< ヨハネの黙示録 17 >
1 七つの鉢を持てる七人の御使の一人きたり、我に語りて言ふ『來れ、われ多くの水の上に坐する大淫婦の審判を汝に示さん。
Mmodzi wa angelo asanu ndi awiri aja amene anali ndi mbale zisanu ndi ziwiri anadza nati kwa ine, “Bwera ndikuonetse chilango cha mkazi wadama wotchuka uja amene akukhala pambali pa madzi ambiri.
2 地の王たちは之と淫をおこなひ、地に住む者らは其の淫行の葡萄酒に醉ひたり』
Mafumu a dziko lapansi amachita naye chigololo ndipo okhala pa dziko lapansi analedzera ndi vinyo wa zigololo zake.”
3 かくてわれ御靈に感じ、御使に携へられて荒野にゆき、緋色の獸に乘れる女を見たり、この獸の體は神を涜す名にて覆はれ、また七つの頭と十の角とあり。
Kenaka mngeloyo anandinyamula mwa Mzimu Woyera kupita nane ku chipululu. Kumeneko ndinaona mkazi atakhala pa chirombo chofiira chokutidwa ndi mayina a chipongwe ndipo chinali ndi mitu isanu ndi iwiri ndi nyanga khumi.
4 女は紫色と緋とを著、金・寶石・眞珠にて身を飾り、手には憎むべきものと己が淫行の汚とにて滿ちたる金の酒杯を持ち、
Mkaziyo anavala zovala za pepo ndi zofiira nadzikongoletsa ndi golide, miyala yapamwamba ndi ngale. Ananyamula chikho chagolide mʼdzanja lake, chodzaza ndi zinthu zonyansa ndi fungo loyipa la zigololo zake.
5 額には記されたる名あり。曰く『奧義 大なるバビロン、地の淫婦らと憎むべき者との母』
Pa mphumi pake panalembedwa dzina lodabwitsa: BABULONI WAMKULU MAYI WA AKAZI ADAMA NDI WAZOYIPITSA ZA DZIKO LAPANSI.
6 我この女を見るに、聖徒の血とイエスの證人の血とに醉ひたり。我これを見て大に怪しみたれば、
Ndinaona kuti mkaziyo anali ataledzera ndi magazi a oyera mtima, magazi a amene anachitira umboni Yesu. Nditamuona mkaziyo ndinadabwa kwambiri.
7 御使われに言ふ『なにゆゑ怪しむか、我この女と之を乘せたる七つの頭、十の角ある獸との奧義を汝に告げん。
Kenaka mngelo uja anati kwa ine, “Bwanji ukudabwa? Ndikufotokozera chinsinsi cha mkaziyu ndi chinsinsi cha chirombo chimene wakwerapochi chokhala ndi mitu isanu ndi iwiri ndi nyanga khumi.
8 なんぢの見し獸は前に有りしも今あらず、後に底なき所より上りて滅亡に往かん、地に住む者にて世の創より其の名を生命の書に記されざる者は、獸の前にありて今あらず、後に來るを見て怪しまん。 (Abyssos )
Chirombo chimene wachionachi chinalipo kale koma tsopano kulibe ndipo chidzatuluka ku chidzenje chakuya ndi kupita kukawonongedwa. Anthu okhala pa dziko lapansi amene mayina awo sanalembedwe mʼbuku lamoyo kuyambira pa kulengedwa kwa dziko lapansi adzadabwa pamene adzaona chirombocho, chifukwa chinalipo kale, tsopano kulibe, komabe chidzabwera. (Abyssos )
9 智慧の心は茲にあり。七つの頭は女の坐する七つの山なり、また七人の王なり。
“Zimenezi zikufunika kuganizira mwanzeru. Mitu isanu ndi iwiriyo ndi mapiri asanu ndi awiri pomwe mkazi uja amakhalirapo. Yomweyonso ndi mafumu asanu ndi awiri.
10 五 人は既に倒れて一人は今あり、他の一人は未だ來らず、來らば暫時のほど止るべきなり。
Mafumu asanu anagwa, imodzi ilipo ndipo ina sinabwere; koma pamene idzafika, idzayenera kukhala kwa kanthawi kochepa.
11 前にありて今あらぬ獸は第八なり、前の七人より出でたる者にして滅亡に往くなり。
Chirombo chomwe chinalipo kale ndipo tsopano kulibe ndiyo mfumu yachisanu ndi chitatu. Iyo ndi ya mʼgulu la asanu ndi awiriwo ndipo ikupita kukawonongedwa.
12 汝の見し十の角は十 人の王にして未だ國を受けざれども、一時のあひだ獸と共に王のごとき權威を受くべし。
“Nyanga khumi unaziona zija ndi mafumu khumi amene sanapatsidwe ulamuliro, koma adzapatsidwa ulamuliro pamodzi ndi chirombo kwa ora limodzi.
13 彼らは心を一つにして己が能力と權威とを獸にあたふ。
Mafumuwo ali ndi cholinga chimodzi ndipo adzapereka mphamvu ndi ulamuliro wawo kwa chirombocho.
14 彼らは羔羊と戰はん。而して羔羊かれらに勝ち給ふべし、彼は主の主、王の王なればなり。これと偕なる召されたるもの、選ばれたるもの、忠實なる者も勝を得べし』
Iwo adzachita nkhondo ndi Mwana Wankhosa, koma Mwana Wankhosayo adzawagonjetsa chifukwa Iye ndi Mbuye wa ambuye ndi Mfumu ya mafumu, ndipo amene adzakhala ndi Iye ndi oyitanidwa ake, osankhidwa ndi otsatira ake okhulupirika.”
15 御使また我に言ふ『なんぢの見し水、すなわち淫婦の坐する處は、もろもろの民・群衆・國・國語なり。
Kenaka mngeloyo anati kwa ine, “Madzi amene unawaona pamene mkazi wadamayo anakhalapo ndiwo anthu ochuluka, mitundu ndi ziyankhulo.
16 なんぢの見し十の角と獸とは、かの淫婦を憎み、之をして荒涼ばしめ、裸ならしめ、且その肉を喰ひ、火をもて之を燒き盡さん。
Nyanga khumi ndi chirombo unazionazo zidzadya mkazi wadamayo. Zidzamufwifwitsa ndi kumusiya wamaliseche; zidzadya nyama yake ndi kumutentha ndi moto.
17 神は彼らに御旨を行ふことと、心を一つにすることと、神の御言の成就するまで國を獸に與ふることとを思はしめ給ひたればなり。
Pakuti Mulungu wayika ichi mʼmitima mwawo kuti akwaniritse cholinga chake povomerezana kupereka mphamvu zawo zolamulira kwa chirombo, kufikira Mawu a Mulungu atakwaniritsidwa.
18 なんぢの見し女は地の王たちを宰どる大なる都なり』
Mkazi unamuonayo ndi mzinda waukulu umene ulamulira mafumu a dziko lapansi.”