< ヘブル人への手紙 6 >
1 この故に我らはキリストの教の初歩に止ることなく、再び死にたる行爲の悔改と神に對する信仰との基、
Tsono tiyeni tisangoyima pa maphunziro oyambirira enieni a Khristu koma tipitirire kuti mukule msinkhu. Tisaphunzitsenso zinthu zomwe zili ngati maziko, monga za kutembenuka mtima kusiya ntchito zosapindulitsa pa moyo wosatha, za kukhulupirira Mulungu,
2 また各樣のバプテスマと按手と、死人の復活と永遠の審判との教の基を置かずして完全に進むべし。 (aiōnios )
za maubatizo, za kusanjika manja, za kuuka kwa akufa ndi za chiweruzo chotsiriza. (aiōnios )
Ndipo Mulungu akalola, tidzaterodi.
4 一たび照されて天よりの賜物を味ひ、聖 靈に與る者となり、
Nʼkosatheka kuwabwezanso anthu amene nthawi ina anawunikiridwa. Iwowa analawapo mphatso yochokera kumwamba, nʼkulandira nawo Mzimu Woyera.
5 神の善き言と來世の能力とを味ひて後、 (aiōn )
Analawa kukoma kwa mawu a Mulungu ndi mphamvu za nthawi ikubwera. (aiōn )
6 墮落する者は更にまた自ら神の子を十字架に釘けて肆し者とする故に、再びこれを悔改に立返らすること能はざるなり。
Popeza anabwerera mʼmbuyo, nʼkosatheka kuti atembenukenso mtima chifukwa akupachikanso Mwana wa Mulungu ndi kumunyozetsa poyera.
7 それ地しばしば其の上に降る雨を吸ひ入れて耕す者の益となるべき作物を生ぜば、神より祝福を受く。
Nthaka yolandira mvula kawirikawiri nʼkubala mbewu zopindulitsa oyilima, Mulungu amayidalitsa.
8 されど茨と薊とを生ぜば、棄てられ、かつ詛に近く、その果ては焚かるるなり。
Koma nthaka yobereka minga ndi nthula ndi yopanda phindu ndipo ili pafupi kutembereredwa. Matsiriziro ake idzatenthedwa mʼmoto.
9 愛する者よ、われら斯くは語れど、汝らには更に善きこと、即ち救にかかはる事あるを深く信ず。
Okondedwa anga, ngakhale tikuyankhula zimenezi, ife tikudziwa kuti muli nazo zinthu zabwino zomwe zimabwera pamodzi ndi chipulumutso.
10 神は不義に在さねば、汝らの勤勞と、前に聖徒につかへ、今もなほ之に事へて御名のために顯したる愛とを忘れ給ふことなし。
Mulungu ndi wolungama, sangayiwale ntchito zanu ndi chikondi chanu chimene munamuonetsa pothandiza anthu ake monga mmene mukuchitirabe tsopano.
11 我らは汝 等がおのおの終まで前と同じ勵をあらはして全き望を保ち、
Ife tikufuna kuti aliyense wa inu aonetse changu chomwechi mpaka kumapeto, kuti zichitikedi zomwe mukuyembekezera.
12 怠ることなく、信仰と耐忍とをもて約束を嗣ぐ人々に效はんことを求む。
Ife sitikufuna kuti inu mukhale aulesi, koma mutsatire anthu amene, pokhulupirira ndi kupirira, akulandira zimene zinalonjezedwa.
13 それ神はアブラハムに約し給ふとき、指して誓ふべき己より大なる者なき故に、己を指して誓ひて言ひ給へり、
Pamene Mulungu ankamulonjeza Abrahamu, popeza panalibe wamkulu womuposa, amene akanamutchula ndikulumbira mwa Iye, analumbira mwa Iye yekha kuti,
14 『われ必ず、なんぢを惠み惠まん、なんぢを殖し殖さん』と、
“Ine ndidzakudalitsa ndithu, ndipo ndidzakupatsa zidzukulu zambiri.”
15 斯くの如くアブラハムは耐へ忍びて約束のものを得たり。
Ndipo Abrahamu atayembekezera mofatsa, analandira zimene anamulonjezazo.
16 おほよそ人は己より大なる者を指して誓ふ、その誓はすべての爭論を罷むる保證たり。
Anthu amalumbira mʼdzina la wina amene akuwaposa, ndipo lumbiro lotere limatsimikizira zomwe zayankhulidwa ndi kuthetsa mikangano yonse.
17 この故に神は約束を嗣ぐ者に御旨の變らぬことを充分に示さんと欲して誓を加へ給へり。
Momwemonso Mulungu pofuna kutsimikizira anthu amene adzalandire lonjezo, kuti Iye sangasinthe maganizo, anatsimikiza lonjezo lakelo ndi lumbiro.
18 これ神の謊ること能はぬ二つの變らぬものによりて、己の前に置かれたる希望を捉へんとて遁れたる我らに強き奨勵を與へん爲なり。
Mulungu anachita zinthu ziwiri, lonjezo ndi lumbiro, zimene sizingathe kusintha ndipo Mulungu sangathe kunama. Choncho Mulungu akutilimbikitsa mtima ife amene tinathawira kwa Iye kuti tichigwiritsitse chiyembekezo chimene tinalandira.
19 この希望は我らの靈魂の錨のごとく安全にして動かず、かつ幔の内に入る。
Chiyembekezo chimenechi tili nacho ngati nangula wa moyo wathu. Nʼchokhazikika ndi chosagwedezeka ndipo chimalowa mʼkatikati mwa malo opatulika, kuseri kwa chinsalu chotchinga.
20 イエス我等のために前驅し、永遠にメルキゼデクの位に等しき大 祭司となりて、その處に入り給へり。 (aiōn )
Yesu anatitsogolera kupita kumeneko, nalowako mʼmalo mwathu. Iye anasanduka Mkulu wa ansembe onse wamuyaya, monga mwa dongosolo la unsembe wa Melikizedeki. (aiōn )