩祭の犠牲のうちから、その供え物を主に携えてこなければならない。
“Awuze Aisraeli kuti, Aliyense amene apereka nsembe yachiyanjano kwa Yehova, abwere ndi gawo la nsembeyo kwa Yehova.
30 主の火祭は手ずからこれを携えてこなければならない。すなわちその脂肪と胸とを携えてきて、その胸を主の前に揺り動かして、揺祭としなければならない。
Atenge ndi manja ake zigawo za chopereka zoyenera kuzitentha pa moto ngati chopereka kwa Yehova. Abweretse mafuta, pamodzi ndi chidale chomwe, ndipo chidalecho achiweyule kuti chikhale chopereka choweyula kwa Yehova.
31 そして祭司はその脂肪を祭壇の上で焼かなければならない。その胸はアロンとその子たちに帰する。
Wansembe atenthe mafutawo pa guwa koma chidalecho chikhale cha Aaroni ndi ana ake.
32 あなたがたの酬恩祭の犠牲のうちから、その右のももを挙祭として、祭司に与えなければならない。
Mumupatse wansembe ntchafu ya kumanja ya nsembe yanu yachiyanjano kuti ikhale chopereka chanu kwa iye.
33 アロンの子たちのうち、酬恩祭の血と脂肪とをささげる者は、その右のももを自分の分として、獲るであろう。
Mwana wa Aaroni amene amapereka magazi ndi mafuta a nsembe yachiyanjano, adzitenga ntchafu ya kumanja kukhala gawo lake.
34 わたしはイスラエルの人々の酬恩祭の犠牲のうちから、その揺祭の胸と挙祭のももを取って、祭司アロンとその子たちに与え、これをイスラエルの人々から永久に彼らの受くべき分とする。
Choncho pa zopereka zachiyanjano za Aisraeli, Ine ndatengapo chidale chomwe amaweyula ndi ntchafu zimene amapereka nsembe ndipo ndazipereka kwa wansembe Aaroni ndi ana ake. Izi ndizo gawo lawo nthawi zonse pa zopereka za Aisraeli.”
35 これは主の火祭のうちから、アロンの受ける分と、その子たちの受ける分とであって、祭司の職をなすため、彼らが主にささげられた日に定められたのである。
Zimenezi ndi chigawo cha Aaroni ndi ana ake chotapidwa pa zopereka kwa Yehova zoti zitenthedwe pa moto zimene zinaperekedwa pa tsiku limene anapatulidwa kuti akhale ansembe otumikira Yehova.
36 すなわち、これは彼らに油を注ぐ日に、イスラエルの人々が彼らに与えるように、主が命じられたものであって、代々永久に受くべき分である』」。
Yehova ndiye analamulira kuti pa zopereka za Aisraeli azitapapo zimenezi ndi kuwapatsa ansembe ngati gawo lawo. Yehovayo analamula zimenezi pa tsiku limene ansembewo anapatulidwa ndipo anachikhazikitsa ngati lamulo la nthawi zonse.
37 これは燔祭、素祭、罪祭、愆祭、任職祭、酬恩祭の犠牲のおきてである。
Awa ndi malamulo a nsembe izi: nsembe yopsereza, nsembe yachakudya, nsembe yopepesera machimo, nsembe yopepesera kupalamula, nsembe ya mwambo wodzoza ndi nsembe yachiyanjano.
38 すなわち、主がシナイの荒野においてイスラエルの人々にその供え物を主にささげることを命じられた日に、シナイ山でモーセに命じられたものである。
Malamulo amenewa Yehova anapereka kwa Mose pa Phiri la Sinai pa tsiku limene Yehova analamulira Aisraeli kuti abwere ndi zopereka za kwa Yehova, ku chipululu cha Sinai kuja.

< レビ記 7 >