< תהילים 89 >

משכיל לאיתן האזרחי חסדי יהוה עולם אשירה לדר ודר אודיע אמונתך בפי׃ 1
Ndakatulo ya Etani, wa banja la Ezara. Ndidzayimba za chikondi chachikulu cha Yehova kwamuyaya; ndi pakamwa panga ndidzachititsa kuti kukhulupirika kwanu kudziwike ku mibado yonse.
כי אמרתי עולם חסד יבנה שמים תכן אמונתך בהם׃ 2
Ndidzalalikira kuti chikondi chanu chidzakhazikika mpaka muyaya, kuti Inu munakhazikitsa kukhulupirika kwanu kumwamba kwenikweniko.
כרתי ברית לבחירי נשבעתי לדוד עבדי׃ 3
Inu munati, “Ndachita pangano ndi wosankhidwa wanga, ndalumbira kwa Davide mtumiki wanga kuti,
עד עולם אכין זרעך ובניתי לדר ודור כסאך סלה׃ 4
‘Ndidzakhazikitsa zidzukulu zako mpaka muyaya. Ndidzachititsa kuti mpando wako waufumu ukhazikike ku mibado yonse,’” (Sela)
ויודו שמים פלאך יהוה אף אמונתך בקהל קדשים׃ 5
Mayiko akumwamba amatamanda zozizwitsa zanu Yehova, kukhulupirika kwanunso, mu msonkhano wa oyera mtima anu.
כי מי בשחק יערך ליהוה ידמה ליהוה בבני אלים׃ 6
Pakuti ndani mu mlengalenga angalingane ndi Yehova? Ndani wofanana ndi Yehova pakati pa zolengedwa zakumwamba?
אל נערץ בסוד קדשים רבה ונורא על כל סביביו׃ 7
Mu msonkhano wa oyera mtima Mulungu amaopedwa kwambiri; Iye ndiye wochititsa mantha kupambana onse amene amuzungulira.
יהוה אלהי צבאות מי כמוך חסין יה ואמונתך סביבותיך׃ 8
Inu Yehova Mulungu Wamphamvuzonse, ndani wofanana nanu? Yehova ndinu wamphamvu ndipo kukhulupirika kwanu kwakuzungulirani.
אתה מושל בגאות הים בשוא גליו אתה תשבחם׃ 9
Mumalamula nyanja ya mafunde awukali; pamene mafunde ake awundana Inu mumawakhalitsa bata.
אתה דכאת כחלל רהב בזרוע עזך פזרת אויביך׃ 10
Munaphwanya Rahabe monga munthu wophedwa; ndi dzanja lanu lamphamvu munabalalitsa adani anu.
לך שמים אף לך ארץ תבל ומלאה אתה יסדתם׃ 11
Mayiko akumwamba ndi anu ndiponso dziko lapansi ndi lanu; munapanga dziko lonse ndi zonse zili mʼmenemo.
צפון וימין אתה בראתם תבור וחרמון בשמך ירננו׃ 12
Munalenga Kumpoto ndi Kummwera; Tabori ndi Herimoni akuyimba ndi chimwemwe pa dzina lanu.
לך זרוע עם גבורה תעז ידך תרום ימינך׃ 13
Mkono wanu ndi wamphamvu; dzanja lanu ndi lamphamvu, dzanja lanu lamanja ndi lopambana.
צדק ומשפט מכון כסאך חסד ואמת יקדמו פניך׃ 14
Chilungamo ndi chiweruzo cholungama ndiye maziko a mpando wanu waufumu; chikondi ndi kukhulupirika zimayenda patsogolo panu.
אשרי העם יודעי תרועה יהוה באור פניך יהלכון׃ 15
Ndi odala amene aphunzira kuyamika Inu, amene amayenda mʼkuwunika kwa nkhope yanu Yehova.
בשמך יגילון כל היום ובצדקתך ירומו׃ 16
Amakondwera mʼdzina lanu tsiku lonse lathunthu; amasangalala koposa mʼchilungamo chanu.
כי תפארת עזמו אתה וברצנך תרים קרננו׃ 17
Pakuti Inu ndiye ulemerero wawo ndi mphamvu yawo ndipo mwa kukoma mtima kwanu Inu mumakweza nyanga yathu.
כי ליהוה מגננו ולקדוש ישראל מלכנו׃ 18
Ndithudi, chishango chathu ndi cha Yehova, Mfumu yathu kwa Woyerayo wa Israeli.
אז דברת בחזון לחסידיך ותאמר שויתי עזר על גבור הרימותי בחור מעם׃ 19
Kale munayankhula mʼmasomphenya, kwa anthu anu okhulupirika munati, “Ndapatsa mphamvu wankhondo; ndakweza mnyamata wochokera pakati pa anthu.
מצאתי דוד עבדי בשמן קדשי משחתיו׃ 20
Ndamupeza mtumiki wanga Davide; ndamudzoza ndi mafuta opatulika.
אשר ידי תכון עמו אף זרועי תאמצנו׃ 21
Dzanja langa lidzamuchirikiza; zoonadi, mkono wanga udzamupatsa mphamvu.
לא ישא אויב בו ובן עולה לא יעננו׃ 22
Adani sadzamulamula kuti apereke msonkho; anthu oyipa sadzamusautsa.
וכתותי מפניו צריו ומשנאיו אגוף׃ 23
Ndidzaphwanya adani ake pamaso pake ndi kukantha otsutsana naye.
ואמונתי וחסדי עמו ובשמי תרום קרנו׃ 24
Chikondi changa chokhulupirika chidzakhala naye, ndipo kudzera mʼdzina langa nyanga yake idzakwezedwa.
