< イザヤ書 35 >
1 荒野とうるほひなき地とはたのしみ 沙漠はよろこびて番紅の花のごとくに咲かがやかん
Chipululu ndi dziko lopanda madzi zidzasangalala; dziko lowuma lidzakondwa ndi kuchita maluwa.
2 盛に咲かがやきてよろこび且よろこび且うたひ レバノンの榮をえカルメルおよびシヤロンの美しきを得ん かれらはヱホバのさかえを見われらの神のうるはしきを見るべし
Dzikolo lidzakhala ndi maluwa ochuluka lidzasangalala kwambiri ndi kufuwula mwachimwemwe. Lidzakhala ndi ulemerero monga wa ku mapiri a ku Lebanoni, maonekedwe ake wokongola adzakhala ngati a ku Karimeli ndi a ku Saroni. Aliyense adzaona ulemerero wa Yehova, ukulu wa Mulungu wathu.
3 なんぢら萎たる手をつよくし弱りたる膝をすこやかにせよ
Limbitsani manja ofowoka, limbitsani mawondo agwedegwede;
4 心さわがしきものに對ていへ なんぢら雄々しかれ懼るるなかれ なんぢらの神をみよ 刑罰きたり神の報きたらん 神きたりてなんぢらを救ひたまふべし
nenani kwa a mitima yamantha kuti; “Limbani mtima, musachite mantha; Mulungu wanu akubwera, akubwera kudzalipsira; ndi kudzabwezera chilango adani anu; akubwera kudzakupulumutsani.”
5 そのとき瞽者の目はひらけ聾者の耳はあくことを得べし
Pamenepo maso a anthu osaona adzapenyanso ndipo makutu a anthu osamva adzatsekuka.
6 そのとき跛者は鹿の如くにとびはしり唖者の舌はうたうたはん そは荒野に水わきいで沙漠に川ながるべければなり
Anthu olumala adzalumpha ngati mbawala, ndipo osayankhula adzayimba mokondwera. Akasupe adzatumphuka mʼchipululu ndipo mitsinje idzayenda mʼdziko lowuma,
7 やけたる沙は池となり うるほひなき地はみづの源となり 野犬のふしたるすみかは蘆葦のしげりあふ所となるべし
mchenga wotentha udzasanduka dziwe, nthaka yowuma idzasanduka ya akasupe. Pamene panali mbuto ya ankhandwe padzamera udzu ndi bango.
8 かしこに大路あり そのみちは聖道ととなへられん 穢れたるものはこれを過ることあたはず ただ主の民のために備へらる これを歩むものはおろかなりとも迷ふことなし
Ndipo kumeneko kudzakhala msewu waukulu; ndipo udzatchedwa Msewu Wopatulika. Anthu odetsedwa sadzayendamo mʼmenemo; zitsiru sizidzasochera mʼmenemo.
9 かしこに獅をらず あらき獸もその路にのぼることなし 然ばそこにて之にあふ事なかるべし ただ贖はれたる者のみそこを歩まん
Kumeneko sikudzakhala mkango, ngakhale nyama yolusa sidzafikako; sidzapezeka konse kumeneko. Koma okhawo amene Yehova anawapulumutsa adzayenda mu msewu umenewu.
10 ヱホバに贖ひすくはれし者うたうたひつつ歸てシオンにきたり その首にとこしへの歡喜をいただき樂とよろこびとをえん 而して悲哀となげきとは逃さるべし
Iwo amene Yehova anawawombola adzabwerera. Adzalowa mu mzinda wa Ziyoni akuyimba; kumeneko adzakondwa mpaka muyaya. Adzakutidwa ndi chisangalalo ndi chimwemwe, ndipo chisoni ndi kudandaula zidzatheratu.