< エゼキエル書 1 >

1 第三十年四月五日に、わたしがケバル川のほとりで、捕囚の人々のうちにいた時、天が開けて、神の幻を見た。
Tsiku lachisanu la mwezi wachinayi, chaka cha makumi atatu, ine ndinali pakati pa amʼndende mʼmbali mwa mtsinje wa Kebara. Tsono kumwamba kunatsekuka ndipo ndinaona maonekedwe a Mulungu mʼmasomphenya.
2 これはエホヤキン王の捕え移された第五年であって、その月の五日に、
Pa tsiku lachisanu la mwezi, chaka chachisanu Yehoyakini ali mʼndende,
3 主の言葉がケバル川のほとり、カルデヤびとの地でブジの子祭司エゼキエルに臨み、主の手がその所で彼の上にあった。
Yehova anayankhula ndi wansembe Ezekieli, mwana wa Buzi, mʼmbali mwa mtsinje wa Kebara mʼdziko la Ababuloni. Dzanja la Yehova linali pa iye kumeneko.
4 わたしが見ていると、見よ、激しい風と大いなる雲が北から来て、その周囲に輝きがあり、たえず火を吹き出していた。その火の中に青銅のように輝くものがあった。
Ndinayangʼana ndipo ndinangoona mphepo yamkuntho ikubwera kuchokera kumpoto. Panali mtambo waukulu wozunguliridwa ndi kuwala ndipo moto unali lawilawi kuchokera mu mtambowo. Pakati pa motowo pankaoneka ngati mkuwa wonyezimira.
5 またその中から四つの生きものの形が出てきた。その様子はこうである。彼らは人の姿をもっていた。
Mʼkatikati mwa motowo munali zinthu zinayi zamaonekedwe a nyama. Thupi lawo limaoneka ngati la munthu
6 おのおの四つの顔をもち、またそのおのおのに四つの翼があった。
koma chilichonse chinali ndi nkhope zinayi ndiponso mapiko anayi.
7 その足はまっすぐで、足のうらは子牛の足のうらのようであり、みがいた青銅のように光っていた。
Miyendo yake inali yowongoka; mapazi ake anali a ziboda ngati phazi la mwana wangʼombe. Ndipo zibodazo zinkawala ngati mkuwa wonyezimira.
8 その四方に、そのおのおのの翼の下に人の手があった。この四つの者はみな顔と翼をもち、
Mʼmunsi mwa mapiko awo kumbali zonse zinayi, nyamazo zinali ndi manja a munthu. Zonse zinayi zinali ndi nkhope ndi mapiko,
9 翼は互に連なり、行く時は回らずに、おのおの顔の向かうところにまっすぐに進んだ。
ndipo mapiko awowo anakhudzana. Chilichonse chimapita molunjika kutsogolo; sizimatembenuka pamene zimayenda.
10 顔の形は、おのおのその前方に人の顔をもっていた。四つの者は右の方に、ししの顔をもち、四つの者は左の方に牛の顔をもち、また四つの者は後ろの方に、わしの顔をもっていた。
Nkhope zawo zimaoneka motere: Chilichonse chinali ndi nkhope ya munthu, ndipo mbali ya kumanja chilichonse chinali ndi nkhope zinayi zosiyana motere: nkhope ya munthu, nkhope ya mkango ku dzanja lamanja, nkhope ya ngʼombe ku dzanja lamanzere, ndipo kumbuyo kwake nkhope ya chiwombankhanga.
11 彼らの顔はこのようであった。その翼は高く伸ばされ、その二つは互に連なり、他の二つをもってからだをおおっていた。
Ndi mʼmene zinalili nkhope zawo. Mapiko awo anali otambasukira mmwamba. Chamoyo chilichonse chinali ndi mapiko awiri okhudzana ndi mapiko a chinzake. Chinalinso ndi mapiko ena awiri ophimbira thupi lake.
12 彼らはおのおのその顔の向かうところへまっすぐに行き、霊の行くところへ彼らも行き、その行く時は回らない。
Zamoyozo zinkayenda molunjika kutsogolo. Kulikonse kumene mzimu umazitsogolera kupita, nazonso zimapita kumeneko, osatembenuka pamene zikupita.
13 この生きもののうちには燃える炭の火のようなものがあり、たいまつのように、生きものの中を行き来している。火は輝いて、その火から、いなずまが出ていた。
Pakati pa zamayozo panali chinthu chooneka ngati makala oyaka kapena miyuni yoyaka. Moto umayendayenda pakati pa zamayozo; wowala kwambiri, ndipo mphenzi zimatuluka pakati pawo.
14 生きものは、いなずまのひらめきのように速く行き来していた。
Zamoyozo zinkathamanga uku ndi uko ngati kungʼanima kwa mphenzi.
15 わたしが生きものを見ていると、生きもののかたわら、地の上に輪があった。四つの生きものおのおのに、一つずつの輪である。
Pamene ndinali kuyangʼana zamoyozo, ndinangoona mikombero ndipo pansi pambali pa chamoyo chilichonse panali mkombero umodzi.