ושמתי בים ידו ובנהרות ימינו׃ 25
Ndidzayika dzanja lake pa nyanja, dzanja lake lamanja pa mitsinje.
הוא יקראני אבי אתה אלי וצור ישועתי׃ 26
Iyeyo adzafuwula kwa Ine kuti, ‘Ndinu Atate anga, Mulungu wanga, Thanthwe ndi Chipulumutso changa.’
אף אני בכור אתנהו עליון למלכי ארץ׃ 27
Ndidzamuyika kuti akhale mwana wanga woyamba kubadwa; wokwezedwa kwambiri pakati pa mafumu a dziko lapansi.
לעולם אשמור לו חסדי ובריתי נאמנת לו׃ 28
Ndidzamusungira chifundo changa kwamuyaya, ndipo pangano langa ndi iye silidzatha.
ושמתי לעד זרעו וכסאו כימי שמים׃ 29
Ine ndidzakhazikitsa zidzukulu zake mpaka muyaya, mpando wake waufumu ngati masiku a miyamba.
אם יעזבו בניו תורתי ובמשפטי לא ילכון׃ 30
“Ngati ana ake adzataya lamulo langa ndi kusatsatira malangizo anga,
אם חקתי יחללו ומצותי לא ישמרו׃ 31
ngati adzaswa malamulo anga ndi kulephera kusunga ziphunzitso zanga,
ופקדתי בשבט פשעם ובנגעים עונם׃ 32
Ine ndidzalanga tchimo lawo ndi ndodo, mphulupulu zawo powakwapula.
וחסדי לא אפיר מעמו ולא אשקר באמונתי׃ 33
Koma sindidzachotsa chikondi changa pa iye, kapena kukhala wosakhulupirika kwa iyeyo.
לא אחלל בריתי ומוצא שפתי לא אשנה׃ 34
Sindidzaswa pangano langa kapena kusintha zimene milomo yanga yayankhula.
אחת נשבעתי בקדשי אם לדוד אכזב׃ 35
Ndinalumbira kamodzi mwa kuyera kwanga ndipo sindidzanama kwa Davide,
זרעו לעולם יהיה וכסאו כשמש נגדי׃ 36
kuti zidzukulu zake zidzakhale kwamuyaya ndipo mpando wake waufumu udzakhazikika pamaso panga ngati dzuwa;
כירח יכון עולם ועד בשחק נאמן סלה׃ 37
udzakhazikika kwamuyaya monga mwezi, mboni yokhulupirika mʼmitambo. (Sela)
ואתה זנחת ותמאס התעברת עם משיחך׃ 38
“Koma tsopano Inu mwamukana, mwamutaya, mwamukwiyira kwambiri wodzozedwa wanu.
נארתה ברית עבדך חללת לארץ נזרו׃ 39
Mwakana pangano ndi mtumiki wanu ndipo mwadetsa mʼfumbi chipewa chake chaufumu.
פרצת כל גדרתיו שמת מבצריו מחתה׃ 40
Inu mwagumula makoma ake onse ndipo mwasandutsa bwinja malinga ake.
שסהו כל עברי דרך היה חרפה לשכניו׃ 41
Onse amene amadutsa amalanda zinthu zake; iye wakhala chotonzedwa cha anansi ake.
הרימות ימין צריו השמחת כל אויביו׃ 42
Mwakweza dzanja lamanja la adani ake; mwachititsa kuti adani ake akondwere.
אף תשיב צור חרבו ולא הקימתו במלחמה׃ 43
Mwabunthitsa lupanga lake, simunamuthandize pa nkhondo.
השבת מטהרו וכסאו לארץ מגרתה׃ 44
Inu mwathetsa kukongola kwa ulemerero wake ndipo mwagwetsa pansi mpando wake waufumu.
הקצרת ימי עלומיו העטית עליו בושה סלה׃ 45
Mwachepetsa masiku a unyamata wake; mwamuphimba ndi chofunda chochititsa manyazi. (Sela)
עד מה יהוה תסתר לנצח תבער כמו אש חמתך׃ 46
“Mpaka liti Yehova? Kodi mudzadzibisa mpaka kalekale? Mpaka liti ukali wanu udzayaka ngati moto?
זכר אני מה חלד על מה שוא בראת כל בני אדם׃ 47
Kumbukirani kuti masiku a moyo wanga ndi ochepa pakuti munalenga kwachabe anthu onse!
מי גבר יחיה ולא יראה מות ימלט נפשו מיד שאול סלה׃ (Sheol h7585) 48
Kodi ndi munthu uti angakhale ndi moyo ndi kusaona imfa? Kapena kudzipulumutsa yekha ku mphamvu ya manda? (Sela) (Sheol h7585)
איה חסדיך הראשנים אדני נשבעת לדוד באמונתך׃ 49
Inu Ambuye kodi chili kuti chikondi chanu chachikulu choyamba chija, chimene mwa kukhulupirika kwanu munalumbira kwa Davide?
זכר אדני חרפת עבדיך שאתי בחיקי כל רבים עמים׃ 50
Kumbukirani, Ambuye momwe mtumiki wanu wanyozedwera, momwe ndakhalira ndi kusunga mu mtima mwanga mawu a pangano a anthu a mitundu yonse,
אשר חרפו אויביך יהוה אשר חרפו עקבות משיחך׃ 51
mawu achipongwe amene adani anu akhala akunyoza, Inu Yehova, ndi mawu amene akhala akunyoza mayendedwe onse a wodzozedwa wanu.
ברוך יהוה לעולם אמן ואמן׃ 52
“Matamando akhale kwa Yehova mpaka muyaya!”

< תהילים 89 >