< レビ記 18 >

1 主はまたモーセに言われた、
Yehova anawuza Mose kuti,
2 「イスラエルの人々に言いなさい、『わたしはあなたがたの神、主である。
“Yankhula ndi Aisraeli ndipo uwawuze kuti, ‘Ine ndine Yehova Mulungu wanu.
3 あなたがたの住んでいたエジプトの国の習慣を見習ってはならない。またわたしがあなたがたを導き入れるカナンの国の習慣を見習ってはならない。また彼らの定めに歩んではならない。
Musamachite zomwe amachita anthu a ku Igupto kumene munkakhala kuja, ndiponso musamachite zomwe amachita anthu a ku Kanaani kumene ndikukupititsani. Musatsatire miyambo yawo.
4 わたしのおきてを行い、わたしの定めを守り、それに歩まなければならない。わたしはあなたがたの神、主である。
Inu muzimvera malamulo anga ndipo muzisamalitsa kutsatira malangizo anga. Ine ndine Yehova Mulungu wanu.
5 あなたがたはわたしの定めとわたしのおきてを守らなければならない。もし人が、これを行うならば、これによって生きるであろう。わたしは主である。
Choncho sungani malangizo ndi malamulo anga, popeza munthu amene amvera zimenezi adzakhala ndi moyo. Ine ndine Yehova.
6 あなたがたは、だれも、その肉親の者に近づいて、これを犯してはならない。わたしは主である。
“‘Munthu aliyense asagonane ndi wachibale wake. Ine ndine Yehova.
7 あなたの母を犯してはならない。それはあなたの父をはずかしめることだからである。彼女はあなたの母であるから、これを犯してはならない。
“‘Usachititse manyazi abambo ako pogonana ndi amayi ako. Iwo ndi amayi ako. Usagonane nawo.
8 あなたの父の妻を犯してはならない。それはあなたの父をはずかしめることだからである。
“‘Usagonane ndi mkazi wa abambo ako (osakhala amayi okubala). Ukatero ukuchititsa manyazi abambo ako.
9 あなたの姉妹、すなわちあなたの父の娘にせよ、母の娘にせよ、家に生れたのと、よそに生れたのとを問わず、これを犯してはならない。
“‘Usagonane ndi mlongo wako, mwana wamkazi wa abambo ako, kapena mwana wamkazi wa amayi ako, kaya anabadwira mʼnyumba mwanu kapena kwina.
10 あなたのむすこの娘、あるいは、あなたの娘の娘を犯してはならない。それはあなた自身をはずかしめることだからである。
“‘Usagonane ndi mdzukulu wako: mwana wa mwana wako wamwamuna kapena mwana wa mwana wako wamkazi. Kutero nʼkudzichotsa ulemu.
11 あなたの父の妻があなたの父によって産んだ娘は、あなたの姉妹であるから、これを犯してはならない。
“‘Usagonane ndi mwana wamkazi wa mkazi wa abambo ako, amene abambo akowo anabereka; popeza ameneyo ndi mlongo wako.
12 あなたの父の姉妹を犯してはならない。彼女はあなたの父の肉親だからである。
“‘Usagonane ndi mlongo wa abambo ako; popeza ameneyo ndi thupi limodzi ndi abambo ako.
13 またあなたの母の姉妹を犯してはならない。彼女はあなたの母の肉親だからである。
“‘Usagonane ndi mchemwali wa amayi ako chifukwa ameneyo ndi thupi limodzi ndi amayi ako.
14 あなたの父の兄弟の妻を犯し、父の兄弟をはずかしめてはならない。彼女はあなたのおばだからである。
“‘Usachititse manyazi mchimwene wa abambo ako pogonana ndi mkazi wake popeza amenewo ndi azakhali ako.
15 あなたの嫁を犯してはならない。彼女はあなたのむすこの妻であるから、これを犯してはならない。
“‘Usagonane ndi mpongozi wako popeza ameneyo ndi mkazi wa mwana wako. Choncho usamuchititse manyazi.
16 あなたの兄弟の妻を犯してはならない。それはあなたの兄弟をはずかしめることだからである。
“‘Usagonane ndi mkazi wa mchimwene wako popeza potero ukuchititsa manyazi mʼbale wakoyo.
