< Ezechiele 10 >

1 Io guardai, ed ecco, sulla distesa sopra il capo dei cherubini, v’era come una pietra di zaffiro; si vedeva come una specie di trono che stava sopra loro.
Ine nditayangʼana ku thambo limene lili pamwamba pa mitu ya akerubi ndinangoona chinthu chooneka ngati mpando waufumu wa mwala wa safiro.
2 E l’Eterno parlò all’uomo vestito di lino, e disse: “Va’ fra le ruote sotto i cherubini, empiti le mani di carboni ardenti tolti di fra i cherubini, e spargili sulla città”. Ed egli v’andò in mia presenza.
Tsono Yehova anawuza munthu wovala chovala chabafuta uja kuti, “Pita pakati pa mikombero kunsi kwa akerubi. Udzaze manja ako ndi makala oyaka amene ali pakati pa akerubiwo ndipo uwawaze mu mzinda.” Iye anachita zimenezi ine ndikuona.
3 Or i cherubini stavano al lato destro della casa, quando l’uomo entrò là; e la nuvola riempì il cortile interno.
Apa akerubiwo anali atayima mbali ya kummwera kwa Nyumba ya Mulungu pamene munthuyo ankalowa. Tsono mtambo unadzaza bwalo lamʼkati.
4 E la gloria dell’Eterno s’alzò di sui cherubini, movendo verso la soglia della casa; e la casa fu ripiena della nuvola; e il cortile fu ripieno dello splendore della gloria dell’Eterno.
Ndipo ulemerero wa Yehova unachoka pamwamba pa akerubi ndipo unafika ku chiwundo cha Nyumba ya Mulungu. Mtambo unadzaza Nyumba ya Mulungu, ndipo kuwala kwa ulemerero wa Yehova kunadzaza bwalolo.
5 E il rumore delle ali dei cherubini s’udì fino al cortile esterno, simile alla voce dell’Iddio onnipotente quand’egli parla.
Phokoso la mapiko a akerubi limamveka mpaka ku bwalo lakunja, monga momwe linamvekera liwu la Mulungu Wamphamvuzonse akamayankhula.
6 E quando l’Eterno ebbe dato all’uomo vestito di lino l’ordine di prender del fuoco di fra le ruote che son tra i cherubini, quegli venne a fermarsi presso una delle ruote.
Kenaka Yehova analamula munthu wovala chovala chabafuta uja kuti, “Pala moto pakati pa mikombero, pakati pa akerubi.” Munthu uja anapitadi nakayima pa mbali pa mkombero umodzi.
7 E uno dei cherubini stese la mano fra gli altri cherubini verso il fuoco ch’era fra i cherubini, ne prese e lo mise nelle mani dell’uomo vestito di lino, che lo ricevette, ed uscì.
Ndipo mmodzi wa akerubi anatambalitsa dzanja lake mpaka pa moto umene unali pakati pawo. Iye anapalako motowo ndipo anapatsa munthu wovala chovala chabafuta uja. Tsono iye anawulandira natuluka.
8 Or ai cherubini si vedeva una forma di mano d’uomo sotto alle ali.
Ndiye kuti kunsi kwa mapiko akerubi kumaoneka zinthu zooneka ngati manja a munthu.
9 E io guardai, ed ecco quattro ruote presso ai cherubini, una ruota presso ogni cherubino; e le ruote avevano l’aspetto d’una pietra di crisolito.
Ine nditayangʼanitsitsa ndinaona mikombero inayi pambali pa akerubi. Pambali pa kerubi aliyense panali mkombero umodzi; mikomberoyo inkanyezimira ngati miyala yokongola ya krizoliti.
10 E, a vederle, tutte e quattro avevano una medesima forma, come se una ruota passasse attraverso all’altra.
Maonekedwe a mikombero inayi ija anali ofanana. Mkombero uliwonse umaoneka ngati mkombero wolowana ndi unzake.
11 Quando si movevano, si movevano dai loro quattro lati; e, movendosi, non si voltavano, ma seguivano la direzione del luogo verso il quale guardava il capo, e, andando, non si voltavano.
