< ローマ人への手紙 12 >

1 されば兄弟よ、われ神のもろもろの慈悲によりて汝らに勸む、己が身を神の悦びたまふ潔き活ける供物として献げよ、これ靈の祭なり。
Nʼchifukwa chake ine ndikukupemphani abale, mwa chifundo cha Mulungu, kuti mupereke matupi anu monga nsembe yamoyo, yopatulika ndi yokondweretsa Mulungu. Nsembeyi ndiye kupembedza kwanu kwa uzimu.
2 又この世に效ふな、神の御意の善にして悦ぶべく、かつ全きことを辨へ知らんために、心を更へて新にせよ。 (aiōn g165)
Musafanizidwenso ndi makhalidwe a dziko lino koma musandulike pokonzanso maganizo anu. Ndipo mudzadziwa ndi kuzindikira chifuniro chabwino cha Mulungu chomwe ndi chokondweretsa ndi changwiro. (aiōn g165)
3 われ與へられし恩惠によりて汝 等おのおのに告ぐ、思ふべき所を超えて自己を高しとすな。神のおのおのに分ち給ひし信仰の量にしたがひ愼みて思ふべし。
Chifukwa cha chisomo chopatsidwa kwa ine, ndinena kwa aliyense wa inu kuti musadziyenereze nokha kuposa mmene mulili. Koma mudziganizire nokha modzichepetsa, molingana ndi muyeso wa chikhulupiriro chimene Mulungu wakupatsani.
4 人は一つ體におほくの肢あれども、凡ての肢その運用を同じうせぬ如く、
Pakuti monga aliyense wa ife ali ndi thupi limodzi koma ziwalo zambiri, ziwalozi sizili ndi ntchito yofanana.
5 我らも多くあれど、キリストに在りて一つ體にして、各人たがひに肢たるなり。
Momwemonso mwa Khristu ife amene tili ambiri tipanga thupi limodzi ndipo chiwalo chilichonse ndi cholumikizika ku chinzake.
6 われらが有てる賜物はおのおの與へられし恩惠によりて異なる故に、或は預言あらば信仰の量にしたがひて預言をなし、
Ife tili ndi mphatso zosiyana, molingana ndi chisomo chopatsidwa kwa ife. Ngati mphatso ya munthu ndi kunenera, musiyeni ayigwiritse ntchito molingana ndi chikhulupiriro chake.
7 或は務あらば務をなし、或は教をなす者は教をなし、
Ngati ndi kutumikira, musiyeni atumikire. Ngati ndi kuphunzitsa, musiyeni aphunzitse.
8 或は勸をなす者は勸をなし、施す者はをしみなく施し、治むる者は心を盡して治め、憐憫をなす者は喜びて憐憫をなすべし。
Ngati ndi kulimbikitsa, musiyeni alimbikitse. Ngati ndi kupereka kuthandiza osowa, musiyeni apereke mowolowamanja. Ngati ndi utsogoleri, musiyeni alamulire mosamala. Ngati ndi kuonetsa chifundo, musiyeni achite mosangalala.
9 愛には虚僞あらざれ、惡はにくみ、善はしたしみ、
Chikondi chikhale chopanda chinyengo. Dana nacho choyipa; gwiritsitsa chabwino.
10 兄弟の愛をもて互に愛しみ、禮儀をもて相 讓り、
Mukondane kwathunthu monga abale. Lemekezanani wina ndi mnzake kuposa inu eni.
11 勤めて怠らず、心を熱くし、主につかへ、
Musakhale aulesi mʼmachitidwe anu. Khalani achangu mu mzimu ndipo tumikirani Ambuye.
12 望みて喜び、患難にたへ、祈を恆にし、
Kondwerani mʼchiyembekezo, pirirani mʼmasautso ndiponso khulupirikani mʼpemphero.
13 聖徒の缺乏を賑し、旅人を懇ろに待せ、
Gawanani ndi anthu a Mulungu amene ali ndi chosowa. Cherezani alendo.
14 汝らを責むる者を祝し、これを祝して詛ふな。
Adalitseni amene akuzunzani. Adalitseni ndipo musawatemberere.
15 喜ぶ者と共によろこび、泣く者と共になけ。
Kondwani pamodzi ndi amene akukondwa ndipo lirani ndi amene akulira.
16 相 互に心を同じうし、高ぶりたる思をなさず、反つて卑きに附け。なんぢら己を聰しとすな。
Muyanjane wina ndi mnzake. Musakhale onyada, koma lolani kuyanjana ndi anthu wamba. Musaganize kuti mumadziwa zonse.
17 惡をもて惡に報いず、凡ての人のまへに善からんことを圖り、
Musabwezere choyipa ndi choyipa kwa aliyense. Samalitsani kuchita chabwino pamaso pa aliyense.
18 汝らの爲し得るかぎり力めて凡ての人と相 和げ。
Ngati nʼkotheka, khalani mwamtendere ndi aliyense monga momwe mungathere.
19 愛する者よ、自ら復讐すな、ただ神の怒に任せまつれ。録して『主いひ給ふ、復讐するは我にあり、我これに報いん』とあり。
Okondedwa anga, musabwezere choyipa, koma lekerani Mulungu. Pakuti kwalembedwa, “Kubwezera chilango nʼkwanga. Ndidzawalanga ndine,” akutero Ambuye.
20 『もし汝の仇 飢ゑなば之に食はせ、渇かば之に飮ませよ、なんぢ斯するは熱き火を彼の頭に積むなり』
Koma, “Ngati mdani wako ali ndi njala, mupatse chakudya. Ngati ali ndi ludzu, mupatse kanthu kakumwa. Pochita ichi, udzamuwunjikira makala amoto pamutu pake.”
21 惡に勝たるることなく、善をもて惡に勝て。
Musagonjetsedwe ndi choyipa, koma gonjetsani choyipa pochita chabwino.

< ローマ人への手紙 12 >