< コリント人への手紙第一 12 >

1 兄弟よ、靈の賜物に就きては、我なんぢらが知らぬを好まず。
Tsopano abale anga okondedwa, sindikufuna mukhale osadziwa za mphatso za Mzimu.
2 なんぢら異邦人なりしとき、誘はるるままに物を言はぬ偶像のもとに導き往かれしは、汝らの知る所なり。
Inu mukudziwa kuti pamene munali akunja, ankakusocheretsani mʼnjira zosiyanasiyana ndi kukukokerani ku mafano osayankhula.
3 然れば我なんぢらに示さん、神の御靈に感じて語る者は、誰も『イエスは詛はるべき者なり』と言はず、また聖 靈に感ぜざれば、誰も『イエスは主なり』と言ふ能はず。
Nʼchifukwa chake ndikuwuzani kuti palibe munthu amene ali ndi Mzimu wa Mulungu angayankhule kuti, “Yesu atembereredwe,” ndiponso palibe munthu anganene kuti “Yesu ndi Ambuye,” popanda kutsogozedwa ndi Mzimu Woyera.
4 賜物は殊なれども、御靈は同じ。
Pali mphatso zosiyanasiyana, koma Mzimu yemweyo.
5 務は殊なれども、主は同じ。
Pali mautumiki osiyanasiyana koma Ambuye yemweyo.
6 活動は殊なれども、凡ての人のうちに凡ての活動を爲したまふ神は同じ。
Pali magwiridwe antchito osiyanasiyana, koma Mulungu yemweyo amagwira ntchito monsemo mwa anthu onse.
7 御靈の顯現をおのおのに賜ひたるは、益を得させんためなり。
Tsono Mzimu amapereka mphatso kwa aliyense kuti ipindulire onse.
8 或 人は御靈によりて智慧の言を賜はり、或 人は同じ御靈によりて知識の言、
Mzimu amapereka kwa munthu wina mawu anzeru, Mzimu yemweyonso amapereka kwa wina mawu achidziwitso.
9 或 人は同じ御靈によりて信仰、ある人は一つ御靈によりて病を醫す賜物、
Kwa wina, Mzimu yemweyo amapereka chikhulupiriro, kwa wina mphatso zamachiritso, Mzimu yemweyo.
10 或 人は異能ある業、ある人は預言、ある人は靈を辨へ、或 人は異言を言ひ、或 人は異言を釋く能力を賜はる。
Kwa wina mphamvu zochita zodabwitsa, kwa wina mawu a uneneri, kwa wina mphatso yozindikira mizimu, kwa wina malilime osiyanasiyana, ndiponso kwa wina kutanthauzira malilimewo.
11 凡て此 等のことは同じ一つの御靈の活動にして、御靈その心に隨ひて各人に分け與へたまふなり。
Zonsezi ndi ntchito za Mzimu mmodzi yemweyo, ndipo amapereka kwa munthu aliyense monga momwe Mzimuyo wafunira.
12 體は一つにして肢は多し、體の肢は多くとも一つの體なるが如く、キリストも亦 然り。
Thupi ndi limodzi, ngakhale kuti lapangidwa ndi ziwalo zambiri. Ndipo ngakhale ziwalo zake zonse ndi zambiri, zimapanga thupi limodzi. Momwemonso ndi mmene alili Khristu.
13 我らはユダヤ人・ギリシヤ人・奴隷・自主の別なく、一體とならん爲に、みな一つ御靈にてバプテスマを受けたり。而してみな一つ御靈を飮めり。
Pakuti tonse tinabatizidwa ndi Mzimu mmodzi mʼthupi limodzi. Myuda kapena Mgriki, kapolo kapena mfulu tonse tinapatsidwa kuti timwe Mzimu mmodzi yemweyo.
14 體は一 肢より成らず、多くの肢より成るなり。
Tsopano thupi silinapangidwe ndi chiwalo chimodzi koma ndi ziwalo zambiri.
15 足もし『我は手にあらぬ故に體に屬せず』と云ふとも、之によりて體に屬せぬにあらず。
Ngati phazi litanena kuti, “Pakuti sindine dzanja, sindine chiwalo cha thupi.” Chifukwa chimenechi sichingachititse phazi kuti lisakhale chiwalo cha thupi.
