< שיר השירים 4 >
הנך יפה רעיתי הנך יפה עיניך יונים מבעד לצמתך שערך כעדר העזים שגלשו מהר גלעד׃ | 1 |
Ndiwe wokongoladi wokondedwa wanga! Ndithudi, ndiwe wokongola! Maso ako ali ngati nkhunda kumbuyo kwa nsalu yophimba kumutu. Tsitsi lako lili ngati gulu la mbuzi zikutsetsereka kuchokera ku Giliyadi.
שניך כעדר הקצובות שעלו מן הרחצה שכלם מתאימות ושכלה אין בהם׃ | 2 |
Mano ako ali ngati gulu la nkhosa zomwe zangometedwa kumene, zochokera kozisambitsa kumene. Iliyonse ili ndi ana amapasa; palibe imene ili yokha.
כחוט השני שפתתיך ומדבריך נאוה כפלח הרמון רקתך מבעד לצמתך׃ | 3 |
Milomo yako ili ngati mbota yofiira; pakamwa pako ndi pokongola kwambiri. Kukhalira kumbuyo kwa nsalu yako yophimba kumutuyo, masaya ako akuoneka ngati mabandu a makangadza.
כמגדל דויד צוארך בנוי לתלפיות אלף המגן תלוי עליו כל שלטי הגבורים׃ | 4 |
Khosi lako lili ngati nsanja ya Davide, yomangidwa bwino ndi yosalala; pa nsanja imeneyo pali zishango 1,000, zishango zonsezo za anthu ankhondo.
שני שדיך כשני עפרים תאומי צביה הרועים בשושנים׃ | 5 |
Mawere ako ali ngati tiana tiwiri ta nswala, ngati ana amapasa a nswala amene akudya pakati pa maluwa okongola.
עד שיפוח היום ונסו הצללים אלך לי אל הר המור ואל גבעת הלבונה׃ | 6 |
Kamphepo kamadzulo kakayamba kuwuzira ndipo mithunzi ikayamba kuthawa, ndidzapita ku phiri la mure ndi ku chitunda cha lubani.
כלך יפה רעיתי ומום אין בך׃ | 7 |
Ndiwe wokongola kwambiri wokondedwa wanga; palibe chilema pa iwe.
אתי מלבנון כלה אתי מלבנון תבואי תשורי מראש אמנה מראש שניר וחרמון ממענות אריות מהררי נמרים׃ | 8 |
Tiye tichoke ku Lebanoni iwe mkwatibwi wanga, tiye tichoke ku Lebanoni, utsikepo pa msonga ya Amana, kuchoka pa msonga ya phiri la Seniri, pamwamba penipeni pa Herimoni, kuchoka ku mapanga a mikango ndiponso kumapiri kumene akambuku amavutitsa.
לבבתני אחתי כלה לבבתיני באחד מעיניך באחד ענק מצורניך׃ | 9 |
Iwe mlongo wanga, mkwatibwi wanga, wanditenga mtima, iwe wanditenga mtima ndi kapenyedwe ka maso ako, ndiponso ndi umodzi mwa mikanda ya mʼkhosi mwako.
מה יפו דדיך אחתי כלה מה טבו דדיך מיין וריח שמניך מכל בשמים׃ | 10 |
Iwe mlongo wanga, mkwatibwi wanga, chikondi chako nʼchosangalatsa! Chikondi chako nʼchosangalatsa kwambiri kupambana vinyo, ndiponso fungo la mafuta ako ndi lopambana zonunkhiritsa zonse!
נפת תטפנה שפתותיך כלה דבש וחלב תחת לשונך וריח שלמתיך כריח לבנון׃ | 11 |
Iwe mkwatibwi wanga, milomo yako ikuchucha uchi ngati chisa cha njuchi; pansi pa lilime lako pali mkaka ndi uchi. Fungo lonunkhira la zovala zako likumveka ngati fungo la ku Lebanoni.
גן נעול אחתי כלה גל נעול מעין חתום׃ | 12 |
Iwe mlongo wanga, mkwatibwi wanga, ndiwe munda wopiringidzidwa; ndiwe kasupe wotchingidwa, chitsime chotetezedwa.
שלחיך פרדס רמונים עם פרי מגדים כפרים עם נרדים׃ | 13 |
Zomera zako ndi munda wa zipatso za makangadza; muli zipatso zokoma kwambiri, muli hena ndi nadi,
נרד וכרכם קנה וקנמון עם כל עצי לבונה מר ואהלות עם כל ראשי בשמים׃ | 14 |
nadi ndi safiro, kalamusi ndi sinamoni, komanso mtengo uliwonse wonunkhira bwino. Mulinso mure ndi aloe ndi zonunkhiritsa zonse zabwino kwambiri.
מעין גנים באר מים חיים ונזלים מן לבנון׃ | 15 |
Iwe ndiwe kasupe wa mʼmunda, chitsime cha madzi oyenda, mtsinje wa madzi ochokera ku Lebanoni.
עורי צפון ובואי תימן הפיחי גני יזלו בשמיו יבא דודי לגנו ויאכל פרי מגדיו׃ | 16 |
Dzuka, iwe mphepo yakumpoto, ndipo bwera, iwe mphepo yakummwera! Uzira pa munda wanga, kuti fungo lake lonunkhira lifalikire ponseponse. Bwenzi langa alowe mʼmunda mwake ndi kudya zipatso zake zabwino kwambiri.