< 2 Cronache 12 >
1 Quando Roboamo fu bene stabilito e fortificato nel regno, egli, e tutto Israele con lui, abbandonò la legge dell’Eterno.
Rehobowamu atakhazikika monga mfumu nakhaladi wamphamvu, iyeyo pamodzi ndi Aisraeli onse anasiya malamulo a Yehova.
2 E l’anno quinto del regno di Roboamo, Scishak re d’Egitto, salì contro Gerusalemme, perch’essi erano stati infedeli all’Eterno.
Chifukwa anakhala osakhulupirika pamaso pa Yehova, Sisaki mfumu ya dziko la Igupto inathira nkhondo Yerusalemu mʼchaka chachisanu cha mfumu Rehobowamu.
3 Egli avea milleduecento carri e sessantamila cavalieri; con lui venne dall’Egitto un popolo innumerevole di Libi, di Sukkei e di Etiopi;
Sisakiyo anabwera ndi magaleta 1,200 ndi anthu okwera akavalo 60,000 ndiponso asilikali osawerengeka ochokera ku Libiya, Suki ndi Kusi amene anabwera naye kuchokera ku Igupto.
4 s’impadronì delle città fortificate che appartenevano a Giuda, e giunse fino a Gerusalemme.
Iye analanda mizinda yotetezedwa ya Yuda ndipo anafika mpaka ku Yerusalemu.
5 E il profeta Scemaia si recò da Roboamo e dai capi di Giuda, che s’erano raccolti in Gerusalemme all’avvicinarsi di Scishak, e disse loro: “Così dice l’Eterno: Voi avete abbandonato me, quindi anch’io ho abbandonato voi nelle mani di Scishak”.
Ndipo mneneri Semaya anabwera kwa Rehobowamu ndi kwa atsogoleri a Yuda amene anasonkhana mu Yerusalemu chifukwa cha Sisaki ndipo iye anawawuza kuti, “Yehova akuti, ‘Inu mwandisiya, choncho Inenso ndakusiyani ndi kukuperekani kwa Sisaki.’”
6 Allora i principi d’Israele e il re si umiliarono, e dissero: “L’Eterno è giusto”.
Atsogoleri a Israeli pamodzi ndi mfumu anadzichepetsa nati, “Yehova ndi wolungama.”
7 E quando l’Eterno vide che s’erano umiliati, la parola dell’Eterno fu così rivolta a Scemaia: “Essi si sono umiliati; io non li distruggerò, ma concederò loro fra poco un mezzo di scampo, e la mia ira non si rovescerà su Gerusalemme per mezzo di Scishak.
Yehova ataona kuti adzichepetsa, anayankhula ndi Semaya kuti, “Pakuti adzichepetsa, Ine sindiwawononga koma posachedwapa ndiwapulumutsa. Sinditsanulira ukali wanga pa Yerusalemu kudzera mwa Sisaki.
8 Nondimeno gli saranno soggetti, e impareranno la differenza che v’è tra il servire a me e il servire ai regni degli altri paesi”.
Komabe iwo adzakhala pansi pa ulamuliro wake, kuti aphunzire kudziwa kusiyanitsa pakati pa kutumikira Ine ndi kutumikira mafumu a mayiko ena.”
9 Scishak, re d’Egitto, salì dunque contro Gerusalemme e portò via i tesori della casa dell’Eterno e i tesori della casa del re; portò via ogni cosa; prese pure gli scudi d’oro che Salomone avea fatti;
Sisaki mfumu ya dziko la Igupto atathira nkhondo Yerusalemu, iye anatenga chuma cha mʼNyumba ya Yehova ndi chuma cha mʼnyumba yaufumu. Iye anatenga zinthu zonse kuphatikizapo zishango zagolide zimene Solomoni anapanga.
10 invece de’ quali, il re Roboamo fece fare degli scudi di rame, e li affidò ai capitani della guardia che custodiva la porta della casa del re.
Ndipo mfumu inapereka zishango zamkuwa kwa oyangʼanira mʼmalo mwake ndipo iwo anazipereka kwa oyangʼanira alonda amene amayangʼanira pa chipata cha nyumba yaufumu.
11 E ogni volta che il re entrava nella casa dell’Eterno, quei della guardia venivano, e li portavano; poi li riportavano nella sala della guardia.
Nthawi ina iliyonse imene mfumu ikupita ku Nyumba ya Yehova, alonda amapita nayo atanyamula zishango, ndipo kenaka amakazibwezera ku chipinda cha alonda.
12 Così, perch’egli s’era umiliato, l’Eterno rimosse da lui l’ira sua e non volle distruggerlo del tutto; e v’erano anche in Giuda delle cose buone.
Pakuti mfumu Rehobowamu inadzichepetsa, mkwiyo wa Yehova unamuchokera, sanawonongedweretu. Kunena zoona, munali zinthu zina zabwino mu Yuda.
13 Il re Roboamo dunque si rese forte in Gerusalemme, e continuò a regnare. Avea quarantun anni quando cominciò a regnare, e regnò diciassette anni a Gerusalemme, la città che l’Eterno s’era scelta fra tutte le tribù d’Israele, per stabilirvi il suo nome. Sua madre si chiamava Naama, l’Ammonita.
Mfumu Rehobowamu anayika maziko a ufumu wake mwamphamvu mu Yerusalemu ndipo anapitirira kukhala mfumu. Iye anali ndi zaka 41 pamene anakhala mfumu, ndipo analamulira zaka 17 mu Yerusalemu, mzinda wa Yehova umene anasankha pakati pa mafuko a Aisraeli mmene Yehova anakhazikikamo. Dzina la amayi ake linali Naama, amene anali Mwamoni.
14 Ed egli fece il male, perché non applicò il cuor suo alla ricerca dell’Eterno.
Rehobowamu anachita zoyipa chifuwa mtima wake sunafunefune Yehova.
15 Or le azioni di Roboamo, le prime e le ultime, sono scritte nelle storie del profeta Scemaia e d’Iddo, il veggente, nei registri genealogici. E vi fu guerra continua fra Roboamo e Geroboamo.
Ntchito za Rehobowamu, kuyambira pachiyambi mpaka pa mapeto, kodi sizinalembedwe mʼbuku la mbiri la mneneri Semaya ndi mlosi Ido amene amalemba mbiri? Panali nkhondo yosatha pakati pa Rehobowamu ndi Yeroboamu.
16 E Roboamo s’addormentò coi suoi padri e fu sepolto nella città di Davide. Ed Abija, suo figliuolo, regnò in luogo suo.
Rehobowamu anamwalira, ndipo anayikidwa mʼmanda mu mzinda wa Davide. Ndipo mwana wake Abiya analowa ufumu mʼmalo wake.