< エレミヤ書 41 >
1 七月のころ、王家のもので、エリシャマの子ネタニヤの子であり、また王の高官のひとりであるイシマエルは、王の十人のつかさたちと共にミヅパにいたアヒカムの子ゲダリヤのもとにきて、ミヅパで食を共にしたが、
Pa mwezi wachisanu ndi chiwiri Ismaeli mwana wa Netaniya, mdzukulu wa Elisama amene anali wa banja laufumu ndiponso mmodzi wa atsogoleri a ankhondo a mfumu, anabwera ku Mizipa kwa Gedaliya mwana wa Ahikamu ndi anthu khumi. Pamene ankadya naye kumeneko,
2 ネタニヤの子イシマエルおよび共にいた十人の者は立ち上がって、バビロンの王がこの地の総督としたシャパンの子アヒカムの子であるゲダリヤを刀で殺し、
Ismaeli mwana wa Netaniya pamodzi ndi anthu khumi aja anayimirira ndi kupha ndi lupanga Gedaliya mwana wa Ahikamu, mdzukulu wa Safani. Choncho anapha munthu amene mfumu ya ku Babuloni inamusankha kukhala bwanamkubwa wa dzikolo.
3 イシマエルはまたミヅパでゲダリヤと共にいたすべてのユダヤ人と、たまたまそこにいたカルデヤびとの兵士たちを殺した。
Ismaeli anaphanso Ayuda onse amene anali pamodzi ndi Gedaliya ku Mizipa, kuphatikizanso asilikali a Ababuloni amene anali ku Mizipako.
4 ゲダリヤが殺された次の日、まだだれもその事を知らないうちに、
Mmawa mwake, anthu asanadziwe kuti Gedaliya waphedwa,
5 八十人の人々がそのひげをそり、衣服をさき、身に傷をつけ、手には素祭のささげ物と香を携え、シケム、シロ、サマリヤからきて、主の宮にささげようとした。
kunafika anthu 80 ochekera ku Sekemu, Silo ndi Samariya, amene anali atameta ndevu zawo, atangʼamba zovala zawo ndi kudzichekacheka. Iwowa anatenga chopereka cha ufa ndi lubani kuti adzapereke ku Nyumba ya Yehova.
6 ネタニヤの子イシマエルはミヅパから泣きながら出てきて彼らを迎え、彼らに会って、「アヒカムの子ゲダリヤのもとにおいでなさい」と言った。
Ismaeli mwana wa Netaniya anachoka ku Mizipa akulira kupita kukakumana nawo. Atakumana nawo, iye anati, “Bwerani mudzaonane ndi Gedaliya mwana wa Ahikamu.”
7 そして彼らが町の中にはいったとき、ネタニヤの子イシマエルは自分と一緒にいた人々と共に彼らを殺して、その死体を穴に投げ入れた。
Atafika pakati pa mzinda, Ismaeli mwana wa Netaniya pamodzi ndi anthu amene anali naye anawapha anthuwo ndi kuwaponya mʼchitsime.
8 しかしそのうちの十人はイシマエルに向かい、「わたしたちは畑に小麦、大麦、油、および蜜を隠しています、わたしたちを殺さないでください」と言ったので、彼らをその仲間と共に殺さないでしまった。
Koma anthu khumi a gululo anawuza Ismaeli kuti, “Musatiphe! Tili ndi tirigu ndi barele, mafuta ndi uchi, zimene tabisa mʼmunda.” Choncho anawasiya ndipo sanawaphere pamodzi ndi anzawo aja.
9 イシマエルが自分の殺した人々の死体を投げ入れた穴は、アサ王がイスラエルの王バアシャを恐れて掘った穴であった。ネタニヤの子イシマエルは殺した人々をこれに満たした。
Tsono chitsime chimene anaponyamo mitembo ya anthu amene anawaphawo pamodzi ndi mtembo wa Gedaliya chinali chimene mfumu Asa anachikumba poopsedwa ndi Baasa mfumu ya Israeli. Ismaeli mwana wa Netaliya anachidzaza ndi mitembo.
