< エズラ記 6 >

1 是に於てダリヨス王詔言を出しバビロンにて寳物を蔵むる所の文庫に就て査べ稽しめしに
Atalandira mawuwo mfumu Dariyo anapereka lamulo ndipo kafukufuku anachitikadi ku Babuloni mʼnyumba yosungira chuma ndi mabuku ambiri yakale.
2 メデア州の都城アクメタにて一の卷物を得たり その内に書しるせる記録は是のごとし
Ndipo ku Ekibatana, likulu la dera la Mediya, kunapezeka mpukutu mmene munalembedwa kuti, Chikumbutso:
3 クロス王の元年にクロス王詔言を出せり云くヱルサレムなる神の室の事につきて諭す その犠牲を獻ぐる所なる殿を建てその石礎を堅く置ゑ其室の高を六十キユビトにし其濶を六十キユビトにし
Mʼchaka choyamba cha ufumu wa Koresi, mfumuyo inapereka lamulo lokhudza Nyumba ya Mulungu mu Yerusalemu. Analamula kuti Nyumba ya Mulungu imangidwenso kukhala malo woperekerako nsembe. Maziko ake amangidwe kolimba pa malo pomwe paja pali maziko ake akale ndipo mulitali mwake mukhale mamita 27, mulifupi mwake mukhale mamita 27.
4 巨石三行新木一行を以せよ 其費用は王の家より授くべし
Mumange mizere itatu ya miyala yayikulu ndi mzere umodzi wa matabwa, ndalama zake zolipirira ntchitoyo zichokere mʼthumba la ufumu.
5 またネブカデネザルがヱルサレムの殿より取いだしてバビロンに携へきたりし神の室の金銀の器皿は之を還してヱルサレムの殿に持ゆかしめ神の室に置てその故の所にあらしむべしと
Ndipo ziwiya zagolide ndi zasiliva za ku Nyumba ya Mulungu zimene Nebukadinezara anatenga mʼNyumba ya Mulungu ku Yerusalemu kupita nazo ku Babuloni, zonsezi zibwezedwe ndipo zipite ku Nyumba ya Mulungu ku Yerusalemu. Chilichonse chikabwezedwe pamalo pake mʼNyumbayo.
6 然ば河外ふの總督タテナイおよびセタルボズナイとその同僚なる河外ふのアパルサカイ人汝等これに遠ざかるべし
Tsopano Tatenai, bwanamkubwa wa dera la Patsidya pa Yufurate ndiponso Setari-Bozenai pamodzi ndi anzanu muchokeko kumeneko.
7 神のその室の工事を妨ぐる勿れ ユダヤ人の牧伯とユダヤ人の長老等に神のその家を故の處に建しめよ
Ntchito yomanga Nyumba ya Mulunguyi muyileke. Mulekeni bwanamkubwa wa Ayuda ndiponso akuluakulu a Ayuda kuti amangenso Nyumba ya Mulunguyo pamalo pake.
8 我また詔言を出し其神の家を建ることにつきて汝らが此ユダヤ人の長老等に爲べきことを示す 王の財寳の中すなはち河外ふの租税の中より迅速に費用をその人々に與へよその工事を滯ほらしむる勿れ
Kuwonjezera pamenepo, ndikukhazikitsa lamulo lonena za mmene mudzachitire ndi akuluakulu a Ayuda powathandiza kumanganso Nyumba ya Mulunguyo: Anthuwa muwalipire msanga kuchokera mʼthumba la ufumu, kuchotsa pa msonkho wa dera la Patsidya pa Yufurate.
9 又その需むる物即ち天の神にたてまつる燔祭の小牛牡羊および羔羊ならびに麥鹽酒油など凡てヱルサレムにをる祭司の定むる所に循ひて日々に怠慢なく彼等に與へ
Ndipo zonse zofunikira monga, ana angʼombe, nkhosa zazimuna, ana ankhosa aamuna zoperekera nsembe yopsereza kwa Mulungu wakumwamba, ndi tirigu, mchere, vinyo ndi mafuta monga mmene ansembe a ku Yerusalemu angafunire, muziwapatsa zimenezo tsiku ndi tsiku ndipo musamalephere kutero.
10 彼らをして馨しき香の犠牲を天の神に獻ぐることを得せしめ王とその子女の生命のために祈ることを得せしめよ
Zikatero ndiye kuti azipereka nsembe za fungo lokomera Mulungu wakumwamba ndi kupempherera moyo wa mfumu ndi ana ake.
11 かつ我詔言を出す誰にもせよ此言を易る者あらば其家の梁を抜きとり彼を擧て之に釘ん その家はまた之がために厠にせらるべし
Ndikulamulanso kuti ngati wina asintha zimene ndalamulazi, mtanda umodzi wa nyumba yake udzasololedwa ndi kumunkhomera pamenepo ndipo nyumba yake adzayisandutse dzala.
