< アモス書 5 >

1 イスラエルの家よ、わたしが悲しみの歌をもって、あなたがたについて宣べるこの言葉を聞け、
Israeli, imva mawu awa, nyimbo ya maliro imene ndikuyimba za iweyo:
2 「おとめイスラエルは倒れて、また起き上がらず、彼女はおのれの地に投げ倒されてこれを起す者がない」。
“Namwali Israeli wagwa, moti sadzadzukanso, wasiyidwa mʼdziko lake lomwe, popanda woti ndi kumudzutsa.”
3 主なる神はこう言われる、「イスラエルの家では、千人出た町は百人残り、百人出た町は十人残る」。
Ambuye Yehova akuti, “Mzinda umene udzapite ku nkhondo ndi anthu 1,000 amphamvu udzatsala ndi anthu 100 okha; mzinda umene udzapite ku nkhondo ndi anthu 100 amphamvu udzatsala ndi anthu khumi okha basi.”
4 主はイスラエルの家にこう言われる、「あなたがたはわたしを求めよ、そして生きよ。
Zimene Yehova akunena kwa nyumba ya Israeli ndi izi: “Mundifunefune kuti mukhale ndi moyo;
5 ベテルを求めるな、ギルガルに行くな。ベエルシバにおもむくな。ギルガルは必ず捕えられて行き、ベテルは無に帰するからである」。
musafunefune Beteli, musapite ku Giligala, musapite ku Beeriseba. Pakuti Giligala adzatengedwa ndithu kupita ku ukapolo, ndipo Beteli adzawonongekeratu.”
6 あなたがたは主を求めよ、そして生きよ。さもないと主は火のようにヨセフの家に落ち下られる。火はこれを焼くが、ベテルのためにこれを消す者はひとりもない。
Funani Yehova kuti mukhale ndi moyo, mukapanda kutero Iye adzatentha nyumba ya Yosefe ngati moto; motowo udzawononga, ndipo sipadzakhala wina wozimitsa motowo ku Beteli.
7 あなたがた、公道をにがよもぎに変え、正義を地に投げ捨てる者よ。
Inu amene mumasandutsa chiweruzo cholungama kukhala chowawa ndi kunyoza chilungamo.
8 プレアデスおよびオリオンを造り、暗黒を朝に変じ、昼を暗くして夜となし、海の水を呼んで、地のおもてに注がれる者、その名は主という。
(Iye amene analenga nyenyezi za Nsangwe ndi Akamwiniatsatana, amene amasandutsa mdima kuti ukhale mmawa ndi kudetsa usana kuti ukhale usiku, amene amayitana madzi a mʼnyanja ndi kuwathira pa dziko lapansi, Yehova ndiye dzina lake.
9 主は滅びをたちまち強い者に臨ませられるので、滅びはついに城に臨む。
Iyeyo amabweretsa chiwonongeko modzidzimutsa pa anthu amphamvu ndi kuwononga mizinda yotetezedwa),
10 彼らは門にいて戒める者を憎み、真実を語る者を忌みきらう。
inu mumadana ndi amene amadzudzula mʼbwalo la milandu ndi kunyoza amene amanena zoona.
11 あなたがたは貧しい者を踏みつけ、彼から麦の贈り物をとるゆえ、あなたがたは切り石の家を建てても、その中に住むことはできない。美しいぶどう畑を作っても、その酒を飲むことはできない。
Mumapondereza munthu wosauka ndi kumukakamiza kuti akupatseni tirigu. Nʼchifukwa chake, ngakhale mwamanga nyumba zamiyala yosema, inuyo simudzakhalamo. Ngakhale mwalima minda yabwino ya mphesa, inu simudzamwa vinyo wake.
12 わたしは知る、あなたがたのとがは多く、あなたがたの罪は大きいからである。あなたがたは正しい者をしえたげ、まいないを取り、門で貧しい者を退ける。
Pakuti Ine ndikudziwa kuchuluka kwa zolakwa zanu ndi kukula kwa machimo anu. Inu mumapondereza anthu olungama ndi kulandira ziphuphu ndipo anthu osauka simuwaweruza mwachilungamo mʼmabwalo anu amilandu.
13 それゆえ、このような時には賢い者は沈黙する、これは悪い時だからである。
Nʼchifukwa chake pa nthawi yotere munthu wanzeru sayankhulapo kanthu, popeza ndi nthawi yoyipa.