16 耳もし『それは眼にあらぬ故に體に屬せず』と云ふとも、之によりて體に屬せぬにあらず。
Ndipo ngati khutu litanena kuti, “Pakuti sindine diso, sindine chiwalo cha thupi.” Chifukwa chimenechi sichingachititse khutu kuti lisakhale chiwalo cha thupi.
17 もし全身、眼ならば、聽くところ何れか。もし全身、聽く所ならば、臭ぐところ何れか。
Kodi thupi lonse likanakhala diso, tikanamamva bwanji? Nanga thupi lonse likanakhala khutu, tikanamanunkhiza bwanji?
18 げに神は御意のままに肢をおのおの體に置き給へり。
Koma zoona nʼzakuti, Mulungu anayika ziwalo mʼthupi, chilichonse monga momwe Iye anafunira.
19 若しみな一 肢ならば、體は何れか。
Nanga zonse zikanakhala chiwalo chimodzi, ndiye thupi likanakhala lotani?
20 げに肢は多くあれど、體は一つなり。
Mmene zililimu, pali ziwalo zambiri koma thupi ndi limodzi lokha.
21 眼は手に對ひて『われ汝を要せず』と言ひ、頭は足に對ひて『われ汝を要せず』と言ふこと能はず。
Diso silingawuze dzanja kuti, “Iwe sindikukufuna!” Ndipo mutu sungawuze phazi kuti “Iwe sindikukufuna!”
22 否、からだの中にて最も弱しと見ゆる肢は、反つて必要なり。
Mʼmalo mwake, ziwalo zathupi zimene zimaoneka ngati zofowoka ndizo zili zofunikira kwambiri,
23 體のうちにて尊からずと思はるる所に、物を纏ひて殊に之を尊ぶ。斯く我らの美しからぬ所は、一層すぐれて美しくすれども、
ndipo ziwalo zathupi zimene timaziyesa zopanda ulemu, ndizo timazilemekeza kwambiri. Ndipo ziwalo zosaoneka bwino ndizo zimalandira ulemu wapadera.
24 美しき所には、物を纏ふの要なし。神は劣れる所に殊に尊榮を加へて、人の體を調和したまへり。
Koma ziwalo zooneka bwino, nʼkosafunika kuti tizisamalire mwapadera. Mulungu polumikiza ziwalo zathupi, anapereka ulemu wopambana kwa ziwalo zimene zimafunadi ulemuwo
25 これ體のうちに分爭なく、肢々 一致して互に相 顧みんためなり。
kuti pasakhale kugawikana mʼthupi koma kuti ziwalo zonse zisamalirane.
26 もし一つの肢 苦しまば、もろもろの肢ともに苦しみ、一つの肢 尊ばれなば、もろもろの肢ともに喜ぶなり。
Ngati chiwalo chimodzi chikumva kuwawa, ziwalo zonse zimamvanso kuwawa. Ngati chiwalo chimodzi chilandira ulemu, ziwalo zonse zimakondwera nawo.
27 乃ち汝らはキリストの體にして各自その肢なり。
Tsopano inu ndinu thupi la Khristu, ndipo aliyense wa inu ndi chiwalo cha thupilo.
28 神は第一に使徒、第二に預言者、第三に教師、その次に異能ある業、次に病を醫す賜物、補助をなす者、治むる者、異言などを教會に置きたまへり。
Ndipo Mulungu mu mpingo anayika poyamba atumwi, kachiwiri aneneri, kachitatu aphunzitsi, kenaka ochita zozizwitsa, ena a mphatso zamachiritso, ena a mphatso yothandiza anzawo, ena a mphatso yotsogolera ndiponso ena a mphatso ya malilime.
29 是みな使徒ならんや、みな預言者ならんや、みな教師ならんや、みな異能ある業を行ふ者ならんや。
Kodi onse ndi atumwi? Kodi onse ndi aneneri? Kodi onse ndi aphunzitsi? Kodi onse amachita zozizwitsa?
30 みな病を醫す賜物を有てる者ならんや、みな異言を語る者ならんや、みな異言を釋く者ならんや。
Kodi onse ali ndi mphatso zamachiritso? Kodi onse amayankhula malilime? Kodi onse amatanthauzira malilime?
31 なんぢら優れたる賜物を慕へ、而して我さらに善き道を示さん。
Koma funitsitsani mphatso zopambana. Tsopano ndikuonetsani njira yopambana kwambiri.

< コリント人への手紙第一 12 >