12 凡そ之を易へまたヱルサレムなるその神の室を毀たんとて手を出す王あるひは民は彼處にその名を留め給ふ神ねがはくはこれを倒したまへ 我ダリヨス詔言を出せり 迅速に之を行なへ
Mulungu amene anasankha kuti anthu azimupembedza pa malo amenewa, achotse mfumu iliyonse kapena munthu aliyense amene adzasinthe zimenezi kapena kuwononga Nyumba ya Mulungu ya ku Yerusalemuko. Ine Dariyo ndikuyika lamuloli, aliyense alitsate mosamala kwambiri.
13 ダリヨス王かく諭しければ河外ふの總督タテナイおよびセタルボズナイとその同僚迅速に之を行なへり
Tsono potsata zomwe analamula mfumu Dariyo, Tatenai bwanamkubwa wa dera la Patsidya pa Yufurate, Setari-Bozenai ndi anzawo anatsatira mosamala kwambiri zimene mfumu Dariyo analamula.
14 ユダヤ人の長老等すなはち之を建て預言者ハガイおよびイドの子ゼカリヤの預言に由て之を成就たり 彼等イスラエルの神の命に循ひクロス、ダリヨスおよびペルシヤ王アルタシヤスタの詔言に依て之を建竣ぬ
Ndipo akuluakulu a Ayuda anapitiriza ntchito yomanga ija molimbikitsidwa ndi aneneri Hagai ndi Zekariya mwana wa Ido. Anamaliza ntchito yomanga Nyumbayo, monga momwe Mulungu wa Israeli analamulira ndiponso potsata lamulo la Koresi, Dariyo ndi Aritasasita, mafumu a ku Perisiya.
15 ダリヨス王の治世の六年アダルの月の三日にこの室成り
Anatsiriza kumanga Nyumbayo pa tsiku lachitatu la mwezi wa Adara mʼchaka chachisanu ndi chimodzi cha ulamuliro wa mfumu Dariyo.
16 是に於てイスラエルの子孫祭司レビ人およびその餘の俘擄人よろこびて神のこの室の落成禮を行なへり
Choncho Aisraeli, ansembe, Alevi ndi anthu ena onse amene anali atabwerako ku ukapolo, anachita chikondwerero chopereka Nyumba ya Mulungu mwachimwemwe.
17 即ち神のこの室の落成禮において牡牛一百牡羊二百 羔羊四百を獻げまたイスラエルの支派の數にしたがひて牡山羊十二を獻げてイスラエル全體のために罪祭となし
Poporeka Nyumba ya Mulunguyi, anthu anapereka nsembe za ngʼombe zazimuna 100, nkhosa zazimuna 200, ana ankhosa aamuna 400. Anaperekanso mbuzi zazimuna 12 ngati nsembe yopepesera machimo a anthu onse, potsata chiwerengero cha mafuko a Israeli.
18 祭司をその分別にしたがひて立て レビ人をその班列にしたがひて立て ヱルサレムに於て神に事へしむ 凡てモーセの書に書しるしたるが如し
Ndipo anakhazikitsa ansembe ndi Alevi pa ntchito zawo zotumikira Mulungu mu Yerusalemu monga zinalembedwera mʼbuku la Mose.
19 斯て俘囚より歸り來りし人々正月の十四日に逾越節を行へり
Pa tsiku la khumi ndi chinayi la mwezi woyamba, obwera ku ukapolo aja anachita chikondwerero cha Paska.
20 即ち祭司レビ人共に身を潔めて皆潔くなり一切俘囚より歸り來りし人々のため其兄弟たる祭司等のため又自己のために逾越の物を宰れり
Ansembe ndi Alevi anali atadziyeretsa ndipo onsewo anali oyeretsedwa. Alevi anapha mwana wankhosa wa Paska kuphera onse amene anatuluka ku ukapolo, ansembe anzawo ndi iwo eni.
21 擄はれゆきて歸り來しイスラエルの子孫および其國の異邦人の汚穢を棄て是等に附てイスラエルの神ヱホバを求むる者等すべて之を食ひ
Nkhosa ya Paskayo anayidya ndi Aisraeli onse amene anatuluka ku ukapolo, wina aliyense amene anaphatikana nawo atadziyeretsa ku zonyansa za mitundu ina ya anthu akunja a mʼdzikomo kuti apembedze Yehova Mulungu wa Israeli.
22 喜びて七日の間酵いれぬパンの節を行へり 是はヱホバかれらを喜ばせアッスリヤの王の心を彼らに向はせ彼をしてイスラエルの神にまします神の家の工事を助けさせたまひしが故なり
Choncho pa masiku asanu ndi awiri anasangalala pa chikondwerero cha buledi wopanda yisiti, chifukwa Yehova anawadzaza ndi chimwemwe. Iye anatembenuza mtima wa mfumu ya ku Asiriya motero kuti iyo inakomera mtima Aisraeli ndi kuwathandiza ntchito yomanga Nyumba ya Mulungu, Mulungu wa Israeli.

< エズラ記 6 >