< ピリピ人への手紙 1 >

1 キリスト・イエスの僕たる我ら、パウロとテモテと、書をピリピにをるキリスト・イエスに在る凡ての聖徒、および監督たちと執事たちとに贈る。
Paulo ndi Timoteyo, atumiki a Khristu Yesu. Kulembera anthu onse oyera mtima a ku Filipi amene ali mwa Khristu Yesu, pamodzi ndi oyangʼanira ndi atumiki awo.
2 願はくは我らの父なる神および主イエス・キリストより賜ふ恩惠と平安と汝らに在らんことを。
Chisomo ndi mtendere zochokera kwa Mulungu Atate athu ndi Ambuye Yesu Khristu zikhale kwa inu.
3 われ汝らを憶ふごとに、我が神に感謝し、
Ndimayamika Mulungu wanga nthawi zonse ndikakumbukira inu.
4 常に汝ら衆のために、願のつどつど喜びて願をなす。
Mʼmapemphero anga onse opempherera inu, nthawi zonse ndimapemphera ndi chimwemwe
5 是なんぢら初の日より今に至るまで、福音を弘むることに與るが故なり。
chifukwa mwakhala mukundithandiza polalikira Uthenga Wabwino kuyambira tsiku loyamba mpaka tsopano.
6 我は汝らの衷に善き業を始め給ひし者の、キリスト・イエスの日まで之を全うし給ふべきことを確信す。
Sindikukayika konse kuti Iye amene anayamba ntchito yabwino mwa inu adzayipitiriza ndi kuyimaliza mpaka pa tsiku la kubweranso kwa Khristu Yesu.
7 わが斯くも汝ら衆を思ふは當然の事なり、我が縲絏にある時にも、福音を辯明して之を堅うする時にも、汝らは皆われと共に恩惠に與るによりて、我が心にあればなり。
Kwa ine ndi bwino kuti ndiziganiza zotere za nonsenu, popeza ndimakukondani, ngakhale ndikhale mʼndende, kapena pamene ndikuteteza ndi kukhazikitsa Uthenga Wabwino, inu nonse mumagawana nane chisomo cha Mulungu.
8 我いかにキリスト・イエスの心をもて汝ら衆を戀ひ慕ふか、その證をなし給ふ者は神なり。
Mulungu angandichitire umboni kuti ndimakulakalakani ndi chikondi cha Khristu Yesu.
9 我は祈る、汝らの愛、知識ともろもろの悟とによりて彌が上にも増し加はり、
Ndipo pemphero langa ndi lakuti chikondi chanu chipitirire kukulirakulira pa chidziwitso ndi kuzama mʼmaganizo,
10 善惡を辨へ知り、キリストの日に至るまで潔よくして躓くことなく、
kuti mukhoza kuzindikira chabwino koposa zonse ndi chiti kuti muthe kukhala wopanda chodetsa ndi wopanda chilema kufikira tsiku la Khristu.
11 イエス・キリストによる義の果を充して、神の榮光と譽とを顯さん事を。
Ndipo moyo wanu udzakhala odzazidwa ndi chipatso cha chilungamo chimene chimachokera mwa Yesu Khristu. Pakuti zimenezi zidzapereka ulemerero ndi matamando kwa Mulungu.
12 兄弟よ、我はわが身にありし事の反つて福音の進歩の助となりしを汝らが知らんことを欲するなり。
Tsopano abale, ndikufuna mudziwe kuti chimene chandichitikira ine chathandiza kwambiri kupititsa patsogolo Uthenga Wabwino.
13 即ち我が縲絏のキリストの爲なることは、近衞の全營にも、他の凡ての人にも顯れ、
Chotsatira chake nʼchakuti zadziwika bwino lomwe kwa onse amene ali ku nyumba yaufumu kuti ine ndili mʼmaunyolo chifukwa cha Khristu.
14 かつ兄弟のうちの多くの者は、わが縲絏によりて主を信ずる心を厚くし、懼るる事なく、ますます勇みて神の言を語るに至れり。
Moti chifukwa cha maunyolo angawa, abale ambiri alimbikitsidwa kuyankhula Mawu a Mulungu molimbika ndi mopanda mantha.
15 或 者は嫉妬と分爭とによりてキリストを宣傳へ、あるものは善き心によりて之を宣傳ふ。
Nʼzoonadi kuti ena amalalikira Khristu chifukwa cha kaduka ndi mikangano, koma ena chifukwa cha zolinga zabwino.
16 これは福音を辯明するために我が立てられたることを知り、愛によりてキリストを宣べ、
Olalikira ndi zolinga zabwinowa amachita izi mwachikondi, podziwa kuti ine ndili muno chifukwa cha kuteteza Uthenga Wabwino.
