< ゼカリヤ書 8 >

1 萬軍のヱホバの言われに臨めり曰く
Awa ndi mawu amene Yehova Wamphamvuzonse ananena.
2 萬軍のヱホバかく言たまふ我シオンのために甚だしく心を熱して妬く思ひ大なる忿怒を起して之がために妬く思ふ
Yehova Wamphamvuzonse akuti, “Ine ndikuchitira nsanje yayikulu Ziyoni. Mtima wanga ukupweteka chifukwa cha nsanje pa iyeyo.”
3 ヱホバかく言たまふ今我シオンに歸れり我ヱルサレムの中に住んヱルサレムは誠實ある邑と稱へられ萬軍のヱホバの山は聖山と稱へらるべし
Yehova akuti, “Ndidzabwerera ku Ziyoni ndi kukakhala ku Yerusalemu. Pamenepo Yerusalemu adzatchedwa Mzinda wa Choonadi ndipo phiri la Yehova Wamphamvuzonse lidzatchedwa Phiri Lopatulika.”
4 萬軍のヱホバかく言たまふヱルサレムの街衢には再び老たる男老たる女坐せん皆年高くして各々杖を手に持べし
Yehova Wamphamvuzonse akuti, “Abambo ndi amayi okalamba adzakhalanso mʼmisewu ya mu Yerusalemu, aliyense ali ndi ndodo mʼmanja mwake chifukwa cha kuchuluka kwa masiku ake.
5 またその邑の街衢には男の兒女の兒滿て街衢に遊び戯れん
Ndipo misewu ya mu mzindamo idzadzaza ndi anyamata ndi atsikana akusewera.”
6 萬軍のヱホバかく言たまふこの事その日には此民の遺餘者の目に奇といふとも我目に何の奇きこと有んや萬軍のヱホバこれを言ふ
Yehova Wamphamvuzonse akuti, “Ngati zikuoneka kuti nʼzosatheka kwa anthu otsala pa nthawi ino, kodi zidzakhala zosathekanso kwa Ine?” akutero Yehova Wamphamvuzonse.
7 萬軍のヱホバかく言たまふ視よ我わが民を日の出る國より日の入る國より救ひ出し
Yehova Wamphamvuzonse akuti, “Taonani ndidzapulumutsa anthu anga kuchokera ku mayiko a kummawa ndi kumadzulo.
8 かれらを携へ來りてヱルサレムの中に住しめん彼らは我民となり我は彼らの神となりて共に誠實と正義に居ん
Ndidzawabweretsa kuti adzakhale mu Yerusalemu; adzakhala anthu anga, ndipo Ine ndidzakhala Mulungu wawo, wokhulupirika ndi wolungama pakati pawo.”
9 萬軍のヱホバかく言たまふ汝ら萬軍のヱホバの室なる殿を建んとて其基礎を置たる日に起りし預言者等の口の言詞を今日聞く者よ汝らの腕を強くせよ
Yehova Wamphamvuzonse akuti, “Inu amene tsopano mukumva mawu awa amene akuyankhula aneneri amene analipo pamene ankayika maziko a nyumba ya Yehova Wamphamvuzonse, ‘limbani mtima kuti mumange Nyumba ya Yehova.’
10 此日の先には人も工の價を得ず獸畜も工の價を得ず出者も入者も仇の故をもて安然ならざりき即ち我人々をして互に相攻しめたり
Mpaka nthawi imeneyi panalibe munthu wolandira malipiro pa ntchito kapena ndalama zolipirira nyama zogwira ntchito. Panalibe munthu amene ankadzigwirira ntchito mwamtendere chifukwa choopa adani ake, pakuti Ine ndinkawayambanitsa.
11 然れども今は我此民の遺餘者に對すること曩の日の如くならずと萬軍のヱホバ言たまふ
Koma tsopano sindidzachitira otsala mwa anthu awa zomwe ndinachita kale,” akutero Yehova Wamphamvuzonse.
12 即ち平安の種子あるべし葡萄の樹は果を結び地は產物を出し天は露を與へん我この民の遺餘者にこれを盡く獲さすべし
“Pakuti mbewu zidzamera bwino, mpesa udzabala zipatso zake, nthaka idzatulutsa zomera zake, ndi thambo lidzagwetsa mame. Ndidzapereka zonse kukhala cholowa cha otsala mwa anthu awa.
