< תהילים 80 >
למנצח אל ששנים עדות לאסף מזמור רעה ישראל האזינה נהג כצאן יוסף ישב הכרובים הופיעה׃ | 1 |
Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Potsata mayimbidwe a “Kakombo wa Pangano.” Salimo la Asafu. Tcherani khutu Inu mʼbusa wa Israeli, Inu amene mumatsogolera Yosefe monga nkhosa; Inu amene mumakhala pa mpando waufumu pakati pa akerubi, walani
לפני אפרים ובנימן ומנשה עוררה את גבורתך ולכה לישעתה לנו׃ | 2 |
kwa Efereimu, Benjamini ndi Manase. Utsani mphamvu yanu; bwerani ndi kutipulumutsa.
אלהים השיבנו והאר פניך ונושעה׃ | 3 |
Tibwezereni mwakale Inu Mulungu; nkhope yanu itiwalire kuti tipulumutsidwe.
יהוה אלהים צבאות עד מתי עשנת בתפלת עמך׃ | 4 |
Inu Mulungu Wamphamvuzonse, mpaka liti mkwiyo wanu udzanyeka kutsutsana ndi mapemphero a anthu anu?
האכלתם לחם דמעה ותשקמו בדמעות שליש׃ | 5 |
Mwawadyetsa buledi wa misozi; mwachitisa iwo kumwa misozi yodzaza mbale.
תשימנו מדון לשכנינו ואיבינו ילעגו למו׃ | 6 |
Mwachititsa kuti tikhale gwero la mikangano pakati pa anansi athu, ndipo adani athu akutinyoza.
אלהים צבאות השיבנו והאר פניך ונושעה׃ | 7 |
Tibwezereni mwakale Inu Mulungu Wamphamvuzonse, nkhope yanu itiwalire kuti tipulumutsidwe.
גפן ממצרים תסיע תגרש גוים ותטעה׃ | 8 |
Munatulutsa mpesa kuchoka ku Igupto; munathamangitsa anthu a mitundu ina ndi kuwudzala mpesawo.
פנית לפניה ותשרש שרשיה ותמלא ארץ׃ | 9 |
Munawulimira munda wamphesawo, ndipo unamera ndi kudzaza dziko.
כסו הרים צלה וענפיה ארזי אל׃ | 10 |
Mapiri anaphimbidwa ndi mthunzi wake, mikungudza yamphamvu ndi nthambi zake.
תשלח קצירה עד ים ואל נהר יונקותיה׃ | 11 |
Unatambalitsa nthambi zake mpaka ku nyanja, mphukira zake mpaka ku mtsinje.
למה פרצת גדריה וארוה כל עברי דרך׃ | 12 |
Chifukwa chiyani mwagwetsa makoma ake kuti onse amene akudutsa athyole mphesa zake?
יכרסמנה חזיר מיער וזיז שדי ירענה׃ | 13 |
Nguluwe zochokera mʼnkhalango zikuwononga ndipo zirombo za mthengo zimawudya.
אלהים צבאות שוב נא הבט משמים וראה ופקד גפן זאת׃ | 14 |
Bweraninso kwa ife Inu Mulungu Wamphamvuzonse! Yangʼanani pansi muli kumwambako ndipo muone! Uyangʼanireni mpesa umenewu,
וכנה אשר נטעה ימינך ועל בן אמצתה לך׃ | 15 |
muzu umene dzanja lanu lamanja ladzala, mwana amene inu munamukuza nokha.
שרפה באש כסוחה מגערת פניך יאבדו׃ | 16 |
Mpesa wanu wadulidwa ndi kutenthedwa ndi moto; pakudzudzula kwanu anthu anu awonongeka.
תהי ידך על איש ימינך על בן אדם אמצת לך׃ | 17 |
Dzanja lanu likhale pa munthu amene ali ku dzanja lanu lamanja, mwana wa munthu amene mwalera nokha.
ולא נסוג ממך תחינו ובשמך נקרא׃ | 18 |
Ndipo ife sitidzatembenukira kumbali kuchoka kwa Inu; titsitsimutseni ndipo tidzayitana pa dzina lanu.
יהוה אלהים צבאות השיבנו האר פניך ונושעה׃ | 19 |
Tibwezereni mwakale Inu Yehova Mulungu Wamphamvuzonse nkhope yanu itiwalire kuti tipulumutsidwe.