< תהילים 83 >
שיר מזמור לאסף אלהים אל דמי לך אל תחרש ואל תשקט אל׃ | 1 |
Nyimbo. Salimo la Asafu. Inu Mulungu musakhale chete; musangoti phee, Mulungu musangoti duu.
כי הנה אויביך יהמיון ומשנאיך נשאו ראש׃ | 2 |
Onani adani anu akuchita chiwawa, amene amadana nanu autsa mitu yawo.
על עמך יערימו סוד ויתיעצו על צפוניך׃ | 3 |
Mochenjera iwo akukambirana za chiwembu kutsutsana ndi anthu anu; Iwo akukonzekera kutsutsana ndi omwe mumawakonda.
אמרו לכו ונכחידם מגוי ולא יזכר שם ישראל עוד׃ | 4 |
Iwo akunena kuti, “Bwerani” akutero, “Tiyeni tiwononge mtundu wonsewu kuti dzina la Israeli lisakumbukikenso.”
כי נועצו לב יחדו עליך ברית יכרתו׃ | 5 |
Ndi mtima umodzi akukonzekera chiwembu; Iwo achita mgwirizano kutsutsana nanu:
אהלי אדום וישמעאלים מואב והגרים׃ | 6 |
Matenti a Edomu ndi Aismaeli, Mowabu ndi Ahagiri,
גבל ועמון ועמלק פלשת עם ישבי צור׃ | 7 |
Agebala, Aamoni ndi Aamaleki, Afilisti, pamodzi ndi anthu a ku Turo.
גם אשור נלוה עמם היו זרוע לבני לוט סלה׃ | 8 |
Ngakhalenso Aasiriya aphatikizana nawo kupereka mphamvu kwa ana a Loti. (Sela)
עשה להם כמדין כסיסרא כיבין בנחל קישון׃ | 9 |
Muwachitire zomwe munachitira Amidiyani, monga munachitira Sisera ndi Yabini ku mtsinje wa Kisoni.
נשמדו בעין דאר היו דמן לאדמה׃ | 10 |
Amene anawonongedwa ku Endori ndi kukhala ngati zinyalala.
שיתמו נדיבמו כערב וכזאב וכזבח וכצלמנע כל נסיכמו׃ | 11 |
Anthu awo otchuka muwachite zomwe munachita Orebu ndi Zeebu ana a mafumu muwachite zomwe munachita Zeba ndi Zalimuna,
אשר אמרו נירשה לנו את נאות אלהים׃ | 12 |
amene anati, “Tiyeni tilande dziko la msipu la Mulungu.”
אלהי שיתמו כגלגל כקש לפני רוח׃ | 13 |
Muwasandutse fumbi lowuluka, Inu Mulungu wanga, ngati mankhusu owuluka ndi mphepo.
כאש תבער יער וכלהבה תלהט הרים׃ | 14 |
Monga moto umatentha nkhalango, kapena malawi a moto kuyatsa phiri,
כן תרדפם בסערך ובסופתך תבהלם׃ | 15 |
kotero muwathamangitse ndi mphepo yamkuntho, ndi kuwachititsa mantha ndi namondwe.
מלא פניהם קלון ויבקשו שמך יהוה׃ | 16 |
Muphimbe nkhope zawo ndi manyazi kuti adzafunefune dzina lanu Yehova.
יבשו ויבהלו עדי עד ויחפרו ויאבדו׃ | 17 |
Achite manyazi ndi mantha nthawi zonse; awonongeke mwa manyazi.
וידעו כי אתה שמך יהוה לבדך עליון על כל הארץ׃ | 18 |
Adziwe kuti Inu amene dzina lanu ndi Yehova, ndinu nokha Wammwambamwamba pa dziko lonse lapansi.