< イザヤ書 32 >

1 見よ、ひとりの王が正義をもって統べ治め、君たちは公平をもってつかさどり、
Taonani, kudzakhala mfumu ina imene idzalamulira mwachilungamo, ndipo akalonga ake adzaweruza molungama.
2 おのおの風をさける所、暴風雨をのがれる所のようになり、かわいた所にある水の流れのように、疲れた地にある大きな岩の陰のようになる。
Munthu aliyense adzakhala ngati pothawirapo mphepo ndi malo obisalirapo namondwe, adzakhala ngati mitsinje ya mʼchipululu, ngati mthunzi wa thanthwe lalikulu la mʼdziko lowuma.
3 こうして、見る者の目は開かれ、聞く者の耳はよく聞き、
Ndipo maso a anthu openya sadzakhalanso otseka, ndipo makutu a anthu akumva adzamvetsetsa.
4 気短な者の心は悟る知識を得、どもりの舌はたやすく、あざやかに語ることができる。
Anthu a mtima wopupuluma adzadziwa ndi kuchita zinthu mofatsa, ndipo anthu ovutika kuyankhula adzayankhula mosadodoma ndi momveka.
5 愚かな者は、もはや尊い人と呼ばれることなく、悪人はもはや、りっぱな人と言われることはない。
Chitsiru sichidzatchedwanso munthu waulemu wake ndipo munthu woyipa sadzalemekezedwa.
6 それは愚かな者は愚かなことを語り、その心は不義をたくらみ、よこしまを行い、主について誤ったことを語り、飢えた者の望みを満たさず、かわいた者の飲み物を奪い取るからである。
Pakuti munthu opusa amayankhula zauchitsiru, amaganiza kuchita zoyipa: Iye amachita zoyipira Mulungu, ndipo amafalitsa zolakwika zokhudza Yehova; anjala sawapatsa chakudya ndipo aludzu sawapatsa madzi.
7 悪人の行いは悪い。彼は悪い計りごとをめぐらし、偽りの言葉をもって貧しい者をおとしいれ、乏しい者が正しいことを語っても、なお、これをおとしいれる。
Munthu woyipa njira zake ndi zoyipanso, iye kwake nʼkulingalira zinthu zoyipa. Amalingalira zakuti awononge anthu aumphawi ndi mabodza ake ngakhale kuti waumphawiyo akuyankhula zoona.
8 しかし尊い人は尊いことを語り、つねに尊いことを行う。
Koma munthu wolemekezeka amalingaliranso kuchita zinthu zabwino, Iye amakhazikika pa zinthu zabwinozo.
9 安んじている女たちよ、起きて、わが声を聞け。思い煩いなき娘たちよ、わが言葉に耳を傾けよ。
Khalani maso, inu akazi amene mukungokhala wopanda kulingalira kuti kunja kulinji ndipo imvani mawu anga. Inu akazi odzitama, imvani zimene ndikunena!
10 思い煩いなき女たちよ、一年あまりの日をすぎて、あなたがたは震えおののく。ぶどうの収穫がむなしく、実を取り入れる時が来ないからだ。
Pakapita chaka ndi masiku pangʼono inu akazi amatama mudzanjenjemera; chifukwa mitengo ya mphesa idzakanika ndipo zipatso sizidzaoneka.
11 安んじている女たちよ、震え恐れよ。思い煩いなき女たちよ、震えおののけ。衣を脱ぎ、裸になって腰に荒布をまとえ。
Nthunthumirani inu okhala mosatekesekanu; ndipo njenjemerani, inu akazi omadzikhulupirira nokhanu. Vulani zovala zanu, ndipo valani ziguduli mʼchiwuno mwanu.
12 良き畑のため、実り豊かなぶどうの木のために胸を打て。
Dzigugudeni pachifuwa mwachisoni chifukwa minda yachonde, ndi mphesa yawonongeka.
13 いばら、おどろの生えているわが民の地のため、喜びに満ちている町にあるすべての喜びの家のために胸を打て。
Mʼdziko la anthu anga mwamera minga ndi mkandankhuku. Zoona, mulilire nyumba zonse zachikondwerero ndi mzinda uno umene unali wachisangalalo.
14 宮殿は捨てられ、にぎわった町は荒れすたれ、丘と、やぐらとは、とこしえにほら穴となり、野のろばの楽しむ所、羊の群れの牧場となるからである。
Nyumba yaufumu idzasiyidwa, mzinda waphokoso udzakhala wopanda anthu; malinga ndi nsanja zidzasanduka chipululu mpaka muyaya. Abulu adzasangalalamo ndipo ziweto zidzapezamo msipu.
15 しかし、ついには霊が上からわれわれの上にそそがれて、荒野は良き畑となり、良き畑は林のごとく見られるようになる。
Yehova adzatipatsa mzimu wake, ndipo dziko lachipululu lidzasanduka munda wachonde, ndipo munda wachonde udzakhala ngati nkhalango.
16 その時、公平は荒野に住み、正義は良き畑にやどる。
Tsono mʼchipululu mudzakhala chiweruzo cholungama ndipo mʼminda yachonde mudzakhala chilungamo.
17 正義は平和を生じ、正義の結ぶ実はとこしえの平安と信頼である。
Mtendere udzakhala chipatso chachilungamo; zotsatira za chilungamo zidzakhala bata ndi kudzidalira mpaka muyaya.
18 わが民は平和の家におり、安らかなすみかにおり、静かな休み所におる。
Anthu anga adzakhala mʼmidzi yamtendere, mʼnyumba zodalirika, ndi malo osatekeseka a mpumulo.
19 しかし林はことごとく切り倒され、町もことごとく倒される。
Ngakhale nkhalango idzawonongedwa ndi matalala ndipo mzinda udzagwetsedwa mpaka pansi,
20 すべての水のほとりに種をまき、牛およびろばを自由に放ちおくあなたがたは、さいわいである。
inutu mudzakhala odalitsika ndithu. Mudzadzala mbewu zanu mʼmbali mwa mtsinje uliwonse, ndipo ngʼombe zanu ndi abulu anu zidzadya paliponse.

< イザヤ書 32 >