Poyenda akerubiwo, amapita mbali iliyonse ya mbali zinayizo kumene akerubiwo amayangʼana. Mikomberoyo simatembenuka pamene akerubiwo ankayenda. Kulikonse kumene mutu walunjika nʼkumene ankapita popanda kutembenuka.
12 E tutto il corpo dei cherubini, i loro dossi, le loro mani, le loro ali, come pure le ruote, le ruote di tutti e quattro, eran pieni d’occhi tutto attorno.
Matupi awo onse, misana yawo, manja awo ndi mapiko awo zinali ndi maso okhaokha, monganso mʼmene inalili mikombero yawo inayi ija.
13 E udii che le ruote eran chiamate “Il Turbine”.
Ine ndinamva mikombero ikutchedwa kuti, “mikombero yakamvuluvulu.”
14 E ogni cherubino aveva quattro facce: la prima faccia era una faccia di cherubino; la seconda faccia, una faccia d’uomo; la terza, una faccia di leone; la quarta, una faccia d’aquila.
Kerubi aliyense anali ndi nkhope zinayi. Nkhope yoyamba inali ya Kerubi, nkhope yachiwiri inali ya munthu, nkhope yachitatu inali ya mkango ndipo nkhope yachinayi inali ya chiwombankhanga.
15 E i cherubini s’alzarono. Erano gli stessi esseri viventi, che avevo veduti presso il fiume Kebar.
Tsono akerubi aja anawuluka. Izi zinali zamoyo zija zimene ndinaziona ku mtsinje wa Kebara.
16 E quando i cherubini si movevano, anche le ruote si movevano allato a loro; e quando i cherubini spiegavano le ali per alzarsi da terra, anche le ruote non deviavano da presso a loro.
Pamene akerubi ankayenda, nayonso mikombero ya mʼmbali mwawo inkayenda. Akerubiwo ankati akatambasula mapiko awo kuti auluke mikombero sinkachoka mʼmbali mwawo.
17 Quando quelli si fermavano, anche queste si fermavano; quando quelli s’innalzavano, anche queste s’innalzavano con loro, perché lo spirito degli esseri viventi era in esse.
Akerubiwo ankati akayima, mikombero inkayimanso. Ngati akerubiwo auluka, mikomberoyo inkapita nawo chifukwa mzimu wa zamoyozo ndiwo unkayendetsa mikomberoyo.
18 E la gloria dell’Eterno si partì di sulla soglia della casa, e si fermò sui cherubini.
Pamenepo ulemerero wa Yehova unachoka pa chiwundo cha Nyumba ya Mulungu ndi kukakhala pamwamba pa akerubi.
19 E i cherubini spiegarono le loro ali e s’innalzarono su dalla terra; e io li vidi partire, con le ruote allato a loro. Si fermarono all’ingresso della porta orientale della casa dell’Eterno; e la gloria dell’Iddio d’Israele stava sopra di loro, su in alto.
Ine ndikuona akerubi, anatambasula mapiko awo ndi kuwuluka. Pamene ankapita, mikombero inapita nawo pamodzi. Akerubi anakayima pa khomo la chipata cha kummawa cha Nyumba ya Yehova. Tsono ulemerero wowala wa Mulungu wa Israeli unali pamwamba pawo.
20 Erano gli stessi esseri viventi, che avevano veduti sotto l’Iddio d’Israele presso il fiume Kebar; e riconobbi che erano cherubini.
Izi ndizo zamoyo ndinaziona pansi pa Mulungu wa Israeli ku mtsinje wa Kebara, ndipo ndinazindikira kuti anali akerubi.
21 Ognun d’essi avevan quattro facce, ognuno quattro ali; e sotto le loro ali appariva la forma di mani d’uomo.
Kerubi aliyense anali ndi nkhope zinayi ndi mapiko anayi, ndipo kunsi kwa mapiko awo kunali chinthu chimene chimaoneka ngati manja a munthu.
22 E quanto all’aspetto delle loro facce, eran le facce che avevo vedute presso il fiume Kebar; erano gli stessi aspetti, i medesimi cherubini. Ognuno andava dritto davanti a sé.
Nkhope zawo zinali zofanana ndi zomwe ndinaziona ku mtsinje wa Kebara. Kerubi aliyense amayenda molunjika.

< Ezechiele 10 >