< רות 2 >
ולנעמי מידע לאישה איש גבור חיל ממשפחת אלימלך ושמו בעז׃ | 1 |
Naomi anali ndi mʼbale wake wolemera kwambiri wochokera ku banja la mwamuna wake Elimeleki, dzina lake Bowazi.
ותאמר רות המואביה אל נעמי אלכה נא השדה ואלקטה בשבלים אחר אשר אמצא חן בעיניו ותאמר לה לכי בתי׃ | 2 |
Tsiku lina Rute, Mmowabu uja anati kwa Naomi, “Mundilole kuti ndikakunkhe barele ku munda wa munthu aliyense amene akandikomere mtima.” Naomi anati kwa iye, “Pita mwana wanga.”
ותלך ותבוא ותלקט בשדה אחרי הקצרים ויקר מקרה חלקת השדה לבעז אשר ממשפחת אלימלך׃ | 3 |
Choncho Rute ananyamuka kupita kukakunkha ku minda yokololedwa kale. Tsono zinangochitika kuti Rute anafika mʼmunda wa Bowazi, yemwe anali wochokera ku banja la Elimeleki.
והנה בעז בא מבית לחם ויאמר לקוצרים יהוה עמכם ויאמרו לו יברכך יהוה׃ | 4 |
Posakhalitsa Bowazi anafika kuchokera ku Betelehemu ndipo analonjera okolola aja kuti, “Yehova akhale nanu!” Iwo anayankha kuti, “Yehova akudalitseni.”
ויאמר בעז לנערו הנצב על הקוצרים למי הנערה הזאת׃ | 5 |
Bowazi anafunsa kapitawo wake amene ankayangʼanira okolola aja kuti, “Mayi uyo ndi ndani?”
ויען הנער הנצב על הקוצרים ויאמר נערה מואביה היא השבה עם נעמי משדה מואב׃ | 6 |
Kapitawo uja anayankha kuti, “Mayiyu ndi Mmowabu amene anabwera ndi Naomi kuchokera ku dziko la Mowabu.
ותאמר אלקטה נא ואספתי בעמרים אחרי הקוצרים ותבוא ותעמוד מאז הבקר ועד עתה זה שבתה הבית מעט׃ | 7 |
Iye anandipempha kuti, ‘Chonde mundilole kuti ndikunkhe barele mʼminda moti akololamo kale.’ Iye wakhala akukunkha kuyambira mmawa mpaka tsopano lino osapuma nʼpangʼono pomwe.”
ויאמר בעז אל רות הלוא שמעת בתי אל תלכי ללקט בשדה אחר וגם לא תעבורי מזה וכה תדבקין עם נערתי׃ | 8 |
Choncho Bowazi anati kwa Rute, “Tamvera mwana wanga, usapite kukakunkha mʼmunda wina, ndipo usachoke mʼmunda uno. Koma uzitsata adzakazi angawa.
עיניך בשדה אשר יקצרון והלכת אחריהן הלוא צויתי את הנערים לבלתי נגעך וצמת והלכת אל הכלים ושתית מאשר ישאבון הנערים׃ | 9 |
Uziyangʼana munda akukolola anyamatawo akamakolola mʼmundamu, ndipo iwe uzitsata pambuyo pawo. Ndawawuza anyamatawo kuti asakuvutitse. Ndipo ukamva ludzu, uzipita ku mitsuko ndi kukamwa madzi amene anyamatawa atunga.”
ותפל על פניה ותשתחו ארצה ותאמר אליו מדוע מצאתי חן בעיניך להכירני ואנכי נכריה׃ | 10 |
Atamva zimenezi Rute anawerama nazolikitsa nkhope yake pansi. Kenaka anafunsa kuti, “Mwandikomera mtima chotere mlendo ngati ine chifukwa chiyani?”
ויען בעז ויאמר לה הגד הגד לי כל אשר עשית את חמותך אחרי מות אישך ותעזבי אביך ואמך וארץ מולדתך ותלכי אל עם אשר לא ידעת תמול שלשום׃ | 11 |
Bowazi anayankha kuti, “Ine ndawuzidwa zonse zimene wakhala ukuchitira apongozi ako chimwalirire mwamuna wako. Ndamvanso kuti unasiya abambo ndi amayi ako komanso dziko la kwanu ndi kubwera kudzakhala ndi anthu amene sumawadziwa ndi kale lonse.
ישלם יהוה פעלך ותהי משכרתך שלמה מעם יהוה אלהי ישראל אשר באת לחסות תחת כנפיו׃ | 12 |
Yehova akubwezere pa zimene wachitazi. Yehova Mulungu wa Israeli, amene wabwera pansi pa mapiko ake kuti akuteteze, akupatse mphotho yayikulu.”
