< שיר השירים 5 >
באתי לגני אחתי כלה אריתי מורי עם בשמי אכלתי יערי עם דבשי שתיתי ייני עם חלבי אכלו רעים שתו ושכרו דודים׃ | 1 |
Ndalowa mʼmunda mwanga, iwe mlongo wanga, iwe mkwatibwi wanga; ndasonkhanitsa mure wanga ndi zokometsera zakudya zanga. Ndadya uchi wanga pamodzi ndi zisa zake zomwe; ndamwa vinyo wanga ndi mkaka wanga. Abwenzi Idyani abwenzi anga, imwani; Inu okondana, imwani kwambiri.
אני ישנה ולבי ער קול דודי דופק פתחי לי אחתי רעיתי יונתי תמתי שראשי נמלא טל קוצותי רסיסי לילה׃ | 2 |
Ndinagona tulo koma mtima wanga unali maso. Tamverani, bwenzi langa akugogoda: “Nditsekulire, mlongo wanga, bwenzi langa, nkhunda yanga, wangwiro wanga. Mutu wanga wanyowa ndi mame, tsitsi langa lanyowa chifukwa cha nkhungu ya usiku.”
פשטתי את כתנתי איככה אלבשנה רחצתי את רגלי איככה אטנפם׃ | 3 |
Ndavula kale zovala zanga, kodi ndizivalenso? Ndasamba kale mapazi anga kodi ndiwadetsenso?
דודי שלח ידו מן החר ומעי המו עליו׃ | 4 |
Bwenzi langa anapisa dzanja lake pa chibowo cha pa chitseko; mtima wanga unagunda chifukwa cha iye.
קמתי אני לפתח לדודי וידי נטפו מור ואצבעתי מור עבר על כפות המנעול׃ | 5 |
Ndinanyamuka kukamutsekulira wachikondi wangayo, ndipo manja anga anali noninoni ndi mure, zala zanga zinali mure chuchuchu, pa zogwirira za chotsekera.
פתחתי אני לדודי ודודי חמק עבר נפשי יצאה בדברו בקשתיהו ולא מצאתיהו קראתיו ולא ענני׃ | 6 |
Ndinamutsekulira wachikondi wanga, koma nʼkuti wachikondi wangayo atachoka; iye anali atapita. Mtima wanga unafumuka chifukwa cha kuchoka kwake. Ndinamuyangʼanayangʼana koma sindinamupeze. Ndinamuyitana koma sanandiyankhe.
מצאני השמרים הסבבים בעיר הכוני פצעוני נשאו את רדידי מעלי שמרי החמות׃ | 7 |
Alonda anandipeza pamene ankayendera mzindawo. Anandimenya ndipo anandipweteka; iwo anandilanda mwinjiro wanga, alonda a pa khoma aja!
השבעתי אתכם בנות ירושלם אם תמצאו את דודי מה תגידו לו שחולת אהבה אני׃ | 8 |
Inu akazi a ku Yerusalemu ndithu ndikukupemphani, mukapeza wokondedwa wangayo, kodi mudzamuwuza chiyani? Muwuzeni kuti ine ndadwala nacho chikondi.
מה דודך מדוד היפה בנשים מה דודך מדוד שככה השבעתנו׃ | 9 |
Iwe wokongola kuposa akazi onsewa, kodi wokondedwa wakoyo ndi wopambana wina aliyense bwanji? Kodi wokondedwa wakoyo ndi wopambana ena onse chotani kuti uzichita kutipempha motere?
דודי צח ואדום דגול מרבבה׃ | 10 |
Wokondedwa wangayo ndi wowala kwambiri ndi wathanzi pakati pa anthu 1,000.
ראשו כתם פז קוצותיו תלתלים שחרות כעורב׃ | 11 |
Mutu wake ndi golide woyengeka bwino; tsitsi lake ndi lopotanapotana, ndiponso lakuda bwino ngati khwangwala.
עיניו כיונים על אפיקי מים רחצות בחלב ישבות על מלאת׃ | 12 |
Maso ake ali ngati nkhunda mʼmbali mwa mitsinje ya madzi, ngati nkhunda zitasamba mu mkaka, zitayima ngati miyala yamtengowapatali.
לחיו כערוגת הבשם מגדלות מרקחים שפתותיו שושנים נטפות מור עבר׃ | 13 |
Masaya ake ali ngati timinda ta mbewu zokometsera zakudya zopatsa fungo lokoma. Milomo yake ili ngati maluwa okongola amene akuchucha mure.
ידיו גלילי זהב ממלאים בתרשיש מעיו עשת שן מעלפת ספירים׃ | 14 |
Manja ake ali ngati ndodo zagolide zokongoletsedwa ndi miyala yamtengowapatali. Thupi lake ndi losalala ngati mnyanga wanjovu woyikamo miyala ya safiro.
שוקיו עמודי שש מיסדים על אדני פז מראהו כלבנון בחור כארזים׃ | 15 |
Miyendo yake ili ngati mizati yamwala, yokhazikika pa maziko a golide. Maonekedwe ake ali ngati Lebanoni, abwino kwambiri ngati mkungudza.
חכו ממתקים וכלו מחמדים זה דודי וזה רעי בנות ירושלם׃ | 16 |
Milomo yake ndi yosangalatsa kwambiri; munthuyo ndi wokongola kwambiri! Uyu ndiye wachikondi wanga ndi bwenzi langa, inu akazi a ku Yerusalemu.