10 次いでイシマエルはミヅパに残っているすべての民、すなわち王の娘たちと侍衛の長ネブザラダンがアヒカムの子ゲダリヤに託したミヅパに残っているすべての民とを捕虜とした。ネタニヤの子イシマエルは彼らを捕虜とし、アンモンびとのもとに渡り行こうとして立ち去った。
Pambuyo pake Ismaeli anatenga ukapolo anthu ena onse amene anali ku Mizipa: ana aakazi a mfumu pamodzi ndi ena onse amene anatsalira kumeneko, amene Nebuzaradani mtsogoleri wa asilikali olonda mfumu anapatsa Gedaliya mwana wa Ahikamu kuti akhale bwanamkubwa wawo. Ismaeli mwana wa Netaliya anatenga ukapolo anthuwa ndi kuwoloka nawo kumapita ku dziko la Aamoni.
11 カレヤの子ヨハナンおよび彼と共にいる軍勢の長たちはネタニヤの子イシマエルの行った悪事をみな聞き、
Pamene Yohanani mwana wa Kareya ndi atsogoleri onse a ankhondo amene anali naye pamodzi anamva zoyipa zonse zimene Ismaeli mwana wa Netaniya anachita,
12 その兵士たちを率いて、ネタニヤの子イシマエルと戦うために出て行き、ギベオンの大池のほとりで彼に会った。
anatenga ankhondo awo onse kupita kukamenyana ndi Ismaeli mwana wa Netaniya. Anakamupeza kufupi ndi chidziwe chachikulu cha ku Gibiyoni.
13 イシマエルと共にいる人々は、カレヤの子ヨハナンおよび彼と共にいる軍勢の長たちを見て喜んだ。
Pamene anthu onse amene Ismaeli anawagwira anaona Yohanani mwana wa Kareya pamodzi ndi atsogoleri a ankhondo amene anali naye, anasangalala.
14 そしてイシマエルがミヅパから捕虜にしてきた人々は身をめぐらしてカレヤの子ヨハナンのもとへ行った。
Anthu onse amene Ismaeli anawagwira ukapolo ku Mizipa anabwerera ndi kupita kwa Yohanani mwana wa Kareya.
15 ネタニヤの子イシマエルは八人の者と共にヨハナンを避けて逃げ、アンモンびとの所へ行った。
Koma Ismaeli pamodzi ndi anthu ake asanu ndi atatu, anathawa Yohanani ndi kuthawira kwa Aamoni.
16 そこでカレヤの子ヨハナンおよび彼と共にいる軍勢の長たちはネタニヤの子イシマエルがアヒカムの子ゲダリヤを殺して、ミヅパから捕虜として連れてきた、あの残っていた民、すなわち兵士や女、子供、宦官をギベオンから連れ帰ったが、
Kenaka Yohanani mwana wa Kareya pamodzi ndi atsogoleri onse a ankhondo amene anali naye anatsogolera anthu onse otsala a ku Mizipa amene anawapulumutsa kwa Ismaeli mwana wa Netaniya atapha Gedaliya mwana wa Ahikamu. Anthu amenewa anali: asilikali, akazi, ana ndi amuna ofulidwa otumikira mfumu amene anawatenga ku Gibiyoni.
17 彼らはエジプトへ行こうとしてベツレヘムの近くにあるゲルテ・キムハムへ行って、そこにとどまった。
Ndipo ananyamuka nayima ku Geruti Kimuhamu pafupi ndi Betelehemu pa ulendo wawo wopita ku Igupto
18 これは、ネタニヤの子イシマエルが、バビロンの王によってこの地の総督に任じられたアヒカムの子ゲダリヤを殺したことにより、カルデヤびとを恐れたからである。
kuthawa Ababuloni. Iwo anaopa Ababuloniwo chifukwa Ismaeli mwana wa Netaniya anapha Gedaliya mwana wa Ahikamu, amene mfumu ya ku Babuloni inamuyika kukhala bwanamkubwa wa dzikolo.