< Ezechiele 2 >

1 Mi disse: «Figlio dell'uomo, alzati, ti voglio parlare».
Iye anandiwuza kuti, “Iwe mwana wa munthu, imirira kuti ndiyankhule nawe.”
2 Ciò detto, uno spirito entrò in me, mi fece alzare in piedi e io ascoltai colui che mi parlava.
Pamene ankayankhula nane, Mzimu wa Mulungu unalowa mwa ine ndipo unandiyimiritsa, ndipo ndinamva Iye akundiyankhula.
3 Mi disse: «Figlio dell'uomo, io ti mando agli Israeliti, a un popolo di ribelli, che si sono rivoltati contro di me. Essi e i loro padri hanno peccato contro di me fino ad oggi.
Iye anati, “Iwe mwana wa munthu, Ine ndikukutuma kwa Aisraeli, mtundu wa anthu owukira umene wandiwukira Ine; Iwo ndi makolo awo akhala akundiwukira Ine mpaka lero lino.
4 Quelli ai quali ti mando sono figli testardi e dal cuore indurito. Tu dirai loro: Dice il Signore Dio.
Ndikukutuma kwa anthu okanika ndiponso nkhutukumve. Ndikukutuma kuti akawawuze zimene Ine Ambuye Yehova ndikunena.
5 Ascoltino o non ascoltino - perché sono una genìa di ribelli - sapranno almeno che un profeta si trova in mezzo a loro.
Kaya akamva kaya sakamvera, pakuti iwo ndi anthu opanduka, komabe adzadziwa kuti mneneri ali pakati pawo.
6 Ma tu, figlio dell'uomo non li temere, non aver paura delle loro parole; saranno per te come cardi e spine e ti troverai in mezzo a scorpioni; ma tu non temere le loro parole, non t'impressionino le loro facce, sono una genìa di ribelli.
Tsono iwe mwana wa munthu, usachite nawo mantha kapena kuopa zimene azikanena. Usachite mantha, ngakhale minga ndi mkandankhuku zikuzinge ndipo ukukhala pakati pa zinkhanira. Usachite mantha ndi zimene akunena kapena kuopsedwa ndi nkhope zawo, popeza anthuwa ndi awupandu.
7 Tu riferirai loro le mie parole, ascoltino o no, perché sono una genìa di ribelli.
Ukawawuze ndithu mawu anga, kaya akamva kaya sakamva. Paja anthuwa ndi awupandu.
8 E tu, figlio dell'uomo, ascolta ciò che ti dico e non esser ribelle come questa genìa di ribelli; apri la bocca e mangia ciò che io ti do».
Koma iwe mwana wa munthu, mvetsera zimene ndikukuwuza. Usakhale wowukira ngati iwowo. Tsono yasama pakamwa pako kuti udye chimene ndikukupatsa.”
9 Io guardai ed ecco, una mano tesa verso di me teneva un rotolo. Lo spiegò davanti a me; era scritto all'interno e all'esterno e vi erano scritti lamenti, pianti e guai.
Nditayangʼana ndinangoona dzanja litaloza ine, litagwira mpukutu wolembedwa.
Anawufunyulura pamaso panga. Mpukutu wonse unali wolembedwa kuseri nʼkuseri. Ndipo mawu amene analembedwa mʼmenemo anali a madandawulo, maliro ndi matemberero.

< Ezechiele 2 >