< תהילים 81 >

למנצח על הגתית לאסף הרנינו לאלהים עוזנו הריעו לאלהי יעקב׃ 1
Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Potsata mayimbidwe a gititi. Salimo la Asafu. Imbani mwachimwemwe kwa Mulungu mphamvu yathu; Fuwulani mokweza kwa Mulungu wa Yakobo!
שאו זמרה ותנו תף כנור נעים עם נבל׃ 2
Yambani nyimbo, imbani tambolini imbani pangwe wolira bwino ndi zeze.
תקעו בחדש שופר בכסה ליום חגנו׃ 3
Imbani lipenga la nyanga ya nkhosa yayimuna pa mwezi watsopano, ndi pamene mwezi waoneka wonse, pa tsiku la phwando;
כי חק לישראל הוא משפט לאלהי יעקב׃ 4
ili ndi lamulo kwa Israeli, langizo la Mulungu wa Yakobo.
עדות ביהוסף שמו בצאתו על ארץ מצרים שפת לא ידעתי אשמע׃ 5
Iye anapereka lamulolo kwa zidzukulu za Yosefe pamene anatuluka kulimbana ndi Igupto, kumene tinamva chiyankhulo chimene sitinachidziwe.
הסירותי מסבל שכמו כפיו מדוד תעברנה׃ 6
Iye akunena kuti, “Ine ndinachotsa zolemetsa pa mapewa awo; Manja awo anamasulidwa mʼdengu.
בצרה קראת ואחלצך אענך בסתר רעם אבחנך על מי מריבה סלה׃ 7
Pa mavuto anu munayitana ndipo ndinakulanditsani, ndinakuyankhani kuchokera mʼmitambo ya mabingu; ndinakuyesani pa madzi a ku Meriba. (Sela)
שמע עמי ואעידה בך ישראל אם תשמע לי׃ 8
“Imvani anthu anga, ndipo ndidzakuchenjezani ngati mungathe kumvetsera, Inu Israeli!
לא יהיה בך אל זר ולא תשתחוה לאל נכר׃ 9
Musadzakhale ndi mulungu wachilendo pakati panu; musadzagwadire mulungu wina.
אנכי יהוה אלהיך המעלך מארץ מצרים הרחב פיך ואמלאהו׃ 10
Ine ndine Yehova Mulungu wanu, amene ndinakutulutsani mʼdziko la Igupto. Yasamani kukamwa kwanu ndipo ndidzakudyetsani.
ולא שמע עמי לקולי וישראל לא אבה לי׃ 11
“Koma anthu anga sanandimvere; Israeli sanandigonjere.
ואשלחהו בשרירות לבם ילכו במועצותיהם׃ 12
Kotero ndinawasiya ndi mitima yawo yosamverayo kuti atsate zimene ankafuna.
לו עמי שמע לי ישראל בדרכי יהלכו׃ 13
“Anthu anga akanangondimvera, Israeli akanatsatira njira zanga,
כמעט אויביהם אכניע ועל צריהם אשיב ידי׃ 14
nʼkanafulumira motani kuti ndigonjetse adani awo ndi kutembenuza mkono wanga kulimbana ndi amaliwongo!
משנאי יהוה יכחשו לו ויהי עתם לעולם׃ 15
Iwo amene amadana ndi Yehova akanakhwinyata pamaso pake, ndipo chilango chawo chinakakhala mpaka kalekale.
ויאכילהו מחלב חטה ומצור דבש אשביעך׃ 16
Koma inu mukanadyetsedwa tirigu wabwino kwambiri; ndikanakukhutitsani ndi uchi wochokera pa thanthwe.”

< תהילים 81 >