16 もろもろの輪の形と作りは、光る貴かんらん石のようである。四つのものは同じ形で、その作りは、あたかも、輪の中に輪があるようである。
Maonekedwe a mikomberoyo anali ngati mwala wonyezimira. Mikombero yonse inali yofanana ndipo mapangidwe awo anali ngati wongolowanalowana.
17 その行く時、彼らは四方のいずれかに行き、行く時は回らない。
Mikombero ija poyenda inkatha kupita mbali iliyonse yomwe zamoyozo zinayangʼana popanda kutembenuka.
18 四つの輪には輪縁と輻とがあり、その輪縁の周囲は目をもって満たされていた。
Marimu a mikomberoyo anali aatali ndi ochititsa mantha ndipo marimu onse anayi anali ndi maso ponseponse.
19 生きものが行く時には、輪もそのかたわらに行き、生きものが地からあがる時は、輪もあがる。
Zamoyozo zinkati zikamayenda, mikomberoyo imayendanso mʼmbali mwake; ndipo zamoyozo zinkati zikamakwera mmwamba, mikomberoyo imakweranso.
20 霊の行く所には彼らも行き、輪は彼らに伴ってあがる。生きものの霊が輪の中にあるからである。
Kulikonse kumene mzimu wake unkazitsogolera, zamoyozo zinkapita komweko. Ndipo mikombero ija inkapita nawo pamodzi popeza kuti mzimu wa zamoyozo ndiwo umayendetsa mikombero ija.
21 彼らが行く時は、これらも行き、彼らがとどまる時は、これらもとどまり、彼らが地からあがる時は、輪もまたこれらと共にあがる。生きものの霊が輪の中にあるからである。
Zamoyo zija zinkati zikamayenda mikombero imayendanso. Zamoyozo zimati zikayima, nayonso mikombero inkayima. Zamoyozo zinkati zikawuluka, mikomberonso imawuluka nazo pamodzi chifukwa mzimu wa zamoyo zija ndiwo umayendetsa mikombero ija.
22 生きものの頭の上に水晶のように輝く大空の形があって、彼らの頭の上に広がっている。、
Pamwamba pa mitu ya zamoyozo panali chinthu chonga thambo, lowala ndipo kunyezimira kwake ngati galasi loyangʼanitsa ku dzuwa, loyalidwa pamwamba pa mitu yake.
23 大空の下にはまっすぐに伸ばした翼があり、たがいに相連なり、生きものはおのおの二つの翼をもって、からだをおおっている。
Zamoyozo zinatambalitsa mapiko ake mʼmunsi mwa thambo lija, mapiko ake ena kumakhudzana, mapiko awiri kumaphimba thupi lake.
24 その行く時、わたしは大水の声、全能者の声のような翼の声を聞いた。その声の響きは大軍の声のようで、そのとどまる時は翼をたれる。
Pamene zamoyo zimayenda ndimamva phokoso la mapiko ake, ngati mkokomo wa madzi ambiri, ngati liwu la Wamphamvuzonse, ngati phokoso la gulu lankhondo. Zimati zikayima zinkagwetsa mapiko ake.
25 また彼らの頭の上の大空から声があった。彼らが立ちとどまる時は翼をおろした。
Ndipo panamveka mawu kuchokera pamwamba pa thambo la pa mitu ya zamoyo zija. Nthawi iyi nʼkuti zamoyozo zitayima ndi kugwetsa pansi mapiko ake.
26 彼らの頭の上の大空の上に、サファイヤのような位の形があった。またその位の形の上に、人の姿のような形があった。
Pamwamba pa thambo la pa mitu yake panali chinthu chimene chimaoneka ngati mpando waufumu wopangidwa ndi mwala wa safiro, ndipo pamwamba pa mpando waufumuwo panali chinthu chooneka ngati munthu.
27 そしてその腰とみえる所の上の方に、火の形のような光る青銅の色のものが、これを囲んでいるのを見た。わたしはその腰とみえる所の下の方に、火のようなものを見た。そして彼のまわりに輝きがあった。
Ndinaona kuti mmwamba mwa chiwuno chake munali ngati chitsulo chowala konsekonse ngati moto. Mʼmunsi mwa chiwuno chake munalinso ngati moto wokhawokha. Kuwala kwa mphamvu kunamuzungulira munthuyo.
28 そのまわりにある輝きのさまは、雨の日に雲に起るにじのようであった。主の栄光の形のさまは、このようであった。わたしはこれを見て、わたしの顔をふせたとき、語る者の声を聞いた。
Kuwalako kunali ndi maonekedwe a utawaleza mʼmitambo tsiku limene kwagwa mvula. Umu ndi mmene ulemerero wa Yehova umaonekera. Pamene ndinawuona ndinagwa pansi ndipo ndinamva mawu akundiyankhula.

< エゼキエル書 1 >