13 ユダの家およびイスラエルの家よ汝らが國々の中に呪詛となりしごとく此度は我なんぢらを救ふて祝言とならしめん懼るる勿れ汝らの腕を強くせよ
Monga mwakhala muli chinthu chotembereredwa pakati pa mitundu ina ya anthu, inu Yuda ndi Israeli, choncho ndidzakupulumutsani, ndipo mudzakhala dalitso. Musachite mantha, koma limbani mtima.”
14 萬軍のヱホバかく言たまふ在昔汝らの先祖我を怒らせし時に我これに災禍を降さんと思ひて之を悔ざりき萬軍のヱホバこれを言ふ
Yehova Wamphamvuzonse akuti, “Monga ndinatsimikiza mtima kubweretsa choyipa pa inu, komanso osakuchitirani chisoni pamene makolo anu anandikwiyitsa,” akutero Yehova,
15 是のごとく我また今日ヱルサレムとユダの家に福祉を降さんと思ふ汝ら懼るる勿れ
“Choncho tsopano ndatsimikiza mtima kuchitiranso zabwino Yerusalemu ndi Yuda. Musachite mantha.
16 汝らの爲べき事は是なり汝ら各々たがひに眞實を言べし又汝等の門にて審判する時は眞實を執て平和の審判を爲べし
Zinthu zoti muchite ndi izi: Muziwuzana zoona zokhazokha, muziweruza moona ndi mwachilungamo mʼmabwalo anu;
17 汝等すべて人の災害を心に圖る勿れ僞の誓を好む勿れ是等はみな我が惡む者なりとヱホバ言たまふ
musamachitire mnzanu chiwembu, musamakonde kulumbira zonama. Zonsezi Ine ndimadana nazo,” akutero Yehova.
18 萬軍のヱホバの言われに臨めり云く
Yehova Wamphamvuzonse anayankhulanso nane.
19 萬軍のヱホバかく言たまふ四月の斷食五月の斷食七月の斷食十月の斷食かへつてユダの家の宴樂となり欣喜となり佳節となるべし惟なんぢら眞實と平和を愛すべし
Ndipo ananena kuti, “Kusala zakudya kwa pa mwezi wachinayi, chisanu, chisanu ndi chiwiri ndi wakhumi, kudzakhala nthawi yachimwemwe, ya chisangalalo ndi nthawi ya madyerero chikondwerero kwa Yuda. Nʼchifukwa chake muzikonda choonadi ndi mtendere.”
20 萬軍のヱホバかく言たまふ國々の民および衆多の邑の居民來り就ん
Yehova Wamphamvuzonse akuti, “Anthu a mitundu yambiri ndi anthu okhala mʼmizinda yambiri adzabwerabe,
21 即ちこの邑の居民往てかの邑の者に向ひ我儕すみやかに往てヱホバを和め萬軍のヱホバを求めんと言んに我も往べしと答へん
ndipo nzika za mzinda wina zidzapita ku mzinda wina, kukanena kuti, ‘Tiyeni mwamsanga tikapemphe madalitso kwa Yehova ndi kukapembedza Yehova Wamphamvuzonse. Inenso ndikupita kumeneko.’
22 衆多の民強き國民ヱルサレムに來りて萬軍のヱホバを求めヱホバを和めん
Anthu ambiri ndiponso a ku mayiko amphamvu adzabwera ku Yerusalemu kudzapembedza Yehova Wamphamvuzonse ndi kudzapempha madalitso.”
23 萬軍のヱホバかく言たまふ其日には諸の國語の民十人にてユダヤ人一箇の裾を拉へん即ち之を拉へて言ん我ら汝らと與に往べし其は我ら神の汝らと偕にいますを聞たればなり
Yehova Wamphamvuzonse akuti, “Masiku amenewo anthu khumi ochokera ku mitundu ya anthu a ziyankhulo zosiyana adzagwira mkanjo wa Myuda ndi kunena kuti, ‘Tipite nawo, chifukwa tamva kuti Mulungu ali nanu.’”

< ゼカリヤ書 8 >