< ガラテヤ人への手紙 2 >
1 その後 十四年を歴て、バルナバと共にテトスをも連れて、復エルサレムに上れり。
Kenaka, patatha zaka khumi ndi zinayi, ndinapitanso ku Yerusalemu, nthawi iyi ndinapita ndi Barnaba. Ndinatenganso Tito kuti apite nafe.
2 我が上りしは默示に因りてなり。かくて異邦人の中に宣ぶる福音を彼らに告げ、また名ある者どもに私に告げたり、これは我が走ること、又すでに走りしことの空しからざらん爲なり。
Ine ndinapita chifukwa Mulungu anachita kundionetsera kuti ndipite ndipo ndinakakumana ndi atsogoleri mu msonkhano mwamseri ndi kuwafotokozera Uthenga Wabwino umene ndimalalikira pakati pa anthu a mitundu ina. Ndinachita zimenezi kuti ndikhale ndi chitsimikizo kuopa kuti mwina ndinathamanga kapena ndimathamanga liwiro pachabe.
3 而して我と偕なるギリシヤ人テトスすら割禮を強ひられざりき。
Komatu ngakhale Tito, amene anali nane sanakakamizidwe kuti achite mdulidwe, ngakhale iyeyo anali Mgriki.
4 これ私に入りたる僞 兄弟あるに因りてなり。彼らの忍び入りたるは、我らがキリスト・イエスに在りて有てる自由を窺ひ、且われらを奴隷とせん爲なり。
Nkhani iyi inayambika chifukwa abale ena achinyengo amene analowerera pakati pathu kuti adzaone za ufulu umene tili nawo mwa Khristu Yesu ndikuti atisandutse akapolo.
5 然れど福音の眞理の汝らの中に留らんために、我ら一 時も彼らに讓り從はざりき。
Ife sitinawagonjere ndi pangʼono pomwe, nʼcholinga chakuti choonadi cha Uthenga Wabwino chikhalebe ndi ife.
6 然るに、かの名ある者どもより――彼らは如何なる人なるにもせよ、我には關係なし、神は人の外面を取り給はず――實にかの名ある者どもは我に何をも加へず、
Koma kunena za aja ankaoneka ngati ofunika kwambiri, chimene iwo anali sichisintha kanthu kwa ine; chifukwa Mulungu alibe tsankho, iwowo sanawonjezepo kanthu pa uthenga wanga.
7 反つてペテロが割禮ある者に對する福音を委ねられたる如く、我が割禮なき者に對する福音を委ねられたるを認め、
Makamaka anaona kuti ine ndinapatsidwa ntchito yolalikira Uthenga Wabwino kwa anthu a mitundu ina monga momwe Petro anapatsidwa ntchito yolalikira Uthenga Wabwino kwa Ayuda.
8 (ペテロに能力を與へて割禮ある者の使徒となし給ひし者は、我にも異邦人のために能力を與へ給へり)
Pakuti Mulungu, amene amagwira ntchito mu utumiki wa Petro monga mtumwi kwa Ayuda, amagwiranso ntchito mu utumiki wanga monga mtumiki kwa anthu a mitundu ina.
9 また我に賜はりたる恩惠をさとりて、柱と思はるるヤコブ、ケパ、ヨハネは、交誼の印として我とバルナバとに握手せり。これは我らが異邦人にゆき、彼らが割禮ある者に往かん爲なり。
Yakobo, Petro ndi Yohane, amene ankatengedwa ngati mizati, atazindikira chisomo chimene chinapatsidwa kwa ine, anagwirana chanza ndi ine ndi Barnaba kusonyeza chiyanjano chathu. Iwo anavomereza kuti ife tipite kwa anthu a mitundu ina ndipo iwo apite kwa Ayuda.
10 唯その願ふところは我らが貧しき者を顧みんことなり、我も固より此の事を勵みて行へり。
Chimene iwo anapempha ndi chakuti ife tipitirize kukumbukira osauka, chinthu chimene ine ndinali okonzeka kuchichita.
11 されどケパがアンテオケに來りしとき、責むべき事のありしをもて面前これと諍ひたり。
Petro atafika ku Antiokeya, ine ndinamudzudzula pa gulu chifukwa anapezeka wolakwa.
