< コリント人への手紙第一 5 >
1 現に聞く所によれば、汝らの中に淫行ありと、而してその淫行は異邦人の中にもなき程にして、或 人その父の妻を有てりと云ふ。
Mbiri yamveka kuti pakati panu pakuchitika chigololo. Ndipo chigololo cha mtunduwu ngakhale pakati pa akunja sichingapezeke; munthu akumagonana ndi mkazi wa abambo ake.
2 斯くてもなほ汝ら誇ることをなし、かかる行爲をなしし者の除かれんことを願ひて悲しまざるか。
Ndipo inu mukudzitukumulabe. Kodi simukanayenera kudzazidwa ndi chisoni ndipo mukanamuchotsa pa chiyanjano chanu munthu wochita zimenezi?
3 われ身は汝らを離れ居れども、心は偕に在りて其處に居るごとく、かかる事を行ひし者を既に審きたり。
Ngakhale sindili nanu mʼthupi, ndili nanu mu mzimu. Ndipo ineyo ndapereka kale chiweruzo pa munthu amene amachita zotere, ngati kuti ndili komweko.
4 すなはち汝ら及び我が靈の、我らの主イエスの能力をもて偕に集らんとき、主イエスの名によりて、
Mukasonkhana mu dzina la Ambuye athu Yesu, ine ndili nanu mu mzimu, ndipo mphamvu ya Ambuye athu Yesu ili pomwepo,
5 斯くのごとき者をサタンに付さんとす、是その肉は亡されて、其の靈は主イエスの日に救はれん爲なり。
mumupereke munthuyu kwa Satana, kuti chikhalidwe chake cha uchimo chiwonongedwe ndikuti mzimu wake udzapulumuke pa tsiku la Ambuye.
6 汝らの誇は善からず。少しのパン種の、粉の團塊をみな膨れしむるを知らぬか。
Kudziwa kwanu si kwabwino. Kodi simukudziwa kuti yisiti wochepa amafufumitsa mphumphu yaufa wonse wa tirigu?
7 なんぢら新しき團塊とならんために舊きパン種を取り除け、汝らはパン種なき者なればなり。夫われらの過越の羔羊すなはちキリスト既に屠られ給へり、
Chotsani yisiti wakale kuti mukhale ndi mphumphu yopanda yisiti, monga inu muli. Pakuti Khristu, Mwana Wankhosa wa Paska wathu, anaperekedwa nsembe.
8 されば我らは舊きパン種を用ひず、また惡と邪曲とのパン種を用ひず、眞實と眞との種なしパンを用ひて祭を行ふべし。
Choncho, tiyeni tisunge chikondwererochi, osati ndi yisiti wakale, wowononga ndi woyipa, koma ndi buledi wopanda yisiti, buledi woona mtima ndi choonadi.
9 われ前の書にて淫行の者と交るなと書き贈りしは、
Ndakulemberani mʼkalata yanga kuti musayanjane nawo anthu achigololo.
10 此の世の淫行の者、または貪欲のもの、奪ふ者、または偶像を拜む者と更に交るなと言ふにあらず(もし然せば世を離れざるを得ず)
Pamenepatu sindikutanthauzatu anthu a dziko lapansi lino amene ndi achigololo, kapena aumbombo, kapena opeza ndalama mwachinyengo, kapena opembedza mafano. Kukanatero mukanangochoka mʼdziko lapansi lino.
11 ただ兄弟と稱ふる者の中に、或は淫行のもの、或は貪欲のもの、或は偶像を拜む者、あるひは罵るもの、或は酒に醉ふもの、或は奪ふ者あらば、斯かる人と交ることなく、共に食する事だにすなとの意なり。
Koma tsopano ndikukulemberani kuti musayanjane ndi aliyense amene adzitcha mʼbale koma ndi wachigololo, kapena waumbombo, kapena wopembedza mafano, kapena wonamizira anzake, woledzera kapena wopeza ndalama mwachinyengo. Munthu wotere ngakhale kudya, osadya naye pamodzi.
12 外の者を審くことは我の干る所ならんや、汝らの審くは、ただ内の者ならずや。
Kodi ndipindulanji kuti ndiweruze anthu amene si a mu mpingo? Kodi simuyenera kuweruza iwo amene ali mu mpingo?
13 外にある者は神これを審き給ふ。かの惡しき者を汝らの中より退けよ。
Mulungu adzaweruza akunja. “Chotsani woyipayo pakati panu.”