< זכריה 10 >
שאלו מיהוה מטר בעת מלקוש יהוה עשה חזיזים ומטר גשם יתן להם לאיש עשב בשדה׃ | 1 |
Pemphani mvula kwa Yehova pa nthawi yamphukira; ndi Yehova amene amapanga mitambo ya mvula. Iye amagwetsa mivumbi ya mvula kwa anthu, ndi kumeretsa mbewu za mʼmunda kwa aliyense.
כי התרפים דברו און והקוסמים חזו שקר וחלמות השוא ידברו הבל ינחמון על כן נסעו כמו צאן יענו כי אין רעה׃ | 2 |
Mafano amayankhula zachinyengo, owombeza mawula amaona masomphenya abodza; amafotokoza maloto onama, amapereka chitonthozo chopandapake. Choncho anthu amangoyendayenda ngati nkhosa zozunzika chifukwa chosowa mʼbusa.
על הרעים חרה אפי ועל העתודים אפקוד כי פקד יהוה צבאות את עדרו את בית יהודה ושם אותם כסוס הודו במלחמה׃ | 3 |
“Ine ndawakwiyira kwambiri abusa, ndipo ndidzalanga atsogoleri; pakuti Yehova Wamphamvuzonse adzasamalira nkhosa zake, nyumba ya Yuda, ndi kuwasandutsa ngati akavalo aulemerero ankhondo.
ממנו פנה ממנו יתד ממנו קשת מלחמה ממנו יצא כל נוגש יחדו׃ | 4 |
Mu Yuda mudzachokera mwala wapangodya, mudzachokera chikhomo cha tenti, mudzachokera uta wankhondo, mudzachokera mtsogoleri aliyense.
והיו כגברים בוסים בטיט חוצות במלחמה ונלחמו כי יהוה עמם והבישו רכבי סוסים׃ | 5 |
Onse pamodzi adzakhala ngati ngwazi zankhondo zoponda mʼmatope a mʼmisewu nthawi yankhondo. Chifukwa Yehova adzakhala nawo, adzachita nkhondo ndi kugonjetsa okwera pa akavalo.
וגברתי את בית יהודה ואת בית יוסף אושיע והושבותים כי רחמתים והיו כאשר לא זנחתים כי אני יהוה אלהיהם ואענם׃ | 6 |
“Ndidzalimbitsa nyumba ya Yuda ndi kupulumutsa nyumba ya Yosefe. Ndidzawabwezeretsa chifukwa ndawamvera chisoni. Adzakhala ngati kuti sindinawakane, chifukwa ndine Yehova Mulungu wawo ndipo ndidzawayankha.
והיו כגבור אפרים ושמח לבם כמו יין ובניהם יראו ושמחו יגל לבם ביהוה׃ | 7 |
Aefereimu adzakhala ngati ankhondo amphamvu adzasangalala ngati anthu amene amwa vinyo. Ana awo adzaziona zimenezi ndipo adzasangalala; mʼmitima mwawo adzakondwa mwa Ambuye.
אשרקה להם ואקבצם כי פדיתים ורבו כמו רבו׃ | 8 |
Ndidzaliza mluzu ndi kuwasonkhanitsa pamodzi. Ndithu ndawawombola; adzachulukana ngati poyamba paja.
ואזרעם בעמים ובמרחקים יזכרוני וחיו את בניהם ושבו׃ | 9 |
Ndinawamwaza pakati pa mitundu ina ya anthu, koma ku mayiko akutaliwo adzandikumbukira. Iwo pamodzi ndi ana awo adzapulumuka, ndipo adzabwerera.
והשיבותים מארץ מצרים ומאשור אקבצם ואל ארץ גלעד ולבנון אביאם ולא ימצא להם׃ | 10 |
Ndidzawabweretsa kuchokera ku Igupto ndipo ndidzawasonkhanitsa kuchokera ku Asiriya. Ndidzawabwezera ku Giliyadi ndi ku Lebanoni, mpaka malo woti nʼkukhalamo adzatheratu.
ועבר בים צרה והכה בים גלים והבישו כל מצולות יאר והורד גאון אשור ושבט מצרים יסור׃ | 11 |
Adzawoloka nyanja ya masautso; nyanja yokokoma idzagonja ndipo madzi onse a mu Nailo adzaphwa. Kudzikuza kwa Asiriya kudzatha ndipo ndodo yaufumu ya Igupto idzathyoka.
וגברתים ביהוה ובשמו יתהלכו נאם יהוה׃ | 12 |
Ndidzalimbitsa iwo mwa Yehova ndipo adzayenda mʼdzina lake,” akutero Yehova.