17 かれは我が縲絏に患難を加へんと思ひ、誠意によらず、徒黨によりて之を宣ぶ。
Ena aja amalalikira Khristu modzikonda osati moona mtima namaganiza kuti kutero kubweretsa mavuto pamene ndili mʼmaunyolo.
18 さらば如何、外貌にもあれ、眞にもあれ、孰も宣ぶる所はキリストなれば、我これを喜ぶ、また之を喜ばん。
Nanga kodi zimenezo zili ndi ntchito? Chofunika ndi chakuti Khristu alalikidwe, kaya ndi mwachinyengo kapena moona. Ndipo ndikukondwera chifukwa cha chimenechi. Ndithu, ndidzapitirira kukondwera,
19 そは此のことの汝らの祈とイエス・キリストの御靈の賜物とによりて、我が救となるべきを知ればなり。
pakuti ndikudziwa kuti chifukwa cha mapemphero anu ndi thandizo lochokera kwa Mzimu wa Yesu Khristu, zimene zandionekera zidzathandiza kuti ndimasulidwe.
20 これは我が何事をも恥ぢずして、今も常のごとく聊かも臆することなく、生くるにも、死ぬるにも、我が身によりてキリストの崇められ給はんことを切に願ひ、また望むところに適へるなり。
Ndili ndi chiyembekezo chonse kuti sindidzachita manyazi ndi pangʼono pomwe, koma ndidzakhala ndi chilimbikitso chokwanira kuti monga mwa nthawi zonse, tsopano Khristu adzakwezedwa mʼthupi langa kaya ndi mʼmoyo kapena mu imfa.
21 我にとりて、生くるはキリストなり、死ぬるもまた益なり。
Pakuti kwa ine kukhala moyo ndi Khristu ndipo kufa ndi phindu.
22 されど若し肉體にて生くる事わが勤勞の果となるならば、孰を選ぶべきか、我これを知らず。
Ngati nditi ndipitirire kukhala ndi moyo mʼthupi ndiye kuti kwa ine ndi kugwira ntchito yopindulitsa. Kodi ndisankhe chiyani? Sindikudziwa.
23 我はこの二つの間に介まれたり。わが願は世を去りてキリストと偕に居らんことなり、これ遙に勝るなり。
Ndathinidwa ndi zinthu ziwirizi: Ndikulakalaka kunyamuka kuti ndikakhale ndi Khristu, chimene ndi chinthu chabwino kwambiri.
24 されど我なほ肉體に留るは汝らの爲に必要なり。
Komanso nʼkofunika kwambiri kuti ndikhalebe mʼthupi chifukwa cha inu.
25 我これを確信する故に、なほ存へて汝らの信仰の進歩と喜悦とのために、汝 等すべての者と偕に留らんことを知る。
Ndili ndi chitsimikizo, ndikudziwa kuti ndidzakhala ndi moyo ndipo ndidzapitirira nanu kuti nonse mupite mʼtsogolo ndi kukhala ndi chimwemwe mu chikhulupiriro
26 これは我が再び汝らに到ることにより、汝らキリスト・イエスに在りて我にかかはる誇を増さん爲なり。
kuti pokhala nanunso, kudzitamandira kwanu mwa Khristu Yesu kudzasefukire chifukwa cha ine.
27 汝 等ただキリストの福音に相應しく日を過せ、さらば我が往きて汝らを見るも、離れゐて汝らの事をきくも、汝らが靈を一つにして堅く立ち、心を一つにして福音の信仰のために共に戰ひ、
Chilichonse chimene chingachitike, chachikulu nʼchakuti mukhale moyo ofanana ndi Uthenga Wabwino wa Khristu. Tsono ngati ndingabwere kudzakuonani kapena kumangomva za inu ndili kutali, ndidzadziwa kuti mwayima mwamphamvu mwa Mzimu mmodzi, kulimbika pamodzi ngati munthu mmodzi chifukwa cha chikhulupiriro cha Uthenga Wabwino
28 凡ての事において逆ふ者に驚かされぬを知ることを得ん。その驚かされぬは、彼らには亡の兆、なんぢらには救の兆にて、此は神より出づるなり。
osachita mantha ndi pangʼono pomwe ndi amene akutsutsana nanu. Ichi ndi chizindikiro kwa iwo kuti adzawonongedwa, koma inu mudzapulumutsidwa ndi Mulungu.
29 汝 等はキリストのために啻に彼を信ずる事のみならず、また彼のために苦しむ事をも賜はりたればなり。
Pakuti inu mwapatsidwa mwayi osati ongokhulupirira Khristu kokha, koma wakumva zowawa mʼmalo mwa Khristu.
30 汝らが遭ふ戰鬪は、曩に我の上に見しところ、今また我に就きて聞くところに同じ。
Inunso mukudutsa mʼzowawa zomwe zija munaona ndikudutsamo inenso ndipo pano mukumva kuti ndikukumana nazobe.

< ピリピ人への手紙 1 >