14 善を求めよ、悪を求めるな。そうすればあなたがたは生きることができる。またあなたがたが言うように、万軍の神、主はあなたがたと共におられる。
Muyike mtima wanu pa zabwino osati pa zoyipa, kuti mukhale ndi moyo. Mukatero Yehova Mulungu Wamphamvuzonse adzakhala nanu, monga mmene mumanenera kuti ali nanu.
15 悪を憎み、善を愛し、門で公義を立てよ。万軍の神、主は、あるいはヨセフの残りの者をあわれまれるであろう。
Mudane ndi zoyipa, mukonde zabwino; mukhazikitse chiweruzo cholungama mʼmabwalo anu amilandu. Mwina mwake Yehova Mulungu Wamphamvuzonse adzachitira chifundo anthu otsala a mʼbanja la Yosefe.
16 それゆえ、主なる万軍の神、主はこう言われる、「すべての広場で泣くことがあろう。すべてのちまたで人々は『悲しいかな、悲しいかな』と言う。また彼らは農夫を呼んできて嘆かせ、巧みな泣き女を招いて泣かせ、
Choncho izi ndi zimene Ambuye, Yehova Mulungu Wamphamvuzonse, akunena: “Mʼmisewu monse mudzakhala kulira mofuwula, ndi kulira chifukwa cha kuwawa kwa masautso kudzakhala paliponse. Adzayitana alimi kuti adzalire, ndipo anthu odziwa maliridwe anthetemya adzalira mofuwula.
17 またすべてのぶどう畑にも泣くことがあろう。それはわたしがあなたがたの中を通るからである」と主は言われる。
Mʼminda yonse ya mpesa mudzakhala kulira kokhakokha, pakuti Ine ndidzadutsa pakati panu,” akutero Yehova.
18 わざわいなるかな、主の日を望む者よ、あなたがたは何ゆえ主の日を望むのか。これは暗くて光がない。
Tsoka kwa inu amene mumalakalaka tsiku la Yehova! Chifukwa chiyani mumalakalaka tsiku la Yehova? Tsikulo kudzakhala mdima osati kuwala.
19 人がししの前を逃れてもくまに出会い、また家にはいって、手を壁につけると、へびにかまれるようなものである。
Lidzakhala ngati tsiku limene munthu pothawa mkango amakumana ndi chimbalangondo, ngati pamene munthu walowa mʼnyumba, natsamira dzanja lake pa khoma ndipo njoka nʼkuluma.
20 主の日は暗くて、光がなく、薄暗くて輝きがないではないか。
Kodi tsiku la Yehova silidzakhala mdima osati kuwala, mdima wandiweyani, popanda powala pena paliponse?
21 わたしはあなたがたの祭を憎み、かつ卑しめる。わたしはまた、あなたがたの聖会を喜ばない。
“Ndimadana nawo masiku anu achikondwerero ndipo ndimawanyoza; sindikondwera nayo misonkhano yanu.
22 たといあなたがたは燔祭や素祭をささげても、わたしはこれを受けいれない。あなたがたの肥えた獣の酬恩祭はわたしはこれを顧みない。
Ngakhale mupereke nsembe zopsereza ndi nsembe zachakudya, Ine sindidzazilandira. Ngakhale mupereke nsembe zabwino zachiyanjano, Ine sindidzaziyangʼana nʼkomwe.
23 あなたがたの歌の騒がしい音をわたしの前から断て。あなたがたの琴の音は、わたしはこれを聞かない。
Musandisokose nazo nyimbo zanu! Sindidzamvetsera kulira kwa azeze anu.
24 公道を水のように、正義をつきない川のように流れさせよ。
Koma chiweruzo cholungama chiyende ngati madzi, chilungamo ngati mtsinje wosaphwa!
25 「イスラエルの家よ、あなたがたは四十年の間、荒野でわたしに犠牲と供え物をささげたか。
“Kodi pa zaka makumi anayi zimene munakhala mʼchipululu muja munkandibweretsera nsembe ndi zopereka, inu nyumba ya Israeli?
26 かえってあなたがたの王シクテをにない、あなたがたが自分で作ったあなたがたの偶像、星の神、キウンをになった。
Inu mwanyamula kachisi wa mfumu yanu, ndi nyenyezi ija Kaiwani, mulungu wanu, mafano amene munadzipangira.
27 それゆえわたしはあなたがたをダマスコのかなたに捕え移す」と、その名を万軍の神ととなえられる主は言われる。
Nʼchifukwa chake Ine ndidzakupititsani ku ukapolo, kutali kupitirira ku Damasiko,” akutero Yehova, amene dzina lake ndi Mulungu Wamphamvuzonse.

< アモス書 5 >