12 その故はある人々のヤコブの許より來るまでは、かれ異邦人と共に食しゐたるに、かの人々の來りてよりは、割禮ある者どもを恐れ、退きて異邦人と別れたり。
Pakuti asanafike anthu otumidwa ndi Yakobo, iye ankadya pamodzi ndi anthu a mitundu ina. Koma atafika, iyeyo anachoka pakati pa anthuwo nakakhala pa yekha chifukwa ankaopa anthu a mʼgulu la mdulidwe.
13 他のユダヤ人も彼とともに僞行をなし、バルナバまでもその僞行に誘はれゆけり。
Ayuda enanso anamutsata pochita zachinyengozi, kotero kuti ngakhale Barnaba anasocheretsedwa chifukwa cha chinyengo chawocho.
14 されど我かれらが福音の眞理に循ひて正しく歩まざるを見て、會衆の前にてケパに言ふ『なんぢユダヤ人なるにユダヤ人の如くせず、異邦人のごとく生活せば、何ぞ強ひて異邦人をユダヤ人の如くならしめんとするか』
Koma nditaona kuti iwo sankachita molingana ndi choonadi cha Uthenga Wabwino, ndinawuza Petro pamaso pa anthu onse kuti, “Iwe ndiwe Myuda koma ukukhala ngati munthu wa mtundu wina, osati Myuda. Nanga nʼchifukwa chiyani ukukakamiza anthu a mitundu ina kuti akhale ngati Ayuda?
15 我らは生來のユダヤ人にして、罪人なる異邦人にあらざれども、
“Ife amene ndife Ayuda mwachibadwa, osati anthu a mitundu ina ochimwa,
16 人の義とせらるるは律法の行爲に由らず、唯キリスト・イエスを信ずる信仰に由るを知りて、キリスト・イエスを信じたり。これ律法の行爲に由らず、キリストを信ずる信仰によりて義とせられん爲なり。律法の行爲によりては義とせらるる者 一人だになし。
tikudziwa kuti munthu salungamitsidwa pochita ntchito za lamulo koma ndi chikhulupiriro mwa Yesu Khristu. Chomwecho, ifenso tinakhulupirira Khristu Yesu kuti tilungamitsidwe mwachikhulupiriro mwa Khristu ndipo osati pochita ntchito za lamulo, chifukwa palibe amene adzalungamitsidwa pochita ntchito za lamulo.
17 若しキリストに在りて義とせららんことを求めて、なほ罪人と認められなば、キリストは罪の役者なるか、決して然らず。
“Tsono ngati ife, pamene tikufuna kulungamitsidwa mwa Khristu, zikuonekeratu poyera kuti ndifenso ochimwa, kodi zikutanthauza kuti Khristu amalimbikitsa uchimo? Ayi. Nʼkosatheka!
18 我もし前に毀ちしものを再び建てなば、己みづから犯罪者たるを表す。
Ngati ine ndimanganso chimene ndinachigumula, ndikuonetsa kuti ndine wophwanya lamulo.
19 我は神に生きんために、律法によりて律法に死にたり。
“Pakuti pamene ndinayesera kutsatira lamulo, lamulolo linandionetsa kuti ndine wochimwa. Choncho ndinasiya kutsatira lamulo kuti ndikhale ndi moyo kwa Mulungu.
20 我キリストと偕に十字架につけられたり。最早われ生くるにあらず、キリスト我が内に在りて生くるなり。今われ肉體に在りて生くるは、我を愛して我がために己が身を捨て給ひし神の子を信ずるに由りて生くるなり。
Ndinapachikidwa pa mtanda pamodzi ndi Khristu, kotero kuti sindinenso amene ndili ndi moyo, koma ndi Khristu amene ali ndi moyo mwa ine. Moyo umene ndili nawo tsopano mʼthupi lino, ndi moyo mwachikhulupiriro mwa Mwana wa Mulungu, amene anandikonda nadzipereka yekha chifukwa cha ine.
21 我は神の恩惠を空しくせず、もし義とせらるること律法に由らば、キリストの死に給へるは徒然なり。
Ine sindikukankhira kumbali chisomo cha Mulungu, chifukwa ngati chilungamo chikanapezeka pochita ntchito za lamulo, ndiye kuti Khristu anafa pachabe.”