< תהילים 85 >

למנצח לבני קרח מזמור רצית יהוה ארצך שבת שבות יעקב׃ 1
Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la ana a Kora. Yehova munakomera mtima dziko lanu; munabwezeretsa ulemerero wa Yakobo.
נשאת עון עמך כסית כל חטאתם סלה׃ 2
Munakhululukira mphulupulu za anthu anu ndi kuphimba machimo awo onse. (Sela)
אספת כל עברתך השיבות מחרון אפך׃ 3
Munayika pambali ukali wanu wonse ndi kutembenuka kuchoka ku mkwiyo wanu woopsa.
שובנו אלהי ישענו והפר כעסך עמנו׃ 4
Tibwezeretseninso mwakale Inu Mulungu Mpulumutsi wathu, ndipo mutichotsere mkwiyo wanu.
הלעולם תאנף בנו תמשך אפך לדר ודר׃ 5
Kodi mudzatikwiyira mpaka liti? Kodi mudzapitiriza kukwiya pa mibado yathu yonse?
הלא אתה תשוב תחינו ועמך ישמחו בך׃ 6
Kodi simudzatitsitsimutsanso, kuti anthu anu asangalale mwa Inu?
הראנו יהוה חסדך וישעך תתן לנו׃ 7
Tionetseni chikondi chanu chosatha, Inu Yehova, ndipo tipatseni chipulumutso chanu.
אשמעה מה ידבר האל יהוה כי ידבר שלום אל עמו ואל חסידיו ואל ישובו לכסלה׃ 8
Ndidzamvetsera zimene Yehova Mulungu adzanena; Iye amalonjeza mtendere kwa anthu ake, oyera mtima ake, koma musawalole kuti abwerere ku zopusa.
אך קרוב ליראיו ישעו לשכן כבוד בארצנו׃ 9
Ndithu chipulumutso chake chili pafupi ndi iwo amene amaopa Iye, kuti ulemerero wake ukhale mʼdziko lathu.
חסד ואמת נפגשו צדק ושלום נשקו׃ 10
Chikondi ndi kukhulupirika zimakumana pamodzi; chilungamo ndi mtendere zimapsompsonana.
אמת מארץ תצמח וצדק משמים נשקף׃ 11
Kukhulupirika kumatumphuka kuchokera ku dziko lapansi, ndipo chilungamo chimayangʼana pansi kuchokera kumwamba.
גם יהוה יתן הטוב וארצנו תתן יבולה׃ 12
Ndithu Yehova adzapereka chimene chili chabwino, ndipo dziko lathu lidzapereka zokolola zake.
צדק לפניו יהלך וישם לדרך פעמיו׃ 13
Wolungama amapita patsogolo pake ndi kukonza njira za mapazi ake.

< תהילים 85 >