17 あなたは女とその娘とを一緒に犯してはならない。またその女のむすこの娘、またはその娘の娘を取って、これを犯してはならない。彼らはあなたの肉親であるから、これは悪事である。
“‘Usagonane ndi mkazi ndiponso mwana wake wamkazi. Usagonane ndi mwana wamkazi wa mwana wake wamwamuna, kapena mwana wamkazi wa mwana wake wamkazi. Amenewo ndi thupi limodzi ndi mkaziyo. Kutero ndikuchita chinthu choyipa kwambiri.
18 あなたは妻のなお生きているうちにその姉妹を取って、同じく妻となし、これを犯してはならない。
“‘Usakwatire mchemwali wa mkazi wako ndi kumagonana naye mkazi wakoyo ali moyo ngati wopikisana naye.
19 あなたは月のさわりの不浄にある女に近づいて、これを犯してはならない。
“‘Usamuyandikire mkazi kuti ugonane naye pa nthawi yake yosamba.
20 隣の妻と交わり、彼女によって身を汚してはならない。
“‘Usagonane ndi mkazi wa mnzako ndi kudziyipitsa naye.
21 あなたの子どもをモレクにささげてはならない。またあなたの神の名を汚してはならない。わたしは主である。
“‘Usapereke mwana wako aliyense kuti akhale nsembe yamoto kwa Moleki ndi kuyipitsa dzina la Yehova. Ine ndine Yehova.
22 あなたは女と寝るように男と寝てはならない。これは憎むべきことである。
“‘Usagonane ndi mwamuna ngati mkazi; chimenecho ndi chinthu chonyansa.
23 あなたは獣と交わり、これによって身を汚してはならない。また女も獣の前に立って、これと交わってはならない。これは道にはずれたことである。
“‘Usagonane ndi nyama ndi kudziyipitsa nayo. Mkazi asadzipereke kwa nyama kuti agonane nayo. Chimenecho ndi chisokonezo.
24 あなたがたはこれらのもろもろの事によって身を汚してはならない。わたしがあなたがたの前から追い払う国々の人は、これらのもろもろの事によって汚れ、
“‘Musadzidetse ndi zinthu zimenezi chifukwa umo ndi mmene mitundu ina imene ndikuyithamangitsa pamaso panu inadzidetsera.
25 その地もまた汚れている。ゆえに、わたしはその悪のためにこれを罰し、その地もまたその住民を吐き出すのである。
Choncho dziko linayipa ndipo ndinalilanga chifukwa cha tchimo lake. Motero dzikolo linasanza anthu ake okhalamo.
26 ゆえに、あなたがたはわたしの定めとわたしのおきてを守り、これらのもろもろの憎むべき事の一つでも行ってはならない。国に生れた者も、あなたがたのうちに宿っている寄留者もそうである。
Koma inu mukasunge malangizo ndi malamulo anga. Mbadwa ndiponso alendo amene akukhala pakati panu asakachite china chilichonse cha zinthu zonyansazi,
27 あなたがたの先にいたこの地の人々は、これらのもろもろの憎むべき事を行ったので、その地も汚れたからである。
pakuti zinthu zonsezi ndi zomwe ankachita anthu amene ankakhala mʼdzikomo inu musanafike, ndipo dziko linayipitsidwa.
28 これは、あなたがたがこの地を汚して、この地があなたがたの先にいた民を吐き出したように、あなたがたをも吐き出すことのないためである。
Koma inu musachite zimenezi kuti dziko lingakusanzeni mutaliyipitsa monga linasanzira mitundu imene imakhalamo inu musanafike.
29 これらのもろもろの憎むべき事の一つでも行う者があれば、これを行う人は、だれでもその民のうちから断たれるであろう。
“‘Aliyense wochita zinthu zonyansa zimenezi achotsedwe pakati pa anthu anzake.
30 それゆえに、あなたがたはわたしの言いつけを守り、先に行われたこれらの憎むべき風習の一つをも行ってはならない。またこれによって身を汚してはならない。わたしはあなたがたの神、主である』」。
Choncho mverani malangizo anga oletsa kuchita miyambo yonyansayi imene ankatsatira anthu amene analipo inu musanafike ndi kudziyipitsa nayo. Ine ndine Yehova Mulungu wanu.’”

< レビ記 18 >