ותאמר אמצא חן בעיניך אדני כי נחמתני וכי דברת על לב שפחתך ואנכי לא אהיה כאחת שפחתיך׃ | 13 |
Rute anati, “Mwandikomera mtima, mbuye wanga. Ndipo mwandisangalatsa ndi kundiyankhula mwa chifundo ngakhale sindili mmodzi mwa adzakazi anu.”
ויאמר לה בעז לעת האכל גשי הלם ואכלת מן הלחם וטבלת פתך בחמץ ותשב מצד הקוצרים ויצבט לה קלי ותאכל ותשבע ותתר׃ | 14 |
Nthawi ya chakudya cha masana Bowazi anati kwa iye, “Bwera kuno, utenge buledi ndi kusunsa nthongo mu vinyo.” Choncho anakhala pansi pafupi ndi okololawo, ndipo Bowazi anamupatsa chakudya ndi nyama yowotcha. Anadya chilichonse amafuna ndipo chakudya china chinatsalako.
ותקם ללקט ויצו בעז את נעריו לאמר גם בין העמרים תלקט ולא תכלימוה׃ | 15 |
Atanyamuka kuti azikakunkha, Bowazi analangiza anyamata ake kuti, “Ngakhale mayiyu azikunkha pakati pa mitolo musamuletse ndi kumuchititsa manyazi.
וגם של תשלו לה מן הצבתים ועזבתם ולקטה ולא תגערו בה׃ | 16 |
Koma muzimusololerako ngala zina za mʼmitolo ndi kumusiyira kuti azikunkha ndipo musamukalipire.”
ותלקט בשדה עד הערב ותחבט את אשר לקטה ויהי כאיפה שערים׃ | 17 |
Choncho Rute anakunkha mʼmundamo mpaka madzulo. Kenaka anapuntha barele anakunkhayo, ndipo anakwanira pafupifupi makilogalamu khumi.
ותשא ותבוא העיר ותרא חמותה את אשר לקטה ותוצא ותתן לה את אשר הותרה משבעה׃ | 18 |
Anasenza barele uja kupita naye ku mudzi, nakaonetsa apongozi ake. Kenaka anatulutsa chakudya chimene chinatsalira atakhuta chija ndi kupatsa apongozi ake.
ותאמר לה חמותה איפה לקטת היום ואנה עשית יהי מכירך ברוך ותגד לחמותה את אשר עשתה עמו ותאמר שם האיש אשר עשיתי עמו היום בעז׃ | 19 |
Apongozi akewo anamufunsa kuti, “Kodi lero unakakunkha kuti? Unakagwira kuti ntchitoyi? Adalitsike munthu amene anakukomera mtimayo.” Ndipo Rute anawuza mpongozi wake za munthu amene ku malo ake anakagwirako ntchito. Iye anati, “Munthuyo dzina lake ndi Bowazi.”
ותאמר נעמי לכלתה ברוך הוא ליהוה אשר לא עזב חסדו את החיים ואת המתים ותאמר לה נעמי קרוב לנו האיש מגאלנו הוא׃ | 20 |
Naomi anati kwa mpongozi wakeyo, “Munthu ameneyu amudalitse Yehova, amene sanasiye kuchitira chifundo anthu amoyo ndi akufa omwe. Anatinso munthu ameneyu ndi mnansi wapaphata. Ndiye ali ndi udindo wotisamalira.”
ותאמר רות המואביה גם כי אמר אלי עם הנערים אשר לי תדבקין עד אם כלו את כל הקציר אשר לי׃ | 21 |
Choncho Rute Mmowabuyo anati, “Iye anandiwuzanso kuti, ‘Uzitsata antchito angawa mpaka atamaliza kukolola munda wonse.’”
ותאמר נעמי אל רות כלתה טוב בתי כי תצאי עם נערותיו ולא יפגעו בך בשדה אחר׃ | 22 |
Naomi anati kwa Rute mpongozi wake, “Kuli bwino mwana wanga kuti uzipita ndi adzakazi ake kuopa kuti mʼmunda wa munthu wina angakuvute.”
ותדבק בנערות בעז ללקט עד כלות קציר השערים וקציר החטים ותשב את חמותה׃ | 23 |
Choncho Rute ankatsatira adzakazi a Bowazi namakunkha mpaka anthu atamaliza kudula barele ndi tirigu. Ndipo amakhalabe ndi mpongozi wakeyo.